“Muziyamika pa Chilichonse”
KODI mumaona kuti ndinu munthu woyamikira? Limeneli ndi funso lofunika kuliganizira. Baibulo linaneneratu kuti masiku athuwa, anthu ambiri adzakhala “osayamika.” (2 Tim. 3:2) Mwina munaonapo anthu amene amangoyembekezera kuti anthu ena aziwachitira komanso kuwapatsa zinthu. Amaoneka kuti alibe mtima wofuna kuthokoza pa zimene amapatsidwa. Kodi mumasangalala kukhala ndi anthu otere?
Koma Baibulo limauza atumiki a Yehova kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” Limanenanso kuti: “Muziyamika pa chilichonse.” (Akol. 3:15; 1 Ates. 5:18) Ndipotu kukhala oyamikira kumatithandiza pa zinthu zambiri.
KUYAMIKIRA KUMATHANDIZA KUTI TIZIDZIONA MOYENERA
Mtima woyamikira ungatithandize kuti tizidziona moyenera. Munthu akayamikira mnzake amasangalala ndipo woyamikiridwayo nayenso amasangalala. N’chifukwa chiyani zimakhala chonchi? Taganizirani izi: Mukazindikira kuti anthu ena amafunitsitsa kukuchitirani zinthu zinazake, mumaona kuti anthuwo amakuwerengerani. Zimasonyezanso kuti anthuwo amakukondani. Ndiye mukazindikira zimenezi, mumaona kuti ndinu wofunika. N’zosakayikitsa kuti Rute anamva chonchi pamene Boazi anamuthandiza. Rute ayenera kuti anasangalala kuzindikira kuti pali munthu amene ankamuganizira.—Rute 2:10-13.
Tiyenera kuyamikira kwambiri Mulungu kuposa aliyense. N’zosachita kufunsa kuti mwaganizirapo mobwerezabwereza zinthu zambiri zimene Mulungu amapereka. (Deut. 8:17, 18; Mac. 14:17) Koma m’malo mongoganizira pang’ono zinthuzi, mungachite bwino kuganizira mozama madalitso onse amene Mulungu wakupatsani inuyo komanso anzanu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzimuyamikira. Kungakuthandizeninso kudziwa kuti amakukondani komanso kukuyamikirani.—1 Yoh. 4:9.
Tisamangoganizira zinthu zimene Yehova watipatsa, koma tizimuyamikiranso. (Sal. 100:4, 5) Anthu ena ananenapo kuti “kuyamikira kumathandiza anthu kuti akhale osangalala.”
KUYAMIKIRA KUMATHANDIZA KUTI ANTHU AZIGWIRIZANA
Kukhala oyamikira kumathandizanso kuti anthu azigwirizana. Aliyense amafuna kudziwa kuti anthu ena amamuyamikira. Mukayamikira munthu mochokera pansi pa mtima chifukwa cha zabwino zimene wakuchitirani, zimathandiza kuti awirinu muzigwirizana kwambiri. (Aroma 16:3, 4) Komanso anthu amene ali ndi mtima woyamikira amakonda kuthandiza anzawo. Amaganizira zinthu zabwino zimene ena anawachitira ndipo amafuna kuchitiranso ena zabwino. Kunena zoona, munthu amasangalala akathandiza ena. Paja Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Mac. 20:35.
Robert Emmons, yemwe akutsogolera kafukufuku wokhudza kuyamikira amene akuchitika kuyunivesite ya California, anati: “Kuti tikhale oyamikira, tiyenera kuzindikira kuti anthufe timadalirana. Nthawi zina ifeyo timapereka zinthu kwa ena ndipo nthawi zina anthuwo ndi amene amatipatsa zinthu.” Mfundo ndi yakuti anthufe timadalira zimene ena amatichitira kuti tikhale ndi moyo. Mwachitsanzo, akhoza kutipatsa chakudya kapena thandizo lakuchipatala. (1 Akor. 12:21) Munthu woyamikira amasonyeza kuti amasangalala ndi zimene ena amamuchitira. Ndiye kodi inuyo mumakonda kuyamikira zimene ena amakuchitirani?
KUYAMIKIRA KUMATHANDIZA KUTI TIZIONA ZINTHU MOYENERA
Kuyamikira kumatithandizanso kuganizira zinthu zabwino m’malo mwa zoipa. Maganizo anu amakhala ngati sefa. Tikutero chifukwa chakuti mumatha kuganizira zinthu zina n’kumapewa kuganizira zinthu zina. Mumatha kuika maganizo anu pa zabwino n’kumapewa kuganizira kwambiri mavuto. Mukakhala oyamikira mutha kuona zinthu zabwino ndipo zimenezi zidzakuthandizani kukhala oyamikira kwambiri. Kukhala ndi mtima woyamikira kungakuthandizeni kutsatira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye.”—Afil. 4:4.
Munthu woyamikira amapewa kumangoganizira zinthu zokhumudwitsa. N’zosatheka kuti munthu ayamikire zinthu zina nthawi imodzimodziyo akuchita nsanje, kukhumudwa kapena kukwiya. Anthu oyamikira amasangalala ndi zimene ali nazo ndipo samangokhalira kufuna zinthu zina.—Afil. 4:12.
MUZIGANIZIRA ZINTHU ZABWINO ZIMENE MULI NAZO
Akhristufe timadziwa kuti Satana amafuna kuti tizikhala okhumudwa chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawo m’masiku otsirizawa. Iye angasangalale ngati titamangoganizira zinthu zokhumudwitsa n’kumadandaula. Koma zimenezi zingachititse kuti anthu asamafune kumvetsera uthenga wathu tikamalalikira. Ndipotu mtima woyamikira umagwirizana ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Mwachitsanzo, kumagwirizana ndi kukhala wachimwemwe chifukwa cha zinthu zimene Mulungu watipatsa komanso kukhulupirira zimene anatilonjeza.—Agal. 5:22, 23.
Anthu a Yehovafe tingavomereze mfundo zokhudza kuyamikira zimene zili munkhaniyi. Koma tikudziwanso kuti kukhala oyamikira si kophweka. Ngakhale zili choncho, musadandaule chifukwa n’zotheka kukhala ndi mtima woyamikira. Kodi zingatheke bwanji? Tsiku lililonse muyenera kuganizira zinthu zina pa moyo wanu zimene mungayamikire. Mukamachita zimenezi mudzayamba kukhala ndi mtima woyamikira. Izi zingakuthandizeni kukhala osangalala kwambiri kuposa anthu amene amakonda kuganizira mavuto awo. Muziganizira zinthu zabwino zimene Mulungu ndiponso anthu ena amachita zomwe zimakusangalatsani. Mwina tsiku lililonse mungamalembe zinthu zabwino ziwiri kapena zitatu zimene mukuyamikira.
Asayansi ena anapeza kuti “ubongo wa munthu amene amayamikira pafupipafupi umasintha ndipo munthuyo amayamba kuganizira kwambiri zinthu zabwino zimene zikuchitika pa moyo wake.” Munthu woyamikira amakhala wosangalala. Choncho muziganizira zinthu zabwino zimene muli nazo, zimene zakuchitikirani ndipo muzikhala oyamikira. M’malo moona zinthu zabwino mopepuka, ‘muziyamikira Yehova chifukwa iye ndi wabwino.’ Tiyeni tiziyesetsa ‘kuyamikira pa chilichonse.’—1 Mbiri 16:34; 1 Ates. 5:18.