Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere”?

Yesu ankalalikira uthenga wamtendere. Koma pa nthawi ina anauza atumwi ake kuti: “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi, sindinabweretse mtendere koma lupanga. Pakuti ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa munthu kutsutsana ndi bambo ake, mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake, ndiponso mtsikana wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.” (Mat. 10:34, 35) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani?

Sikuti Yesu ankafuna kulekanitsa anthu apachibale. Koma ankadziwa kuti zimene ankaphunzitsa zingachititse kuti mabanja ena agawikane. Choncho amene akufuna kubatizidwa n’kukhala ophunzira a Khristu ayenera kudziwa zotsatirapo za chosankha chawo. Nthawi zina akamatsutsidwa ndi mwamuna kapena mkazi wawo ndiponso achibale awo omwe si a Mboni, zingakhale zovuta kutsatira zimene Khristu anaphunzitsa.

Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti ‘azikhala mwamtendere ndi anthu onse.’ (Aroma 12:18) Koma zimene Yesu anaphunzitsa zingakhale ngati “lupanga” m’mabanja ena. Zimenezi zimachitika ngati mmodzi m’banjamo walola kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa pamene ena akana. Zikatero achibalewo amakhala “adani” a munthu amene akuphunzira choonadiyo.​—Mat. 10:36.

Ophunzira a Khristu omwe ali m’mabanja amene anthu ake ndi osiyana zipembedzo, nthawi zina amakumana ndi zinthu zowachititsa kuti asonyeze ngati amakonda kwambiri Yehova ndi Yesu. Mwachitsanzo, achibale awo omwe si a Mboni angawakakamize kuti achite nawo holide inayake yachipembedzo. Ndiye akakumana ndi mayesero amenewa, kodi angasankhe kusangalatsa ndani? Yesu anati: “Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine.” (Mat. 10:37) Komabe Yesu sankatanthauza kuti amene asankha kukhala ophunzira ake asamakonde makolo awo. M’malomwake ankatsindika mfundo yakuti aziona zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri. Choncho ngati achibale omwe si a Mboni akutsutsa kulambira kwathu timapitiriza kuwakonda, koma timazindikira kuti chofunika kwambiri ndi kukonda Mulungu.

N’zoonekeratu kuti kutsutsidwa ndi achibale kungakhale kowawa kwambiri. Komabe ophunzira a Yesu amakumbukira mawu ake akuti: “Aliyense wosalandira mtengo wake wozunzikirapo ndi kunditsatira sali woyenera ine.” (Mat. 10:38) Tingati Akhristu amaona kuti kutsutsidwa ndi achibale awo ndi ena mwa mayesero omwe amayenera kukhala okonzeka kuwapirira. Komabe pa nthawi yofananayo, iwo amayembekezera kuti khalidwe lawo labwino lingachititse achibale awowo kusintha n’kuyamba kufuna kumva uthenga wa m’Baibulo.​—1 Pet. 3:1, 2.