Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi Akhristu angagwiritse ntchito lupu (IUD) ngati njira ya kulera?
Banja lililonse liyenera kusankha lokha pa nkhani imeneyi kuti likhale ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu. Kuti mabanja achite zimenezi, ayenera kuganizira zimene Baibulo limanena komanso mmene njirayi imagwirira ntchito.
Yehova analamula Adamu ndi Hava komanso Nowa ndi banja lake kuti: “Muberekane, muchuluke.” (Gen. 1:28; 9:1) Iye anachita zimenezi chifukwa choti pa nthawiyo anthu anali ochepa kwambiri. Koma Baibulo silinena kuti Akhristu ayenera kutsatirabe lamuloli. Choncho banja lililonse liyenera kusankha ngati likufuna kugwiritsa ntchito njira za kulera. Kodi mabanja ayenera kuganizira mfundo ziti posankha zochita pa nkhaniyi?
Akhristu ayenera kuganizira ngati njira za kulera zimene akufuna kugwiritsa ntchito n’zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. N’chifukwa chake Akhristu sachotsa mimba pofuna kuti asakhale ndi mwana. Kuchita zimenezi kumasemphana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani yolemekeza moyo. Akhristu sangasankhe kuchotsa mimba chifukwa kumakhala kupha munthu wosabadwa. (Eks. 20:13; 21:22, 23; Sal. 139:16; Yer. 1:5) Ndiye kodi tinganene zotani pa nkhani ya lupu?
Nkhani imeneyi inafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 15, 1979, patsamba 30 ndi 31. Malupu amene ankagwiritsidwa ntchito pa nthawiyo ankakhala apulasitiki ndipo ankaikidwa m’chiberekero kuti mayi asatenge pakati. Nkhaniyo inanena kuti sizidziwika bwinobwino mmene malupuwo amagwirira ntchito. Akatswiri ambiri ananena kuti malupuwo ankachititsa kuti mbewu ya abambo isakumane ndi dzira la amayi. Izi zinkathandiza kuti mwana asayambe kupangika.
Koma zikuoneka kuti nthawi zina mbewu ya abambo inkakumana ndi dzira la amayi. Ndiyeno mwana ankayamba kupangika m’njira yodutsa mazira kapena m’chiberekero. Izi zikachitikira m’chiberekero, lupuyo inkachititsa kuti mimba isapitirire kukula. Apa zinkakhala ngati mimba yachotsedwa. Magaziniyo inamaliza kuti: “Akhristu amene akufuna kugwiritsa ntchito lupu ayenera kuganizira mosamala kwambiri mfundo zimenezi komanso zimene Baibulo limanena pa nkhani yolemekeza moyo.”—Kodi pali zilizonse zimene zasintha pa nkhani ya sayansi kapena zachipatala kuchokera pamene magaziniyi inatuluka mu 1979?
Masiku ano pali malupu a mitundu iwiri. Mtundu woyamba ndi wokhala ndi mkuwa ndipo unayamba kupezeka kwambiri ku United States pofika mu 1988. Mtundu wina ndi wa mahomoni ndipo unayamba kupezeka mu 2001. Kodi malupu amenewa amagwira ntchito bwanji?
Malupu okhala ndi mkuwa: Monga tanena kale, malupu amachititsa kuti mbewu ya abambo isakumane ndi dzira la amayi. Zikuonekanso kuti mkuwawo umachititsa kuti mbewuyo ithe mphamvu. * Akuti malupu amenewa amasinthanso zinthu zina m’chiberekero kuti mimba isamakuliremo.
Malupu a mahomoni: Pali malupu ena amene amakhala ndi mahomoni ofanana ndi amene amapezeka m’mapilisi a kulera. Malupuwa amagwira ntchito ngati malupu akale aja, kungoti amatulutsanso mahomoni m’chiberekero omwe amachititsa kuti mazira a akazi ena asamakhwime. Choncho n’zosatheka kuti mbewu ikumane ndi mazira chifukwa mazirawo amakhala asanakhwime. Komanso amati mahomoniwo amasintha zinthu zina m’chiberekero kuti mimba isamakuliremo. * Malupuwa amapangitsanso kuti timadzi timene timakhala pakhomo la chiberekero tikhale toundana ndipo zimenezi zimalepheretsa kuti mbewu ya abambo ifike m’chiberekero.
Monga tanena kale, malupu onse amasintha zinthu zina m’chiberekero kuti mimba isamakuliremo. Ndiye kodi chingachitike n’chiyani ngati mbewu ya abambo yakumana ndi dzira la amayi? Mwina dziralo likhoza kufika m’chiberekero koma mimbayo singakule. Izi zingachititse kuti mimba imene yangoyamba kumene ichoke. Koma asayansi amati zimenezi zimangochitika mwa kamodzikamodzi ngati mmene zililinso ndi mapilisi a kulera.
Choncho palibe amene anganene motsimikiza kuti munthu amene amagwiritsa ntchito malupu okhala ndi mkuwa kapena mahomoni sangatenge pakati. Komabe malinga ndi zimene takambiranazi, pali umboni wakuti zimakhala zovuta kuti munthu amene akugwiritsa ntchito malupuwa atenge pakati.
Choncho banja limene likuganiza zogwiritsa ntchito lupu liyenera kukambirana ndi akuchipatala kuti adziwe mtundu wa malupu amene akupezeka kudera lawo komanso mmene angakhudzire mkaziyo. Si bwino kulola munthu wina, ngakhale dokotala, kuti awasankhire zochita pa nkhaniyi. (Aroma 14:12; Agal. 6:4, 5) Nkhaniyi ndi yoti banja lililonse lizisankha lokha zimene likuona kuti zingasangalatse Mulungu komanso zingawathandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino.—Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 1:18, 19; 2 Timoteyo 1:3.
^ ndime 4 Bungwe loona zaumoyo ku England linanena kuti: “Malupu okhala ndi mkuwa wambiri amathandiza kwambiri kuti mayi asatenge pakati moti pa akazi 100 amene amagwiritsa ntchito malupuwa pachaka, mmodzi yekha ndi amene angatenge pakati ndipo mwina palibenso amene angatenge. Koma malupu amene amakhala ndi mkuwa wochepa, mphamvu yake imakhalanso yocheperapo.”
^ ndime 5 Madokotala ena amauza akazi amene amataya magazi ambiri pa nthawi yosamba kuti azigwiritsanso ntchito malupu amenewa chifukwa amathandiza kuti asamataye magazi ambiri. Amanena zimenezi kwa akazi a pa banja ngakhalenso amene sali pa banja.