Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 49

NYIMBO NA. 147 Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha

Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha?

Kodi Tiyenera Kuchita Chiyani Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha?

“Aliyense wovomereza Mwana komanso kumukhulupirira [adzakhala] ndi moyo wosatha.”​—YOH. 6:40.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona mmene nsembe ya Yesu Khristu imathandizira odzozedwa komanso a nkhosa zina.

1. Kodi anthu ena amamva bwanji akaganizira za moyo wosatha?

 ANTHU ambiri amakhala osamala ndi zimene amadya komanso amachita masewera olimbitsa thupi pafupipafupi kuti akhale athanzi. Komabe iwo amadziwa kuti kuchita zimenezi sikungawathandize kuti asakalambe kapena kufa. Choncho iwo amaganiza kuti n’zosatheka kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Ngakhale zili choncho, Yesu anafotokoza kuti n’zotheka kudzapeza “moyo wosatha.” Chitsanzo ndi zimene ananena pa Yohane 3:16 ndi 5:24.

2. Kodi Yesu ananena chiyani zokhudza moyo wosatha mu Yohane chaputala 6? (Yohane 6:39, 40)

2 Tsiku lina Yesu anachita zodabwitsa pomwe anadyetsa gulu la anthu mkate ndi nsomba. a Zimenezi zinalidi zodabwitsa, koma zodabwitsa kwambiri ndi zimene ananena tsiku lotsatira. Gulu la anthu linamutsatira ku Kaperenao pafupi ndi nyanja ya Galileya komwe iye anawauza kuti akufa adzaukitsidwa komanso adzakhala ndi moyo wosatha. (Werengani Yohane 6:39, 40.) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti n’chiyani chomwe chidzachitikire anzanu ndi achibale anu omwe anamwalira? Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti anthu ambiri omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo inuyo limodzi ndi anthu amene mumawakonda mudzakhala ndi moyo mpaka kalekale. Komabe mawu ena a Yesu a mu Yohane chaputala 6 anali ovuta kwa anthu ambiri kuti awamvetse. Tiyeni tione zimene iye ananena.

3. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani zokhudza iyeyo pa Yohane 6:51?

3 Gulu la anthu ku Kaperenao linaona kugwirizana komwe kunalipo pakati pa mkate umene Yesu anali atangowapatsa kumene ndi mana amene Yehova anapereka kwa makolo awo. Malemba amatchula mana kuti “chakudya chochokera kumwamba.” (Sal. 105:40; Yoh. 6:31) Yesu anagwiritsa ntchito mana pofuna kuwathandiza kumvetsa mfundo imene ankafuna kuwaphunzitsa. Ngakhale kuti mana anali chakudya chimene Mulungu anapereka modabwitsa, patapita nthawi anthu amene anadya anamwalira. (Yoh. 6:49) Mosiyana ndi zimenezi Yesu anadzitchula kuti anali “chakudya chenicheni chochokera kumwamba,” “chakudya chimene Mulungu wapereka,” komanso “chakudya chopatsa moyo.” (Yoh. 6:32, 33, 35) Yesu anafotokoza kusiyana komwe kunalipo kapakati pa mana ndi iyeyo. Iye anati: “Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati wina atadya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha.” (Werengani Yohane 6:51.) Ayudawo sanamvetse zimene iye ananenazi. Iwo sankamvetsa chifukwa chake Yesu ananena kuti anali “chakudya” choposa mana amene Mulungu anapereka modabwitsa kwa makolo awo. Kenako iye anafotokoza mfundo yochititsa chidwi pomwe ananena kuti: “Chakudya chimene ndidzapereke . . . ndi mnofu wangawu.” Kodi iye ankatanthauza chiyani? M’pofunika kumvetsa zimenezi chifukwa zimatithandiza kudziwa mmene zidzakhalire zotheka kuti ifeyo ndi anthu amene timawakonda tidzapeze moyo wosatha. Tiyeni tione zimene Yesu ankatanthauza.

CHAKUDYA CHOPATSA MOYO KOMANSO MNOFU WAKE

4. N’chifukwa chiyani ena anadabwa ndi zimene Yesu ananena?

4 Ena mwa anthu omwe ankamumvetsera Yesu anadabwa kwambiri pamene iye ananena kuti adzapereka “mnofu [wake] kuti dzikoli lipeze moyo.” Mwina iwo ankaganiza kuti iye adzawapatsa mnofu wake weniweni kuti adye. (Yoh. 6:52) Pambuyo pake iye ananena zinanso zimene zinawazunguza kwambiri. Yesu anati: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.”​—Yoh. 6:53.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sankatanthauza kuti anthuwo amwe magazi ake enieni?

5 Kale mu nthawi ya Nowa, Mulungu analetsa anthu kuti asamadye magazi. (Gen. 9:3, 4) Yehova anabwerezanso lamuloli m’Chilamulo chimene anapereka kwa Aisiraeli. Aliyense wodya magazi ankayenera ‘kuphedwa.’ (Lev. 7:27) Yesu ankamvera malamulo omwe Mulungu anapereka m’Chilamulo. (Mat. 5:17-19) Choncho zinali zosamveka kuti iye auze Ayudawo kuti adye mnofu kapena kumwa magazi ake. Koma ndi mawu amenewa, Yesu ankaphunzitsa anthuwo mmene angapezere “moyo wosatha.”​—Yoh. 6:54.

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pa Yohane 6:53, Yesu anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa?

6 Kodi Yesu ankatanthauza chiyani? Apa n’zoonekeratu kuti Yesu anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa ngati mmene anachitira polankhula ndi mayi wa Chisamariya pomwe anati: “Koma amene adzamwe madzi amene ine ndidzamupatse sadzamvanso ludzu ngakhale pangʼono. Madzi amene ndidzamupatsewo adzasanduka kasupe wa madzi amene akutuluka mwa iye nʼkumupatsa moyo wosatha.” (Yoh. 4:7, 14) b Yesu sankatanthauza kuti mayiyo adzapeza moyo wosatha pongomwa madzi enieni. Mofanana ndi zimenezi iye sankatanthauza kuti anthu omwe ankalankhula nawo ku Kaperenao adzapeza moyo wosatha ngati atadya mnofu wake weniweni komanso kumwa magazi ake.

ZIMENE ANALANKHULANSO PA NTHAWI INA

7. Kodi ena amanena zotani zokhudza mawu a Yesu a pa Yohane 6:53?

7 Anthu ena achipembedzo amanena kuti mawu a Yesu a pa Yohane 6:53, okhudza kudya mnofu komanso kumwa magazi ake, amafotokoza zimene ziyenera kuchitika pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Amatero chifukwa pamwambowu anagwiritsanso ntchito mawu ofanana ndi amenewa. (Mat. 26:26-28) Iwo amanena kuti aliyense yemwe wapezeka pamwambowu ayenera kudya mkate komanso kumwa vinyo. Kodi zimenezi ndi zoona? M’pofunika kupeza yankho la funso limeneli chifukwa chaka chilichonse, anthu mamiliyoni padziko lonse amasonkhana nafe pamwambowu. Munkhaniyi tiona kuti zimene ananena pa Yohane 6:53, n’zosiyana ndi zimene ananena pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.

8. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa zochitika ziwirizi? (Onaninso chithunzi.)

8 Tiyeni tione kusiyana kwa zochitika ziwirizi. Choyamba, kodi ndi liti, nanga ndi kuti kumene Yesu analankhula mawu amene ali pa Yohane 6:53-56? Iye analankhula zimenezi kwa Ayuda ku Galileya mu 32 C.E. Ndipo panali patatsala pafupifupi chaka chimodzi kuti ayambitse mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ku Yerusalemu. Chachiwiri, kodi ankalankhula ndi ndani? Anthu ambiri amene ankamumvetsera ku Galileya ankangofuna kupeza chakudya osati kufuna kuphunzira zokhudza Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 6:26) Ndipo Yesu atalankhula zinthu zimene iwo sanazimvetse sanachedwe kusiya kumukhulupirira. Ngakhalenso ena mwa ophunzira ake anasiya kumutsatira. (Yoh. 6:14, 36, 42, 60, 64, 66) Ndiye yerekezerani zimenezi ndi zomwe zinachitika patapita pafupifupi chaka mu 33 C.E. pomwe Yesu anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Pamwambowu atumwi ake okhulupirika 11 anali naye limodzi ngakhale kuti iwo sankamvetsa zonse zimene iye ankaphunzitsa. Mosiyana ndi anthu a ku Galileya aja, atumwiwa sankakayikira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu yemwe anatsika kuchokera kumwamba. (Mat. 16:16) Iye anawayamikira kuti: “Inu ndi amene mwakhalabe ndi ine mʼmayesero anga.” (Luka 22:28) Kusiyana kuwiriku kukusonyeza kuti mawu a Yesu a pa Yohane 6:53, sakufotokoza zomwe ziyenera kuchitika pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Koma palinso maumboni ena omwe amasonyeza kuti pali kusiyana.

Mu Yohane chaputala 6 amafotokoza zimene Yesu anauza Ayuda ku Galileya (kumanzere). Patatha chaka chimodzi analankhula ndi kagulu kochepa ka ophunzira ake okhulupirika ku Yerusalemu (kumanja) (Onani ndime 8)


ZIMENE MAWU A YESU AMATANTHAUZA KWA INU

9. Kodi mawu amene Yesu ananena pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye amanena za ndani?

9 Pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye Yesu anapereka mkate wopanda chofufumitsa kwa atumwi ake ndipo anawauza kuti ukuimira thupi lake. Kenako anawapatsa vinyo n’kuwauza kuti akuimira ‘magazi ake apangano.’ (Maliko 14:22-25; Luka 22:20; 1 Akor. 11:24) Zimene ananenazitu n’zofunika kwambiri. Pangano latsopanoli silikukhudza anthu onse koma ndi lapakati pa iyeyo ndi “nyumba [yauzimu] ya Isiraeli,” yomwe ndi anthu amene adzalamulire naye “mu Ufumu wa Mulungu.” (Aheb. 8:6, 10; 9:15) Pa nthawiyo atumwiwo sanamvetse zimenezi, koma pambuyo pake iwo anadzozedwa ndi mzimu woyera ndipo analowa m’pangano latsopano kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba.​—Yoh. 14:2, 3.

10. Kodi zimene Yesu analankhula ku Galileya zikusiyana bwanji ndi zimene analankhula pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye? (Onaninso chithunzi.)

10 Dziwani kuti pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, Yesu ankalankhula za “kagulu ka nkhosa.” Kagulu kameneka kanayamba ndi atumwi ake okhulupirika omwe analipo m’chipindamo. (Luka 12:32) Atumwiwo anadya mkate komanso kumwa vinyo ndipo anthu enanso omwe anali kudzalowa m’gululi ankayembekezeka kumadya zizindikirozi. Amenewa ndi amene adzalamulire naye kumwamba. Zimene Yesu anauza atumwi ake zikusiyana ndi zimene anauza gulu la anthu ku Galileya. Zimene analankhula ku Galileyako zinali zokhudza anthu ambiri.

Anthu ochepa ndi amene amadya mkate komanso kumwa vinyo koma “aliyense” akhoza kukhulupirira Yesu n’kudzapeza moyo wosatha (Onani ndime 10)


11. Kodi Yesu ananena zotani ku Galileya zomwe zimasonyeza kuti ankanena za anthu ambiri?

11 Pamene Yesu anali ku Galileya mu 32 C.E., ankalankhula ndi Ayuda omwe ankafuna kuti awapatse chakudya. Koma iye anawauza za zinthu zina zofunika kwambiri kuposa chakudya. Anawauza zinthu zomwe zingawathandize kudzapeza moyo wosatha. Yesu anawauza anthuwo kuti anthu omwe anamwalira adzaukitsidwa ndipo adzakhala ndi moyo wosatha. Apa sankanena za anthu ochepa ngati mmene anachitira pa nthawi ya Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Ku Galileya iye ankanena za madalitso amene anthu onse akhoza kupeza. Ndipotu iye ananena kuti: “Ngati wina atadya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha. . . . Chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.”​—Yoh. 6:51.

12. Kodi chofunika n’chiyani kuti anthu adzapeze madalitso amene Yesu ananena?

12 Kodi Yesu ankatanthauza kuti anthu onse omwe ali padzikoli komanso amene adzabadwe adzalandira madalitso amenewa? Ayi. Madalitsowa ndi a anthu amene ‘amadya chakudya chimenechi’ kapena kuti amene amasonyeza chikhulupiriro. Anthu ambiri omwe amati ndi Akhristu amaganiza kuti akhoza kupulumutsidwa chifukwa ‘chongokhulupirira [Yesu ]’ komanso kumuona kuti iye ndi mpulumutsi. (Yoh. 6:29) Komatu Ayuda ena omwe poyamba ankakhulupirira Yesu, anasiya kumutsatira. N’chifukwa chiyani anasiya kumutsatira?

13. Kodi munthu amafunika kuchita chiyani kuti akhale wophunzira wa Yesu weniweni?

13 Anthu ambiri omwe Yesu anawadyetsa, ankangomutsatira kuti apeze zimene akufuna. Iwo ankangosangalala ndi kuchiritsidwa, kudya chakudya chaulere komanso kuphunzitsidwa zinthu zogwirizana ndi maganizo awo. Koma Yesu anasonyeza kuti munthu ayenera kuchita zambiri kuti akhale wophunzira wake. Iye sanabwere padzikoli kuti azidzangopereka zimene anthu akufuna. Iwo ankafunika kuvomera pempho lakuti ‘bwerani kwa ine,’ potsatira zonse zimene ankaphunzitsa.​—Yoh. 5:40; 6:44.

14. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipindule ndi thupi ndi magazi a Yesu?

14 Polankhula ndi gululo Yesu anasonyeza kufunika kosonyeza chikhulupiriro. Munthu amafunika kukhulupirira kuti thupi ndi magazi a Yesu zili ndi mphamvu yotha kupulumutsa anthu kuti adzapeze moyo wosatha. Chikhulupiriro chimenechi chinali chofunika kwa Ayuda pa nthawiyo ndiponso kwa ifeyo masiku ano. (Yoh. 6:40) Kuti tipindule ndi thupi komanso magazi a Yesu, zotchulidwa pa Yohane 6:53, tiyenera kukhulupirira dipo. Mwayi umenewu waperekedwa kwa anthu ambiri.​—Aef. 1:7.

15-16. Kodi nkhani ya mu Yohane chaputala 6, imatikumbutsa za madalitso ati?

15 Nkhani yopezeka pa Yohane chaputala 6 ndi yofunika kwambiri kwa tonsefe. Imasonyeza kuti Yesu amakonda kwambiri anthu. Iye ali ku Galileya anachiritsa odwala, kuphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso kuwapatsa chakudya. (Luka 9:11; Yoh. 6:2, 11, 12) Koma chofunika kwambiri ndi chakuti anawaphunzitsa kuti iye ndi “chakudya chopatsa moyo.”​—Yoh. 6:35, 48.

16 Anthu a “nkhosa zina” sayenera kudya kapena kumwa vinyo pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (Yoh. 10:16) Ngakhale zili choncho iwo amapindula ndi thupi komanso magazi a Yesu Khristu. Iwo amadya chakudya chimenechi akamakhulupirira kuti nsembe ya Yesu ingawapulumutse. (Yoh. 6:53) Koma anthu omwe amadya mkate komanso kumwa vinyo amasonyeza kuti ali m’pangano latsopano ndipo adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Choncho kaya ndife odzozedwa kapena a nkhosa zina nkhani ya mu Yohane chaputala 6 ndi yofunika kwambiri kwa tonsefe. Imatsindika mfundo yakuti tiyenera kusonyeza chikhulupiriro kuti tikapeze moyo wosatha.

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

a Lemba la Yohane 6:5-35, linafotokozedwa munkhani yapita ija.

b Madzi amene Yesu anatchula amaimira zinthu zimene Yehova amatipatsa kuti tidzapeze moyo wosatha.