NKHANI YOPHUNZIRA 9
Muzitsanzira Yesu Potumikira Ena
“Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—MAC. 20:35.
NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi anthu a Yehova amachita zinthu zabwino ziti?
KALERO, Baibulo linaneneratu kuti anthu a Mulungu “adzadzipereka mofunitsitsa” potumikira Yehova motsogoleredwa ndi Mwana wake. (Sal. 110:3) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. Chaka chilichonse atumiki akhama a Yehova, amalalikira kwa maola ambiri. Iwo amachita zimenezi mwakufuna kwawo ndipo amagwiritsa ntchito zinthu zawo. Amathandizanso abale ndi alongo awo kupeza zimene akufunikira, kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Abale audindo amakhala maola ambiri akukonzekera mbali zimene apatsidwa pamisonkhano komanso kuchita maulendo aubusa kwa abale ndi alongo awo. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu a Yehova amachita zinthu zonsezi? N’chifukwa chakuti iwo amakonda Yehova komanso anzawo.—Mat. 22:37-39.
2. Mogwirizana ndi Aroma 15:1-3, kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani?
2 Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri poika patsogolo zofuna za ena m’malo mwa zofuna zake. Timachita zonse zomwe tingathe pomutsanzira. (Werengani Aroma 15:1-3.) Anthu omwe amayesetsa kumutsanzira adzapeza madalitso. Yesu ananena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Mac. 20:35.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi tikambirana zimene Yesu anachita kuti azitha kutumikira ena komanso mmene tingamutsanzirire. Tionanso zimene tingachite kuti tizikhala ndi mtima wofunitsitsa kutumikira ena.
MUZITSANZIRA YESU
4. Kodi Yesu anatani kuti aike zofuna za ena patsogolo osati zake?
4 Yesu ankathandiza ena ngakhale atatopa. Taganizirani zimene Yesu anachita ataona khamu la anthu likubwera kwa iye ali m’mbali mwa phiri, mwina pafupi ndi ku Kaperenao. Iye anali atachezera kupemphera usiku wonse. Ayenera kuti anali atatopa kwambiri. Koma ataona khamu la anthulo, iye anayamba kuganizira kwambiri za odwala komanso osauka amene anali pamenepo. Sikuti Yesu anangochiritsa odwalawo, koma anakambanso imodzi mwa nkhani zolimbikitsa kwambiri yomwe imadziwika kuti ulaliki wa paphiri.—Luka 6:12-20.
5. Kodi amuna omwe ndi mitu ya mabanja amatsanzira bwanji Yesu pamene atopa?
5 Zimene mitu ya mabanja imachita potsanzira Yesu. Taganizirani chitsanzo ichi: Pambuyo pogwira ntchito tsiku lonse, mwamuna yemwe ndi mutu wabanja akufika pakhomo atatopa. Ngakhale kuti akukhala ndi maganizo oti asachite kulambira kwa pabanja patsikulo, iye akupempha Yehova kuti amupatse mphamvu kuti achititsebe kulambirako. Yehova akuyankha pemphero lake ndipo kulambirako kukuchitika monga mwa nthawi zonse. Tsiku limenelo ana ake akuphunzira mfundo yofunika kwambiri yakuti makolo awo, amaona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambiri kuposa china chilichonse.
6. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene Yesu anagwiritsira ntchito nthawi yochita zinthu payekha pothandiza ena.
6 Yesu ankathandiza ena ngakhale panthawi imene ankafunika kuchita zinthu payekha. Taganizirani mmene Yesu anamvera atadziwa kuti mnzake, Yohane M’batizi waphedwa. Iye ayenera kuti anamva chisoni kwambiri. Baibulo limati: “Yesu atamva zimenezi, [zokhudza kuphedwa kwa Yohane], anachoka kumeneko pa ngalawa n’kupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.” (Mat. 14:10-13) Tingamvetse chifukwa chake ankafuna kukhala payekha. Ambirife timakonda kukhala kwatokha tikakhala ndi chisoni. Komatu kwa Yesu zimenezi sizinatheke. Khamu la anthu linakafika kumaloko iye asanafikeko n’komwe. Ndiye kodi Yesu anatani? Anayamba kuganizira zimene anthuwo ankafunikira ndipo “anawamvera chifundo.” Iye ankachita kuoneratu kuti anthuwo akufunika kulimbikitsidwa mwauzimu, moti anawalimbikitsadi. Ndipotu “anayamba kuwaphunzitsa [osati zinthu zochepa, koma] zinthu zambiri.”—Maliko 6:31-34; Luka 9:10, 11.
7-8. Perekani chitsanzo cha mmene akulu achikondi amatsanzirira Yesu pothandiza ena.
7 Mmene akulu achikondi amatsanzirira Yesu. Timayamikira kwambiri ntchito zimene akulu odzipereka amagwira potithandiza. Zambiri mwa ntchito zimene amagwirazi, abale ndi alongo mumpingo saziona. Mwachitsanzo, akulu amene ali m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala, amafulumira kuti akathandize Akhristu anzawo pakafunika thandizo. Ndipotu nthawi zambiri zimenezi zimachitika pakati pa usiku. Koma chifukwa chokonda abale ndi alongo omwe akumana ndi mavutowo, akuluwa limodzi ndi mabanja awo amaika patsogolo zofuna za Akhristu anzawo m’malo mwa zofuna zawo.
8 Akulu amathandizanso pantchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi zinthu zina za gulu komanso amathandiza pakachitika ngozi. Ndipo pali zambiri zomwe tinganene zimene akulu mumpingo wathu amachita potilangiza, kutilimbikitsa komanso kutithandiza. Timafunika kumayamikira kwambiri abale amenewa komanso mabanja awo. Yehova apitirize kuwadalitsa chifukwa cha mtima wawo wodzipereka. Komabe mofanana ndi aliyense, akulu nawonso amafunika kuchita zinthu moganiza bwino. Iwo sayenera kumangokhalira kuchita zinthu zokhudza utumiki wawo mpaka kufika polephera kusamalira mabanja awo.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIKHALE NDI MTIMA WOFUNITSITSA KUTHANDIZA ENA
9. Mogwirizana ndi Afilipi 2:4, 5, kodi Akhristu onse ayenera kukhala ndi maganizo otani?
9 Werengani Afilipi 2:4, 5. N’zoona kuti tonsefe si akulu komabe tingathe kutsanzira mtima wa Yesu wofunitsitsa kuthandiza ena. Baibulo limati iye anakhala “ngati kapolo.” (Afil. 2:7) Taganizirani zimene mfundo imeneyi ikutanthauza. Kapolo wabwino ankayesetsa kuchita zimene angathe kuti azisangalatsa mbuye wake. Monga kapolo wa Yehova komanso munthu amene amatumikira abale ake, n’zosakaikitsa kuti mumafuna kuchita zambiri potumikira Yehova komanso Akhristu anzanu. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuchita zimenezi.
10. Kodi tingadzifunse mafunso ati?
10 Muzifufuza zolinga zanu. Muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndine wofunitsitsa kuika zofuna za ena patsogolo kuti ndiwathandize? Mwachitsanzo, kodi ndimatani ngati ndikapemphedwa kuti ndikachezere m’bale wachikulire kapenanso kutenga mlongo wachikulire popita kumisonkhano? Kodi ndimafulumira kudzipereka pakafunika anthu oti akathandize kuyeretsa malo a msonkhano kapena kukonza Nyumba ya Ufumu?’ Yehova amasangalala ngati chifukwa cha chikondi timapereka nthawi ndi zinthu zathu kwa iye pothandiza ena. Kodi tingatani ngati tikuona kuti tikufunika kusintha mmene timachitira zinthu pothandiza ena?
11. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tizifunitsitsa kuthandiza ena?
11 Muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Tiyerekeze kuti mwazindikira kuti mukufunika kukonza zinthu zina, koma mukuona kuti mulibe mtima wofuna kuchita zimenezo. Ngati zili choncho, muzipemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Muzimuuza moona mtima mmene mukumvera. Ndipo muzimupempha kuti ‘alimbitse zolakalaka zanu,’ kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.
12. Kodi m’bale wachinyamata wobatizidwa angathandize bwanji mumpingo?
12 Ngati ndinu m’bale wachinyamata komanso wobatizidwa, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri mumpingo. M’mayiko ambiri akulu ndi ochuluka poyerekeza ndi atumiki othandiza ndipo ambiri mwa atumiki othandizawa si achinyamata. Pamene gululi likukula pakufunika abale achinyamata ambiri oti athandize kusamalira anthu a Yehova. Mukhoza kusangalala kwambiri ngati muli ofunitsitsa kutumikira paliponse pamene pakufunikira. Chifukwa chiyani? Chifukwa mudzasangalatsa Yehova, mudzakhala ndi mbiri yabwino komanso mudzapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chothandiza ena.
13-14. Kodi tingachite zinthu ziti pofuna kuthandiza abale ndi alongo athu? (Onani chithunzi chapachikuto.)
13 Muzikhala tcheru kuti muone zimene ena akufunikira. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a Chiheberi kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheb. 13:16) Amenewatu anali malangizo othandiza. Chifukwa pasanapite nthawi yayitali kuchokera pamene analandira kalatayi, Akhristu a ku Yudeya ankafunika kusiya nyumba, mabizinezi komanso achibale awo omwe sanali Akhristu, ‘n’kuyamba kuthawira kumapiri.’ (Mat. 24:16) N’zosachita kufunsa kuti panthawiyi iwo ankafunika kwambiri kuthandizana. Ngati Akhristuwa akanakhala kuti anali atayamba kale kutsatira malangizo a Paulo akuti azigawana zimene ali nazo, zikanakhala zosavuta kuzolowera moyo wawo watsopano kumene analowera.
14 Si nthawi zonse pamene abale ndi alongo athu angatiuze zimene akufunikira. Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti m’bale wina, mkazi wake wamwalira. Kodi m’baleyo akufunika kumuthandiza pankhani ya chakudya, mayendedwe kapena ntchito zapakhomo? N’kutheka kuti iye sanganene chilichonse poopa kuti ativutitsa. Koma akhoza kuyamikira kwambiri ngati titamuthandiza popanda kudikira kuti achite kutipempha. Sitiyenera kungoganiza kuti ena amuthandiza kapenanso kuti nthawi zonse azitifotokozera mmene tingamuthandizire. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikanakhala ineyo ndikanafuna kuti ena andithandize bwanji?’
15. Kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani kuti tizithandiza ena?
15 Muzikhala ofikirika. Mosakaikira mukudziwa abale ndi alongo mumpingo wanu amene amakhala okonzeka kuthandiza ena. Koma iwo samatichititsa kuti tiziona ngati tikuwavutitsa. Timadziwa kuti tingawadalire tikakumana ndi vuto ndipo timafuna kuwatsanzira. Alan, mkulu yemwe ali ndi zaka za m’ma 40, amafuna kuti anthu ena azimasuka kumupempha thandizo. Poganizira chitsanzo cha Yesu, Alan ananena kuti: “Yesu ankakhala wotanganidwa koma anthu amisinkhu yonse ankamukonda ndipo sankaopa kumupempha kuti awathandize. Iwo ankamuona monga munthu amene amawakonda kwambiri. Ndimafunitsitsa kutengera chitsanzo chake n’kumadziwika monga munthu amene ndi wofikirika, waubwenzi komanso woganizira ena.”
16. Kodi kugwiritsa ntchito malangizo a pa Salimo 119:59, 60, kungatithandize bwanji kutsanzira Yesu mosamala kwambiri?
16 Sitiyenera kukhumudwa ngati tikuona kuti tikulephera kutsatira Yesu ndendende. (Yak. 3:2) Mwachitsanzo, wophunzira sangathe kutsatira ndendende zimene mphunzitsi wake wachita. Koma akamaphunzirapo kathu pa zimene akulakwitsa, n’kumayesetsa kutsatira mphunzitsi wakeyo mosamala kwambiri, iye angapitirize kuwonjezera luso lake. Mofanana ndi zimenezi tikamagwiritsira ntchito zimene taphunzira pophunzira Baibulo patokha, komanso kuyesetsa kukonza zimene timalakwitsa, tingakwanitse kutsatira chitsanzo chimene Yesu anatisiyira.—Werengani Salimo 119:59, 60.
MADALITSO AMENE TIMAPEZA CHIFUKWA CHOFUNITSITSA KUTHANDIZA ENA
17-18. Kodi tidzapeza madalitso otani chifukwa chotsanzira mtima wa Yesu wofunitsitsa kuthandiza ena?
17 Anthu ena akhoza kutengera mtima wathu wofuna kuthandiza ena. M’bale wina dzina lake Tim ananena kuti: “Tili ndi abale ambiri achinyamata amene anapita patsogolo mpaka kufika pokhala atumiki othandiza ndipo ena anachita zimenezi ali ndi zaka zochepa kwambiri. Chifukwa chotsanzira mtima wofunitsitsa kuthandiza ena umene ena anasonyeza, abale amenewa amathandiza kwambiri mpingo komanso akulu.”
18 Tikukhala m’dziko limene anthu ambiri ndi odzikonda. Koma anthu a Yehova ndi osiyana ndi anthu a m’dzikoli. Timakhudzidwa ndi mtima umene Yesu anali nawo wofuna kuthandiza ena ndipo ndife otsimikiza kuti tizimutsanzira. N’zoona kuti sitingathe kumutsanzira ndendende komabe tingathe ‘kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’ (1 Pet. 2:21) Tikamachita zonse zimene tingathe potsanzira mtima umene Yesu anali nawo wofuna kuthandiza ena, ifenso tidzapeza chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chakuti Yehova akusangalala nafe.
NYIMBO NA. 13 Khristu ndi Chitsanzo Chathu
^ ndime 5 Nthawi zonse Yesu ankaika zofuna za ena patsogolo osati zake. Munkhaniyi tikambirana mmene tingamutsanzirire. Tikambirananso madalitso amene tingapeze chifukwa chotsanzira mtima wa Yesu wofunitsitsa kuthandiza ena.
^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Dan, yemwe ndi m’bale wachinyamata akuona zimene akulu awiri achita pobwera kudzaona bambo ake kuchipatala. Iye wakhudzidwa kwambiri ndi chikondi chimene akuluwo asonyeza. Nayenso akukhala tcheru kuti azithandiza ena mumpingo. M’bale wina wachinyamata dzina lake Ben, akuona zimene Dan akuchita posonyeza kuganizira ena. Chitsanzo cha Dan chikulimbikitsa Ben kuti athandize pantchito yokonza Nyumba ya Ufumu.