NKHANI YOPHUNZIRA 26
Kodi Chikondi Chingatithandize Bwanji Kuti Tisamachite Mantha?
“Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.”—SAL. 118:6.
NYIMBO NA. 105 “Mulungu Ndiye Chikondi”
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi zinthu zina zomwe anthu amaopa ndi ziti?
TAGANIZIRANI zinthu izi zomwe zinachitikira a Mboni ena. Nestor ndi mkazi wake María, ankafuna kukatumikira kumene kunkafunika olalikira ambiri. * Kuti akwanitse zimenezi ankafunika kusintha zinthu zina pa moyo wawo. Koma ankaopa kuti azikhala ndi ndalama zochepa ndiponso osasangalala. Biniam yemwe amakhala m’dziko lomwe ntchito yathu ndi yoletsedwa, atakhala wa Mboni za Yehova, anazindikira kuti monga mmodzi wa anthu a Mulungu akhoza kuzunzidwa. Zimenezi zinkamuchititsa mantha. Komabe iye ankaopa kwambiri zimene achibale ake angachite akadziwa kuti walowa chipembedzo chatsopano. Valérie anapezeka ndi khansa ndipo anavutika kupeza dokotala wopanga opaleshoni, yemwe akanalemekeza zomwe iye amakhulupirira pa nkhani ya magazi. N’zomveka kuti iye ankaopa kuti akhoza kufa.
2. N’chifukwa chiyani timafunika kuyesetsa kuthetsa mantha omwe tili nawo?
2 Kodi inunso munachitapo mantha ndi zinthu ngati zimenezi? Ambirife tinaopako zoterezi. Ngati sitingaphunzire mmene tingathetsere mantha, nthawi zambiri tingamasankhe zinthu molakwika, zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Zimenezi ndi zomwe Satana amafuna. Amafuna tizichita mantha kuti tisamvere malamulo a Yehova, kuphatikizapo lamulo lakuti tizilalikira uthenga wabwino. (Chiv. 12:17) Satana ndi woipa, wankhanza komanso wamphamvu. Komabe mungathe kudziteteza kwa iye. Motani?
3. N’chiyani chingatithandize kuthetsa mantha omwe tili nawo?
3 Tikamakhulupirira kuti Yehova amatikonda ndipo ali kumbali yathu, sitingamaope Satana. (Sal. 118:6) Mwachitsanzo, amene analemba Salimo 118 anakumana ndi zinthu zina zodetsa nkhawa. Anali ndi adani ambiri ndipo ena anali a maudindo akuluakulu (vesi 9, 10). Nthawi zina ankapanikizidwa kwambiri (vesi 13). Komanso anapatsidwa uphungu wamphamvu ndi Yehova (vesi 18). Ngakhale zinali choncho, wolemba salimoyu anaimba kuti: “Sindidzaopa.” Kodi n’chiyani chinkamuchititsa kuona kuti ndi wotetezeka? Iye ankadziwa kuti ngakhale kuti Yehova anam’patsa uphungu wamphamvu, Atate wake akumwambawa ankamukonda kwambiri. Wolemba salimoyu ankakhulupirira kuti kaya akumana ndi zotani, Mulungu wake wachikondiyu anali wokonzeka kumuthandiza.—Sal. 118:29.
4. Kodi tingathetse mantha pa zinthu ngati ziti tikamakhulupirira kuti Mulungu amatikonda?
4 Tizikhulupirira kuti Yehova amatikonda ifeyo patokha. Zimenezi zidzatithandiza kuthetsa mantha pa zinthu zitatu zimene anthu ambiri amaziopa, zomwe ndi (1) kuopa kuti sakwanitsa kupezera banja lawo zinthu zofunika, (2) kuopa anthu komanso (3) kuopa imfa. Anthu omwe atchulidwa mundime yoyamba ija anakwanitsa kuthetsa mantha omwe anali nawo chifukwa ankakhulupirira kuti Mulungu amawakonda.
KUOPA KUTI SITIZITHA KUPEZERA BANJA LATHU ZOFUNIKA
5. Kodi ndi zochitika ziti zomwe zingamadetse nkhawa kwambiri mutu wa banja? (Onani chithunzi chapachikuto.)
5 Mkhristu yemwe ndi mutu wa banja saona mopepuka udindo wosamalira banja lake. (1 Tim. 5:8) Ngati ndinu mutu wa banja, n’kutheka kuti pa nthawi ya mliri waposachedwawu munkaopa kuti ntchito yanu ikhoza kukutherani. Mwina munkadera nkhawa kuti muzipeza bwanji chakudya komanso ndalama yolipirira nyumba. Mwinanso munkaopa kuti ngati ntchito itakutherani simukwanitsa kupezanso ina. Kapenanso mofanana ndi Nestor ndi María, munkazengereza kusintha zinthu zina pa nkhani ya ntchito chifukwa choopa kuti muzipeza ndalama zochepa. Satana wakwanitsa kuchititsa anthu ambiri kuti asiye kutumikira Yehova chifukwa chokhala ndi mantha ngati amenewa.
6. Kodi Satana amafuna kuti tizikhulupirira chiyani?
6 Satana amayesetsa kutichititsa kuganiza kuti Yehova satiganizira ifeyo patokha ndipo satithandiza kupezera banja lathu zofunika. Choncho tingamaone kuti tiyenera kuchita chilichonse chomwe tingathe kuti titeteze ntchito yathu, ngakhale zitakhala kuti tikuphwanya mfundo za m’Malemba.
7. Kodi Yesu amatitsimikizira chiyani?
7 Yesu yemwe amawadziwa bwino Atate kuposa aliyense amatitsimikizira kuti Mulungu ‘amadziwa zimene tikufunikira tisanapemphe n’komwe.’ (Mat. 6:8) Ndipo Yesu amadziwa kuti Yehova ndi wokonzeka kutipatsa zimene tikufunikira. Monga Akhristu tili m’banja la Mulungu. Choncho tingakhale otsimikiza kuti monga Mutu wa banja, Yehova adzachita zomwe anauza mitu ya mabanja pa 1 Timoteyo 5:8.
8. (a) N’chiyani chingatithandize kuti tisamachite mantha pa nkhani yopezera banja lathu zinthu zofunika? (Mateyu 6:31-33) (b) Kodi tikuphunzira chiyani pachithunzi cha banja lomwe likukapereka chakudya kwa mlongo wina?
8 Tikamakhulupirira kuti Yehova amatikonda komanso amakonda banja lathu, sitingakayikire kuti tidzapeza zomwe timafunikira. (Werengani Mateyu 6:31-33.) Iye amafunitsitsa kutipatsa zimene timafunikira, ndipo ndi wowolowa manja. Pamene ankalenga dzikoli, sikuti anangotipatsa zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi moyo. Mwachikondi, iye anadzaza dzikoli ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti tizisangalala kwambiri. (Gen. 2:9) Ngakhale kuti nthawi zina tingakhale ndi zinthu zofunika zokha tingachite bwino kumakumbukira kuti Yehova ndi amene watipatsa zimenezo. (Mat. 6:11) Tisamaiwale kuti zilizonse zimene tingadzimane sizingafanane ndi zimene Mulungu wathu wachikondi angatipatse panopa kapenanso m’tsogolo. Imeneyi ndi mfundo yomwe Nestor ndi María anazindikira.—Yes. 65:21, 22.
9. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Nestor ndi María?
9 Nestor ndi María omwe kwawo ndi ku Colombia ankakhala moyo wofewa. Iwo ananena kuti: “Tinaganiza zoti tiyambe kukhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti tiwonjezere utumiki wathu, koma tinkaopa kuti sitizisangalala chifukwa tizikhala ndi ndalama zochepa.” Ndiye n’chiyani chinawathandiza kuti asamaope zimenezi? Anaganizira njira zambiri zomwe Yehova anasonyezera kuti amawakonda. Chifukwa chokhulupirira kuti iye adzawasamalira anasiya ntchito zawo zomwe zinali za ndalama zambiri. Iwo anagulitsa nyumba yawo n’kusamukira kudera lina m’dziko lomwelo komwe kunkafunika olalikira ambiri. Kodi amamva bwanji chifukwa cha zomwe anasankhazi? Nestor ananena kuti: “Taona kuti mawu a pa Mateyu 6:33 ndi oona. Sitinasowepo chilichonse. Panopa timakhala moyo wosangalala kwambiri.”
KUOPA ANTHU
10. N’chifukwa chiyani n’zomveka kuti anthu amaopa anthu anzawo?
10 Kuyambira kale anthu akhala akuchitira anzawo zoipa. (Mlal. 8:9) Mwachitsanzo, anthu amagwiritsa ntchito molakwika udindo wawo, ophwanya malamulo amachita zachiwawa, ana asukulu amanyoza kapena kuopseza anzawo ndipo anthu ena amachitira nkhanza ngakhale anthu a m’banja lawo. Mpake kuti anthu amaopa anthu anzawo. Ndiye kodi Satana amapezerapo mwayi wotani?
11-12. Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji kuopa anthu polimbana nafe?
11 Satana amagwiritsa ntchito kuopa anthu pofuna kutisiyitsa kuchita zomwe Yehova amafuna komanso kulalikira. (Luka 21:12; Chiv. 2:10) Mbali zosiyanasiyana za dziko la Satanali zimafalitsa mabodza oipa kwambiri okhudza Mboni za Yehova. Anthu amene amakhulupirira mabodzawa angamatinyoze ngakhalenso kutiukira. (Mat. 10:36) Koma kodi zimene Satana amachitazi ziyenera kutidabwitsa? Ayi. Iye ankachitanso zimenezi m’nthawi ya atumwi.—Mac. 5:27, 28, 40.
12 Koma sikuti kuopa kutsutsidwa ndi boma ndi chida chokhacho chimene Satana amagwiritsa ntchito. Ena amaopa kwambiri zimene achibale awo angachite chifukwa choti akhala a Mboni za Yehova, kuposa mmene angaopere kuchitiridwa nkhanza. Amakonda kwambiri achibale awowo ndipo amafuna kuti adziwe komanso kukonda Yehova. Zimawapweteka akamamva akulankhula zinthu zosalemekeza Mulungu woona komanso atumiki ake. Komabe nthawi zina achibale omwe poyamba anali otsutsa nawonso amayamba kuphunzira Baibulo. Koma kodi tingatani ngati anthu a m’banja lathu asiya kuchita nafe zinthu chifukwa cha zimene tayamba kukhulupirira?
13. Kodi kukhulupirira kuti Mulungu amatikonda kungatithandize bwanji achibale athu akatikana? (Salimo 27:10)
13 Tingalimbikitsidwe kwambiri ndi mfundo ya choonadi yopezeka pa Salimo 27:10. (Werengani.) Tikamakumbukira mmene Yehova amatikondera, timamva kuti ndife otetezeka pamene tikutsutsidwa. Timakhulupirira kuti iye adzatipatsa mphoto chifukwa chopirira. Kuposa aliyense, Yehova adzatipatsa zonse zimene timafunikira kuti tikhale ndi moyo, tizisangalala komanso tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Zimenezi ndi zimene Biniam yemwe tamutchula kale uja anazindikira.
14. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Biniam?
14 Biniam anakhala wa Mboni za Yehova ngakhale kuti ankadziwa kuti adzazunzidwa kwambiri. Taganizirani mmene kudziwa kuti Yehova amamukonda kunamuthandizira kuti asamaope anthu. Iye anati: “Ndinazunzidwa kwambiri, koma kuposa kuzunzidwa ndi boma, ndinkaopa kwambiri kutsutsidwa ndi anthu a m’banja langa. Ndinkaopa kuti zomwe ndinasankha kuti ndikhale wa Mboni za Yehova zikhumudwitsa bambo anga, ndipo anthu a m’banja lathu aziona kuti ndine wolephera.” Komabe, Biniam ankakhulupirira kuti Yehova amasamalira anthu omwe amawakonda. Iye anafotokoza kuti: “Ndinaganizira mmene Yehova anandithandizira kupirira mavuto a zachuma, kusalidwa komanso kuchitiridwa zachiwawa. Ndinkadziwa kuti iye adzandidalitsa ndikapitiriza kukhala wokhulupirika. Nditamangidwa maulendo angapo ngakhalenso kuzunzidwa, ndinadzionera ndekha kuti Yehova amatithandiza pa nthawi ya mavuto tikakhalabe okhulupirika.” Biniam anafika poona kuti Yehova ndi Atate wake enieni, ndipo atumiki ake anasonyeza kuti ndi anthu a m’banja lake.
KUOPA IMFA
15. N’chifukwa chiyani si zachilendo kuti timaopa imfa?
15 Baibulo limavomereza kuti imfa ndi mdani. (1Akor. 15:25, 26) Tikhoza kumada nkhawa tikaganizira za imfa makamaka ngati ifeyo kapena munthu amene timamukonda akudwala kwambiri. N’chifukwa chiyani timaopa imfa? Chifukwa Yehova anatilenga m’njira yoti tizilakalaka kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlal. 3:11) Ndipotu kuopa imfa moyenera kungatiteteze. Mwachitsanzo, kungatithandize kuti tizisankha moyenera pa nkhani ya zakudya komanso masewera olimbitsa thupi, kupeza thandizo lachipatala pakafunika kutero komanso kupewa kuchita zinthu zimene zingaike moyo wathu pachiswe.
16. Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji mantha achibadwa omwe timakhala nawo pa nkhani ya imfa pofuna kutisokoneza?
16 Satana amadziwa kuti timaona kuti moyo wathu ndi wamtengo wapatali. Komabe iye amanena kuti tikhoza kulolera kutaya chilichonse ngakhale ubwenzi wathu ndi Yehova, n’cholinga choti titeteze moyo wathu. (Yobu 2:4, 5) Komatu iye amakhala akudzinamiza. Ngakhale zili choncho, popeza kuti iye “ali ndi njira yobweretsera imfa,” amayesa kugwiritsa ntchito mantha achibadwa omwe timakhala nawo pa nkhani ya imfa kuti atichititse kusamvera Yehova. (Aheb. 2:14, 15) Nthawi zina anthu amene amatsogoleredwa ndi Satana amatiopseza kuti atipha ngati sitisiya kukhulupirira Yehova. Pamene tikufunika thandizo lachipatala mwamsanga, nthawi zina Satana angapezerepo mwayi wotichititsa kusankha zinthu molakwika. Madokotala kapena achibale omwe si a Mboni angatikakamize kuti tivomere kuikidwa magazi zomwe zingachititse kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Kapenanso munthu wina angatilimbikitse kuti tipeze thandizo la mankhwala losemphana ndi mfundo za m’Malemba.
17. Mogwirizana ndi Aroma 8:37-39, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa imfa?
17 Ngakhale kuti sitifuna kufa, timadziwa kuti Yehova sadzasiya kutikonda ngakhale titamwalira. (Werengani Aroma 8:37-39.) Anzake a Yehova akamwalira, iye amawakumbukirabe ndipo zimangokhala ngati adakali ndi moyo. (Luka 20:37, 38) Amafunitsitsa kudzawaukitsa. (Yobu 14:15) Yehova anapereka malipiro okwera kwambiri n’cholinga choti ‘tidzapeze moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16) Timadziwa kuti iye amatikonda kwambiri ndipo amatiganizira. Choncho m’malo mosiya Yehova tikakhala kuti tikudwala kapena tikhoza kufa, timamudalira kuti atilimbikitse, kutipatsa nzeru komanso kutipatsa mphamvu. Izi ndi zimene Valérie ndi mwamuna wake anachita.—Sal. 41:3.
18. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Valérie?
18 Ali ndi zaka 35, Valérie anapezeka ndi khansa yoopsa kwambiri. Taonani mmene kukonda Mulungu kunamuthandizira kuti asamaope imfa. Iye anati: “Zinthu zinasintha mwadzidzidzi pa moyo wathu nditangopezeka ndi khansayi. Ndinkafunika opaleshoni yaikulu kuti ndikhale ndi moyo. Ndinakambirana ndi madokotala ambiri, koma onsewa anakana kundichita opaleshoni yosaika magazi. Ndinkachita mantha, komabe poganizira lamulo la Mulungu sindikanalola kuikidwa magazi. Pa moyo wanga wonse Yehova wakhala akusonyeza kuti amandikonda kwambiri. Apa tsopano ndinali ndi mwayi womusonyeza kuti nanenso ndimamukonda. Nthawi zonse zikakhala kuti zinthu sizinayende bwino, ndinkatsimikiza mtima kuti ndisangalatse Yehova osati kuchititsa Satana kupambana. Kenako ndinachitidwa opaleshoni popanda kuikidwa magazi ndipo zinayenda bwino. Ngakhale kuti thanzi langa silili bwino, nthawi zonse Yehova amatipatsa zomwe tikufunikira. Mwachitsanzo, pamsonkhano wa kumapeto kwa mlungu womwe tinachita nditangotsala pang’ono kupezeka ndi khansayi, tinaphunzira nkhani yakuti ‘Limbani Mtima Pokumana ndi Mavuto.’ * Nkhaniyi inatilimbikitsa ndipo tinkaiwerenga mobwerezabwereza. Nkhani zofanana ndi imeneyi komanso kuchita zinthu zokhudza kulambira kwathandiza ine ndi mwamuna wanga kukhala ndi mtendere wa mumtima, kukhala oganiza bwino komanso kusankha zinthu mwanzeru.”
KUTHETSA MANTHA OMWE TILI NAWO
19. Kodi n’chiyani chichitike posachedwapa?
19 Mothandizidwa ndi Yehova, Akhristu padziko lonse akwanitsa kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana komanso kutsutsa Mdyerekezi. (1 Pet. 5:8, 9) Inunso mungakwanitse. Posachedwapa Yehova adzauza Yesu ndi olamulira anzake kuti “awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yoh. 3:8) Zimenezi zikadzachitika, anthu amene azidzatumikira Mulungu padzikoli ‘sadzaopa aliyense, ndipo chilichonse choopsa adzatalikirana nacho.’ (Yes. 54:14; Mika 4:4) Komabe pamene tikuyembekezera zimenezi tiyenera kumayesetsa kuthetsa mantha omwe tingakhale nawo.
20. N’chiyani chimene chingatithandize kusiya kuchita mantha?
20 Tiyenera kupitiriza kukhulupirira kwambiri kuti Yehova amakonda komanso kuteteza atumiki ake. Kuganizira ndiponso kukambirana mmene Yehova anatetezera atumiki ake mbuyomu kungatithandize kuchita zimenezi. Komanso tiziganizira mmene iye wakhala akutithandizira ifeyo patokha pa nthawi ya mavuto. Mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kusiya kuchita mantha.—Sal. 34:4.
NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira
^ Si nthawi zonse pamene mantha angakhale oipa. Mantha ena angatiteteze pomwe ena angachititse kuti tikumane ndi mavuto. Satana angagwiritse ntchito mantha potichititsa kusankha zolakwika. N’zoonekeratu kuti timafunika kuyesetsa kuti tisamakhale ndi mantha amenewo. Kodi n’chiyani chingatithandize? Monga mmene tionere munkhaniyi, tikamakhulupirira kuti Yehova ali kumbali yathu komanso amatikonda, sitingamaope chilichonse.
^ Mayina ena asinthidwa.