“Lirani ndi Anthu Amene Akulira”
“Pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 ATES. 5:11.
NYIMBO: 121, 75
1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukambirana mmene tingalimbikitsire anthu oferedwa? (Onani chithunzi choyambirira.)
MLONGO wina dzina lake Susi ananena kuti: “Mwana wathu atamwalira, zinatipweteka koopsa pafupifupi kwa chaka chathunthu.” Nayenso m’bale wina ananena kuti mkazi wake atamwalira mwadzidzidzi, ankamva “ululu winawake wosaneneka.” Koma chomvetsa chisoni ndi chakuti mavuto ngati amenewa akuchitikira anthu ambiri. Ndipo Akhristu ambiri sankayembekezera kuti anthu amene amawakonda akhoza kumwalira Aramagedo isanachitike. Kaya nafenso tinaferedwa kapena ayi, tikhoza kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu oferedwa angalimbikitsidwe bwanji?’
2 Mwina munamva anthu akunena kuti nthawi ikamapita chisoni chimatha. Koma kodi ndi zoona kuti munthu amasiyadi kumva chisoni pakangopita nthawi? Mlongo wina wamasiye ananena kuti: “Ine ndimaona kuti zimene munthu amachita nthawi ikamadutsa n’zimene zimathandiza kuti ayambe kumva bwino.” Mofanana ndi bala kapena chilonda, chisoni chimatha mumtima
mwa munthu ngati munthuyo akusamalira mtima wakewo. Ndiye kodi n’chiyani chingathandize anthu oferedwa kuti chisoni chawo chiyambe kutha?YEHOVA NDI “MULUNGU AMENE AMATITONTHOZA M’NJIRA ILIYONSE”
3, 4. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amamvetsa mmene munthu amamvera akaferedwa?
3 Atate wathu wakumwamba Yehova ndi amene angatitonthoze kuposa munthu aliyense. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yomvera ena chisoni ndipo anauza anthu ake kuti: “Ineyo ndi amene ndikukutonthozani anthu inu.”—Yes. 51:12; Sal. 119:50, 52, 76.
4 Nayenso Atate wathu wachifundo anaona anthu amene ankawakonda akumwalira ndipo ena a iwo anali Abulahamu, Isaki, Yakobo, Mose ndiponso Davide. (Num. 12:6-8; Mat. 22:31, 32; Mac. 13:22) Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Yehova akufunitsitsa kwambiri kuti adzawaukitse. (Yobu 14:14, 15) Anthu amenewa akadzaukitsidwa adzakhala osangalala komanso athanzi. Tisaiwalenso kuti Mwana wokondedwa wa Mulungu, yemwe ‘ankasangalala naye,’ anafa imfa yopweteka kwambiri. (Miy. 8:22, 30) Pa nthawi imeneyi, Yehova ayenera kuti anamva kupweteka kosaneneka.—Yoh. 5:20; 10:17.
5, 6. Kodi Yehova angatilimbikitse bwanji?
5 Sitiyenera kukayikira kuti Yehova angatithandize ngati taferedwa. Choncho tiyenera kupemphera kwa iye n’kumuuza mmene tikumvera mumtima mwathu. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa chisoni chathu ndipo angatilimbikitse m’njira yoyenerera. Koma kodi amatilimbikitsa bwanji?
6 Chinthu chimodzi chimene Mulungu amachita ndi kutipatsa mzimu woyera kuti utilimbikitse. (Mac. 9:31) Mzimu wa Mulungu ndi wamphamvu ndipo ungatilimbikitse kwambiri. Yesu analonjeza kuti Atate wakumwamba adzapereka “mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Susi, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Nthawi zambiri tinkangogwada n’kumachonderera Yehova kuti atilimbikitse. Nthawi iliyonse imene tinkachita zimenezi, mtendere wa Mulungu unkateteza mitima ndiponso maganizo athu.”—Werengani Afilipi 4:6, 7.
YESU NDI MKULU WA ANSEMBE WACHIFUNDO
7, 8. N’chifukwa chiyani sitingakayikire zoti Yesu angatilimbikitse?
7 Zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita ali padzikoli zimasonyeza bwino chifundo cha Yehova. (Yoh. 5:19) Mulungu anatumiza Mwana wakeyu padziko kuti alimbikitse “anthu osweka mtima” komanso atonthoze “anthu onse olira.” (Yes. 61:1, 2; Luka 4:17-21) N’chifukwa chake iye anali wachifundo, ankamvetsa mavuto a anthu komanso ankafunitsitsa kuwathandiza.—Aheb. 2:17.
8 Yesu ali wamng’ono ayenera kuti anavutika mumtima kuona achibale ake kapena anzake akumwalira. Zikuoneka kuti Yosefe, yemwe anali bambo ake omulera, anamwalira iye adakali wachinyamata. * Pa nthawiyo Yesu ayenera kuti anali asanakwanitse zaka 20 kapena ali ndi zaka za m’ma 20. Ndiye poti anali ndi mtima wachifundo, ayenera kuti ankavutika ndi chisoni komanso ankamvera chisoni mayi ake ndi abale ake.
9. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo Lazaro atamwalira?
9 Yesu atayamba utumiki wake, ankachita zinthu mozindikira kwambiri komanso mwachifundo. Chitsanzo ndi zimene anachita Lazaro atamwalira. Ngakhale kuti ankadziwa zoti amuukitsa, zinamupweteka kwambiri ataona chisoni chimene Mariya ndi Marita anali nacho. Chifukwa cha mtima wake wachifundo anavutika kwambiri mumtima mpaka anagwetsa misozi.—10. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu amachitirabe anthu chifundo masiku ano?
10 Kodi chifundo cha Yesu chingatithandize bwanji masiku ano? Baibulo limanena kuti “Yesu Khristu ali chimodzimodzi dzulo ndi lero, ndiponso mpaka muyaya.” (Aheb. 13:8) Popeza Yesu yemwe ndi “Mtumiki Wamkulu wa moyo” amamvetsa mmene zimakhalira munthu akaferedwa, “amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.” (Mac. 3:15; Aheb. 2:10, 18) Choncho tingadziwe kuti Khristu sanasiye kumvera chisoni anthu, kumvetsa mmene akumvera ndiponso kuwalimbikitsa ‘pa nthawi imene akufunika thandizo.’—Werengani Aheberi 4:15, 16.
‘MALEMBA ANGAWALIMBIKITSE’
11. Kodi ndi malemba ati amene amakulimbikitsani kwambiri?
11 Nkhani yoti Yesu anamva chisoni kwambiri Lazaro atamwalira ndi yolimbikitsa kwambiri ndipo m’Baibulo muli malemba ena ambiri olimbikitsa. M’pake kuti Baibulo limati: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Ngati inuyo mwaferedwa, mukhoza kulimbikitsidwa ndi malemba ngati awa:
-
“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Sal. 34:18, 19.
-
“Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu [Yehova] otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Sal. 94:19.
-
“Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njira yosalephera ndiponso anatipatsa chiyembekezo chabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu.”—2 Ates. 2:16, 17. *
MPINGO UNGAWALIMBIKITSE
12. Tchulani njira ina imene tingalimbikitsire anthu amene ali ndi chisoni.
12 Mpingo wachikhristu ukhozanso kulimbikitsa anthu amene aferedwa. (Werengani 1 Atesalonika 5:11.) Kodi inuyo mungalimbikitse bwanji anthu amene ‘asweka mtima’? (Miy. 17:22) Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Mlongo wina wamasiye dzina lake Dalene ananena kuti: “Anthu amene aferedwa amafuna kufotokoza maganizo awo komanso mmene akumvera mumtima. Choncho chinthu chofunika kwambiri chimene tingawachitire ndi kuwamvetsera popanda kuwadula mawu.” Mlongo winanso dzina lake Junia, amene mchimwene wake anadzipha, ananena kuti: “Mwina sitingamvetse chisoni chimene munthu woferedwa ali nacho koma chofunika kwambiri ndi mtima wofuna kudziwa mmene akumvera.”
13. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya chisoni?
13 Tizikumbukiranso kuti chisoni cha anthu Miy. 14:10) Nthawi zina munthu angafotokoze mmene akumvera koma ena sangamvetse bwinobwino zimene akunenazo.
chimakhala chosiyanasiyana. Nthawi zina munthu amangodziwa yekha mmene akumvera mumtima mwake ndipo sangafotokoze bwinobwino mmene akumvera. Paja Mawu a Mulungu amati: “Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu, ndipo mlendo sangalowerere pamene mtimawo ukusangalala.” (14. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene aferedwa?
14 Kunena zoona, n’zovuta kudziwa mawu amene tinganene kwa munthu amene akumva chisoni kwambiri. Komabe Baibulo limanena kuti “lilime la anthu anzeru limachiritsa.” (Miy. 12:18) Ena amapeza mfundo zolimbikitsa m’kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. * Koma nthawi zambiri chomwe chimafunika ndi ‘kulira ndi anthu amene akulira.’ (Aroma 12:15) Mlongo wina dzina lake Gaby, yemwe mwamuna wake anamwalira, ananena kuti: “Ine ndimaona kuti kulira kumathandiza kuti anthu ena adziwe mmene ndikumvera. Choncho anzanga akamalira nane zimandilimbikitsa. Ndimaona kuti sindikumva ndekha chisonicho.”
15. Kodi tingatani ngati zikutivuta kulimbikitsa munthu pamasom’pamaso? (Onaninso bokosi lakuti “ Mawu Amene Angalimbikitse Anthu Oferedwa.”)
15 Ngati simungathe kunena mawu olimbikitsa pamasom’pamaso, mukhoza kungolemba khadi, imelo, meseji kapena kalata. Mukhoza kungolembapo lemba limodzi lolimbikitsa, khalidwe lina labwino limene womwalirayo anali nalo kapena zinthu zina zosangalatsa zimene munachitira limodzi. Junia anati: “Ndikalandira uthenga wolimbikitsa kapena ndikapemphedwa kuti ndikacheze ndi
Mkhristu wina zimandilimbikitsa kwambiri. Ndimaona kuti anthu amandikonda komanso kundiganizira.”16. Kodi chinthu china chofunika kwambiri polimbikitsa oferedwa n’chiyani?
16 Kupemphera ndi Akhristu anzathu amene aferedwa kapena kuwapempherera kumathandizanso kwambiri. Pa nthawi yovuta ngati imeneyi munthu akhoza kuvutika kuti anene zomveka m’pemphero. Koma ngakhale atapemphera uku akunjenjemera kapena kulira, akhoza kuthandiza kwambiri munthu woferedwayo. Mlongo Dalene, amene tamutchula uja, ananena kuti: “Nthawi zina alongo akabwera kudzandilimbikitsa ndinkawapempha kuti apemphere. Nthawi zambiri akamayamba pempherolo ankavutika koma kenako mawu awo ankayamba kumveka bwinobwino ndipo mapemphero awo ankakhala olimbikitsa kwambiri. Ndimalimbikitsidwa ndikaganizira chikhulupiriro chawo, chikondi chawo komanso mtima wawo woganizira ena.”
PITIRIZANI KUWALIMBIKITSA
17-19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kulimbikitsa munthu amene waferedwa?
17 Anthu amamva chisoni mosiyanasiyana. Choncho ndi bwino kupitiriza kulimbikitsa munthu ngakhale achibale kapena anzake amene ankamulimbikitsa pa nthawi ya maliro atachoka. Paja “bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Abale ndi alongo ayenera kulimbikitsa munthu mpaka nthawi imene chisoni chake chachepa.—Werengani 1 Atesalonika 3:7.
18 Tizikumbukira kuti anthu oferedwa akhoza kumvanso chisoni pa nthawi inayake pa chaka, akamva nyimbo inayake, kuona zithunzi, kuchita zinthu zina komanso akamva fungo kapena phokoso linalake. Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira angavutike kwambiri akayambiranso kuchita zinthu zina payekha monga kupita kumsonkhano kapena ku Chikumbutso. M’bale wina anati: “Ndinkaona kuti ndidzavutika kwambiri likadzafika tsiku limene tinakwatirana ndipo zinalidi zovuta. Koma abale ndi alongo ena anakonza zoti ndikacheze ndi anzanga apamtima pa tsikulo n’cholinga choti ndisakhale ndekha.”
19 Koma tizikumbukiranso kuti anthu amene aferedwa amafunikira kuwalimbikitsa nthawi zonse, osati pa nthawi zapadera zokha. Junia ananena kuti: “Anthu akacheza nawe ndiponso kukuthandiza, ngakhale pamene palibe zifukwa zapadera, umalimbikitsidwa kwambiri.” N’zoona kuti sitingathetseretu chisoni cha munthu amene waferedwa koma tikhoza kumulimbikitsa m’njira zosiyanasiyana. (1 Yoh. 3:18) Gaby anati: “Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha akulu achikondi amene ankandithandiza kwambiri mwamuna wanga atamwalira. Ndinkamva ngati Yehova wandikumbatira mwachikondi.”
20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malonjezo a Yehova ndi olimbikitsa kwambiri?
20 Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira kuti Yehova adzathetseratu chisoni chathu pamene “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Khristu] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Mulungu yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa walonjeza kuti ‘adzameza imfa kwamuyaya ndiponso adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.’ (Yes. 25:8) Pa nthawiyo, sipadzakhalanso ‘zolira ndi anthu amene akulira,’ m’malomwake ‘tizidzasangalala ndi anthu amene akusangalala.’—Aroma 12:15.
^ ndime 8 Yosefe anatchulidwa komaliza pamene Yesu anali ndi zaka 12. Pa nthawi imene Yesu anachita chinthu chodabwitsa choyamba, chomwe ndi kusandutsa madzi kukhala vinyo, Yosefe sanatchulidwe ndipo satchulidwanso munkhani zina zotsatira. Ndipo Yesu ali pamtengo wozunzikirapo, anauza mtumwi Yohane kuti azisamalira mayi ake. Akanakhala kuti Yosefe anali moyo, Yesu sakananena zimenezi.—Yoh. 19:26, 27.
^ ndime 11 Malemba ena amene amalimbikitsa anthu ndi Salimo 20:1, 2; 31:7; 38:8, 9, 15; 55:22; 121:1, 2; Yesaya 57:15; 66:13; Afilipi 4:13 ndiponso 1 Petulo 5:7.
^ ndime 14 Onaninso nkhani yakuti “Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2010.