NKHANI YOPHUNZIRA 52
Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova
“Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.”—SAL. 127:3.
NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1. Kodi Yehova anapatsa makolo udindo wotani?
YEHOVA analenga anthu oyambirira m’njira yoti azifuna kubereka ana. Paja Baibulo limati: “Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Tiyerekeze kuti mnzanu wapamtima wakusungitsani ndalama zambiri. Kodi mungamve bwanji? N’zosachita kufunsa kuti mungaone kuti amakudalirani. Koma mwina mungamadere nkhawa za kasungidwe ka ndalamazo kuti zisabedwe. Yehova, yemwe ndi Mnzathu wapamtima, anapatsa makolo chinthu chamtengo wapatali kuposa ndalama kuti asamalire. Iye anawapatsa udindo woonetsetsa kuti ana awo akusamaliridwa bwino komanso akusangalala.
2. Kodi tikambirana mafunso ati?
2 Kodi ndi ndani amene ayenera kusankha ngati banja likufunika kubereka ana komanso nthawi yobereka anawo? Nanga kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale osangalala? Tiyeni tione mfundo zina za m’Mawu a Mulungu zimene zingathandize mabanja kusankha zochita mwanzeru.
TIZILEMEKEZA ZIMENE ANTHU ASANKHA
3. (a) Kodi udindo wosankha kuti banja likhale ndi ana kapena ayi ndi wa ndani? (b) Kodi achibale kapena anzawo a anthu a pa banja ayenera kukumbukira mfundo iti ya m’Baibulo?
3 M’zikhalidwe zina, anthu ambiri amaona kuti anthu amene akwatirana kumene ayenera kuyamba msanga kubereka ana. Anthu a pa banjawo akhoza kukakamizidwa ndi achibale kapena anthu ena kuti abereke msanga. M’bale wina Agal. 6:5) N’zoona kuti achibale komanso anzawo a anthu amene akwatirana kumene angafune kuti banja latsopanolo lizisangalala. Koma onse ayenera kukumbukira kuti banjalo ndi limene liyenera kusankha kubereka ana kapena ayi.—1 Ates. 4:11.
wa ku Asia dzina lake Jethro anati: “Anthu ena mumpingo amene ali ndi ana amakakamiza mabanja ena kuti nawonso abereke.” M’bale winanso wa ku Asia dzina lake Jeffrey ananena kuti: “Anthu ena amauza mabanja amene alibe ana kuti adzasowa owasamalira akadzakalamba.” Koma ndi udindo wa banja lililonse kusankha kuti likhale ndi ana kapena ayi. (4-5. Kodi anthu ayenera kukambirana mafunso awiri ati, nanga angachite bwino kukambirana pa nthawi iti? Fotokozani.
4 Banja limene lasankha kuti libereke ana lingachite bwino kukambirana mafunso awiri ofunika awa: (1) Kodi tikufuna kuyamba liti kubereka ana? (2) Kodi tikhale ndi ana angati? Koma kodi ayenera kukambirana mafunsowa pa nthawi iti? Nanga mafunso amenewa ndi ofunika bwanji?
5 Nthawi zambiri, anthu angachite bwino kukambirana mafunsowa asanakwatirane. Zili choncho chifukwa kukhala ndi maganizo ofanana pa nkhaniyi ndi kofunika kwambiri. Komanso ayenera kuona ngati akonzeka kukhala ndi udindo umenewu. Anthu ena amasankha kuti adikire kaye chaka chimodzi kapena ziwiri asanakhale ndi ana podziwa kuti kulera ana kumafuna nthawi ndiponso mphamvu zambiri. Choncho amaona kuti akadikira adzakhala ndi nthawi yozolowera moyo wa m’banja n’kuyamba kugwirizana kwambiri.—Aef. 5:33.
6. Kodi mabanja ena asankha zotani chifukwa choti tikukhala mu nthawi yovuta?
6 Akhristu ena amasankha zotsatira chitsanzo cha ana a Nowa ndi akazi awo. Mabanja atatuwa anadikira kaye asanakhale ndi ana. (Gen. 6:18; 9:18, 19; 10:1; 2 Pet. 2:5) Yesu ananena kuti nthawi yathu ikufanana ndi “masiku a Nowa” ndipo n’zosachita kufunsa kuti tikukhala “masiku otsiriza” komanso ‘nthawi yovuta.’ (Mat. 24:37; 2 Tim. 3:1) Chifukwa cha zimenezi, mabanja ena asankha kuti asakhale ndi ana panopa n’cholinga choti azichita zambiri mu utumiki.
7. Kodi mfundo za pa Luka 14:28, 29 ndi Miyambo 21:5 zingathandize bwanji anthu?
7 Anthu anzeru ‘amawerengera’ zimene zingafunike asanasankhe kukhala ndi ana Luka 14:28, 29.) Makolo amavomereza kuti kulera ana kumafuna ndalama zambiri, nthawi ndiponso mphamvu. Choncho anthu ayenera kuganizira mafunso ngati awa: ‘Kodi tonsefe tingafunike kugwira ntchito kuti tizipezera banja lathu zofunika pa moyo? Nanga tonsefe tili ndi maganizo ofanana pa nkhani yoti zofunika pa moyo ndi ziti? Ngati tonsefe tingafunike kugwira ntchito, kodi ndi ndani azidzasamalira ana athu? Nanga tingafune kuti ana athu atengere maganizo ndi zochita za ndani?’ Anthu amene amakambirana mafunsowa modekha amatsatira mfundo ya pa Miyambo 21:5.—Werengani.
komanso kuchuluka kwa ana amene angakhale nawo. (Werengani8. Kodi mabanja ayenera kuganizira mavuto ati, nanga mwamuna wachikondi amachita zotani?
8 Kuti mwana akule bwino, kholo lililonse limafunika kugwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zambiri pomusamalira. Choncho ngati makolo angabereke ana ambiri motsatizana, angavutike kusamalira mwana aliyense mokwanira. Mabanja amene anabereka ana ambiri motsatizana anavomereza kuti ankapanikizika. Mayi akhoza kutopa kwambiri ndipo izi zingachititse kuti asamakwanitse kuphunzira, kupemphera ndiponso kulalikira mokwanira. Komanso zingamuvute kuti azimvetsera kumisonkhano. Mwamuna wachikondi amayesetsa kuthandiza mkazi wake kusamalira ana kumisonkhano komanso kunyumba. Mwachitsanzo, akhoza kuthandiza mkazi wake ntchito zapakhomo. Bamboyo ayenera kuonetsetsa kuti akuchita kulambira kwa pabanja m’njira yothandiza banja lonse. Ayeneranso kulowa mu utumiki ndi banja lake pafupipafupi.
KODI MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKONDA YEHOVA?
9-10. Kodi makolo amene akufuna kuthandiza ana awo ayenera kuchita chiyani?
9 Kodi ndi zinthu ziti zimene makolo angachite pothandiza ana awo kuti azikonda Yehova? Nanga angawateteze bwanji kuti asatengere makhalidwe oipa am’dzikoli? Tiyeni tikambirane zimene makolo angachite.
10 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi makolo a Samisoni. Manowa atazindikira kuti iyeyo ndi mkazi wake adzakhala ndi mwana, anapempha Yehova kuti amupatse malangizo olerera mwanayo.
11. Malinga ndi Oweruza 13:8, kodi makolo angatsatire bwanji chitsanzo cha Manowa?
11 Nihad ndi Alma, a ku Bosnia ndi Herzegovina, anaphunzira pa chitsanzo cha Manowa. Iwo ananena kuti: “Mofanana ndi Manowa, tinapempha Yehova kuti atipatse Oweruza 13:8.
malangizo olerera bwino ana athu. Ndipo Yehova anayankha mapemphero athu pogwiritsa ntchito Malemba, mabuku a gulu, misonkhano yampingo komanso ikuluikulu.”—Werengani12. Kodi Yosefe ndi Mariya anapereka chitsanzo chotani kwa ana awo?
12 Muzipereka chitsanzo chabwino. Zimene mungauze ana anu zimakhala zofunika, koma zochita zanu n’zimene zimakhala zofunika kwambiri. N’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi Mariya ankapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana awo, kuphatikizapo Yesu. Yosefe ankagwira ntchito mwakhama kuti azisamalira banja lake. Ndipo ankalimbikitsanso anthu a m’banja lake kuti azikonda zinthu zauzimu. (Deut. 4:9, 10) Yosefe ankapita ndi banja lake ku Yerusalemu “chaka ndi chaka” kukachita mwambo wa Pasika ngakhale kuti Chilamulo sichinkanena kuti munthu azipita ndi banja lake. (Luka 2:41, 42) Amuna ena a pa nthawiyo mwina ankaona kuti ulendowu unali wotopetsa, wautali komanso wowonongetsa ndalama zambiri. Koma n’zoonekeratu kuti Yosefe ankakonda zinthu zauzimu ndipo anaphunzitsa ana ake kuti azichitanso zomwezo. Nayenso Mariya ankadziwa bwino Malemba. Choncho mawu ndi zochita zake ziyenera kuti zinathandiza ana ake kuti azikonda Malemba.
13. Kodi banja lina linatsatira bwanji chitsanzo cha Yosefe ndi Mariya?
13 Nihad ndi Alma, amene tawatchula kale aja, ankayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yosefe ndi Mariya. Kodi zimenezi zinawathandiza bwanji pophunzitsa mwana wawo kuti azikonda Mulungu komanso kumutumikira? Iwo anati: “Pa moyo wathu tinkayesetsa kusonyeza mwana wathu kuti kutsatira mfundo za Yehova n’kothandiza.” Nihad ananenanso kuti: “Muziyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mukufuna kuti mwana wanu akhale nawo.”
14. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kudziwa anthu amene ana awo amacheza nawo?
14 Muzithandiza ana anu kuti azicheza ndi anthu abwino. Mayi ndi bambo ayenera kudziwa anthu amene ana awo amacheza nawo komanso zimene amachita. Iwo ayeneranso kudziwa anthu amene ana awo amacheza nawo pa intaneti komanso pafoni. Zili choncho chifukwa ana anu akhoza kutengera maganizo ndi zochita za anthuwo.—1 Akor. 15:33.
15. Kodi makolo angaphunzire chiyani kwa Jessie?
15 Kodi makolo angatani ngati sadziwa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono? M’bale wina dzina lake Jessie, yemwe amakhala ku Philippines, ananena kuti: “Sitinkadziwa bwino kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Koma tinkathandizabe ana athu kudziwa mavuto amene angabwere ngati atazigwiritsa ntchito molakwika.” Jessie sanaletse ana ake kugwiritsa ntchito zipangizozi chifukwa choti iye sankazidziwa bwino. Iye anati: “Ndinkalimbikitsa ana anga kuti azigwiritsa ntchito zipangizozi kuti aphunzire chilankhulo china, azikonzekera misonkhano komanso aziwerenga Baibulo tsiku lililonse.” Ngati ndinu makolo, kodi mwawerenga komanso kukambirana ndi ana anu malangizo anzeru okhudza kutumizirana mameseji komanso kugawana zithunzi omwe akupezeka pa jw.org® pamene alemba kuti “Achinyamata”? Nanga kodi mwaonera nawo vidiyo yakuti Kodi Zipangizo Zanu Zamakono Zimakulamulirani? ndi yakuti Muzichita Zinthu Mosamala Mukamacheza ndi Anzanu pa Intaneti? * Zinthu zimenezi zingakuthandizeni pophunzitsa ana anu kuti azigwiritsa ntchito mwanzeru zipangizo zamakono.—Miy. 13:20.
16. Kodi makolo ambiri anachita zotani, nanga zinathandiza bwanji ana awo?
16 Makolo ambiri amayesetsa kuthandiza ana awo kuti azicheza ndi anthu amene amapereka chitsanzo chabwino potumikira Mulungu. Mwachitsanzo, N’Déni ndi Bomine, amene amakhala ku Côte d’Ivoire, ankakonda kuitana woyang’anira dera kuti azifikira kunyumba kwawo. N’Déni ananena kuti: “Zimenezi zinathandiza kwambiri mwana wathu moti iye anayamba upainiya ndipo panopa ndi woyang’anira dera wogwirizira.” Kodi nanunso mungakonze zoti ana anu azicheza ndi anthu abwino?
17-18. Kodi makolo ayenera kuyamba kuphunzitsa ana awo liti?
17 Muziyamba kuphunzitsa ana adakali aang’ono. Zinthu zimayenda bwino makolo akayamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono. (Miy. 22:6) Chitsanzo ndi Timoteyo, amene ankayenda ndi mtumwi Paulo. Mayi ake a Timoteyo dzina lawo a Yunike ndi agogo ake dzina lawo a Loisi ankamuphunzitsa kuyambira ali “wakhanda.”—2 Tim. 1:5; 3:15.
18 M’bale wina dzina lake Jean-Claude ndi mkazi wake Peace, omwenso amakhala ku Côte d’Ivoire, anathandiza ana awo onse 6 kuti azikonda Yehova komanso kumutumikira. Kodi n’chiyani chinawathandiza? Iwo anatsatira chitsanzo cha Yunike ndi Loisi. Banjali linati: “Tinayamba kukhomereza Mawu a Mulungu mwa ana athu pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anabadwa.”—Deut. 6:6, 7.
19. Kodi kukhomereza Mawu a Mulungu mwa ana n’kutani?
19 Kodi mawu akuti “kukhomereza” Mawu a Mulungu mwa ana amatanthauza chiyani? “Kukhomereza” kumatanthauza “kuphunzitsa ndi kukumbutsa mobwerezabwereza.” Kuti zimenezi zitheke, makolo ayenera kukhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi ana awo. Nthawi zina, kulangiza ana mobwerezabwereza kungaoneke kotopetsa. Komabe makolo ayenera kuona kuti imeneyi ndi njira yothandizira ana awo kumvetsa Mawu a Mulungu komanso kuwagwiritsa ntchito.
20. Kodi lemba la Salimo 127:4 likugwirizana bwanji ndi kulera ana?
Salimo 127 limayerekezera ana ndi mivi. (Werengani Salimo 127:4.) Mofanana ndi mivi imene imapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana komanso imasiyana kukula kwake, ananso amakhala osiyana. Choncho makolo ayenera kudziwa mmene angaphunzitsire mwana aliyense. Banja lina la ku Israel lomwe linalera bwino ana awo awiri kuti azitumikira Yehova linafotokoza zimene zinawathandiza. Iwo anati: “Tinkaphunzira ndi mwana aliyense payekha.” Munthu aliyense amene ndi mutu wa banja angasankhe ngati zimenezi zingathandize.
20 Muzidziwa bwino ana anu. Lemba laYEHOVA ADZAKUTHANDIZANI
21. Kodi Yehova amathandiza bwanji makolo?
21 N’zoona kuti nthawi zina makolo angaone kuti kulera ana n’kovuta. Koma azikumbukira kuti ana ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo iye angawathandize nthawi iliyonse. Yehova amamvetsera mapemphero a makolo. Ndipo amayankha mapempherowo pogwiritsa ntchito Baibulo, mabuku athu komanso zitsanzo ndi malangizo a makolo ena amumpingo.
22. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene makolo angapatse ana awo?
22 Anthu ena amanena kuti kulera ana kumatenga zaka 20 koma zoona zake n’zakuti makolo amakhalabe makolo. Zinthu zina zabwino kwambiri zimene makolo angapatse ana ndi chikondi chawo, nthawi yawo komanso kuwaphunzitsa mfundo za m’Baibulo. Mwana aliyense angatsatire malangizo mosiyana ndi mnzake. Koma ana ambiri amene analeredwa ndi makolo amene amakonda Yehova amagwirizana ndi maganizo a mlongo wina wa ku Asia dzina lake Joanna Mae. Iye anati: “Ndikaganizira mmene makolo anga anandiphunzitsira, ndimayamikira kwambiri. Ankandilangiza komanso kundiphunzitsa kukonda Yehova. Sikuti anangondipatsa moyo basi koma anandithandiza kuti ndizisangalala ndi moyowo.” (Miy. 23:24, 25) Akhristu ambiri akhoza kugwirizana ndi maganizo amenewa.
NYIMBO NA. 59 Tamandani Ya Limodzi ndi Ine
^ ndime 5 Kodi anthu a pa banja ayenera kubereka ana? Ngati angasankhe kubereka, kodi ayenera kukhala ndi ana angati? Nanga kodi angaphunzitse bwanji anawo kuti azikonda komanso kutumikira Yehova? Munkhaniyi tikambirana zitsanzo za masiku ano komanso mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuyankha mafunso amenewa.
^ ndime 15 Onaninso Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba, mutu 36 ndi Buku Lachiwiri, mutu 11.
^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja likukambirana ngati likufuna kudzakhala ndi ana ndipo likuganizira ubwino ndi mavuto ake.
^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja likuphunzira ndi mwana aliyense payekha chifukwa choti ana awo ndi osiyana msinkhu komanso luso.