Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 17

Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Amtengo Wapatali

Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Amtengo Wapatali

“Yehova amasangalala ndi anthu ake.”​—SAL. 149:4.

NYIMBO NA. 108 Chikondi Chosatha cha Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Atate wathu wakumwamba “amasangalala” ndi aliyense wa ife (Onani ndime 1)

1. Kodi Yehova amaona chiyani mwa anthu ake?

YEHOVA MULUNGU “amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Imeneyitu ndi mfundo yosangalatsa kwambiri. Yehova amaona makhalidwe athu abwino, amadziwa zimene tingakwanitse kuchita komanso amatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Tikapitiriza kukhala okhulupirika, iyenso adzapitiriza kukhala nafe pa ubwenzi mpaka kalekale.​—Yoh. 6:44.

2. N’chifukwa chiyani ena zimawavuta kukhulupirira kuti Yehova amawakonda?

2 Ena anganene kuti, ‘Ndimadziwa kuti Yehova amakonda anthu ake monga gulu, koma kodi ndingatsimikize bwanji kuti ineyo amandikonda pandekha?’ N’chiyani chingachititse kuti munthu afunse funso limeneli? Oksana, * yemwe anakumana ndi mavuto ambiri ali mwana ananena kuti: “Ndinasangalala kwambiri nditabatizidwa komanso nditayamba upainiya. Koma patatha zaka 15, ndinayamba kukumbukira zinthu zoipa zimene zinandichitikira ndili mwana. Ndinkaganiza kuti Yehova sakusangalala nane ndipo wasiya kundikonda. Mpainiya wina dzina lake Yua, yemwe nayenso ali mwana anakumana ndi mavuto ambiri anati: “Ndinadzipereka kwa Yehova chifukwa ndinkafuna kuchita zinthu zimene zimamusangalatsa. Koma ndinkakhulupirira kuti iye sangandikonde.”

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Mofanana ndi Akhristu okhulupirika tangowatchulawa, n’kutheka kuti inunso mumakonda kwambiri Yehova, koma mwina mungamakayikire kuti iye amakukondani. N’chifukwa chiyani muyenera kutsimikizira kuti iye amakukondani kwambiri? Nanga n’chiyani chingakuthandizeni mukayamba kukhala ndi maganizo oti sakukondani? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.

KUKAYIKIRA KUTI YEHOVA AMAKUKONDANI N’KOOPSA

4. N’chifukwa chiyani kukayikira kuti Yehova amatikonda n’koopsa?

4 Chikondi ndi champhamvu kwambiri. Tikakhala kuti sitikukayikira kuti Yehova amatikonda timafunitsitsa kumutumikira ndi mtima wonse ngakhale tikumane ndi mavuto. Koma tikayamba kukayikira, ‘mphamvu zathu zimakhala zochepa.’ (Miy. 24:10) Ndipo tikafooka n’kusiya kukhulupirira kuti Mulungu amatikonda, Satana angatigonjetse mosavuta.​—Aef. 6:16.

5. Kodi n’chiyani chinachitikira Akhristu ena omwe ankakaikira kuti Mulungu amawakonda?

5 Akhristu ena okhulupirika, chikhulupiriro chawo chafooka chifukwa chokayikira kuti Yehova amawakonda. Mkulu wina dzina lake James anati: “Ngakhale kuti ndinkatumikira pa Beteli ndipo ndinkalalikira ndi mpingo wachinenero china, ndinkakayikira kuti Yehova amasangalala ndi zimene ndimachita pomutumikira. Moti nthawi ina, ndinafika pokayikira kuti Yehova amamva mapemphero anga.” Eva, yemwe nayenso ali mu utumiki wa nthawi zonse anati: “Ndimaona kuti kukayikira kuti Yehova amakukonda n’koopsa chifukwa kumakhudza zonse zimene umachita pomutumikira. Zimenezi zimachititsa kuti usiye kukonda zinthu zokhudza kulambira komanso kuti usamasangalale potumikira Yehova.” Michael, yemwe ndi mpainiya wokhazikika komanso mkulu anati: “Ukamakayikira kuti Mulungu amakukonda umayamba kutengeka pang’onopang’ono, n’kusiyana naye.”

6. Kodi tingatani ngati tayamba kukhala ndi maganizo oti Mulungu satikonda?

6 Zimene zinachitikira Akhristuwa, zikusonyeza kuti kukhala ndi maganizo oti Mulungu satikonda kungawononge kwambiri chikhulupiriro chathu. Koma kodi tingatani ngati tayamba kukhala ndi maganizo amenewa? Tiyenera kuwachotsa mwamsanga. Tizipempha Yehova kuti atithandize kuchotsa ‘malingaliro amene akutisowetsa mtendere,’ n’kutipatsa ‘mtendere umene udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu.’ (Sal. 139:23; Afil. 4:6, 7) Komanso muzikumbukira kuti simuli nokha. Palinso abale ndi alongo ena amene akuvutika ndi maganizo oipa akuti Mulungu sawakonda. Ngakhalenso atumiki ena a Yehova m’mbuyomu anavutikapo ndi maganizo amenewa. Tiyeni tione zimene tikuphunzira pa chitsanzo cha mtumwi Paulo.

KODI TINGAPHUNZIRE CHIYANI PA ZIMENE ZINACHITIKIRA PAULO?

7. Kodi Paulo ankakumana ndi mavuto otani?

7 Kodi nthawi zina mumapanikizika n’kumaona kuti pali zambiri zoti muchite koma simungakwanitse kuzichita? Ngati zili choncho ndiye kuti mungamvetse mmene Paulo ankamvera. Iye ankadera nkhawa osati mpingo umodzi wokha koma “mipingo yonse.” (2 Akor. 11:23-28) Kodi mukudwala matenda aakulu omwe nthawi zambiri amakuchititsani kukhala wosasangalala? Paulo ankalimbana ndi “munga m’thupi.” N’kutheka kuti mwina panali matenda enaake amene ankadwala ndipo ankafunitsitsa matendawo atatha. (2 Akor. 12:7-10) Kodi nthawi zina mumafooka chifukwa cha zinthu zimene mumalakwitsa? Nthawi zinanso Paulo ankamva choncho. Iye anafika ponena kuti “munthu wovutika ine,” chifukwa nthawi zambiri ankakhala pa nkhondo yofuna kuyesetsa kuti azichita zabwino.​—Aroma 7:21-24.

8. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti athe kupirira mavuto amene ankakumana nawo?

8 Ngakhale kuti ankakumana ndi mayesero komanso zinthu zambiri zofooketsa, Paulo anapitirizabe kutumikira Yehova. Kodi n’chiyani chinam’patsa mphamvu? Iye ankadziwa kuti si wangwiro ndipo ankakhulupirira kwambiri kuti nsembe ya dipo ingamuthandize. Ankadziwanso bwino zimene Yesu analonjeza kuti “aliyense wokhulupirira mwa iye [Yesu]. .  akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16; Aroma 6:23) Mwachionekere, Paulo anali mmodzi mwa anthu amene ankakhulupirira kwambiri dipo. Iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova ndiwokonzeka kukhululukira anthu amene achita machimo akuluakulu koma alapa.​—Sal. 86:5.

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Paulo a pa Agalatiya 2:20?

9 Paulo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu amamukonda ndipo anatumiza Khristu kuti adzamufere. (Werengani Agalatiya 2:20.) Taonani mawu olimbikitsa amene ali kumapeto kwa vesili. Paulo anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” Onani kuti Paulo sanaone kuti chikondi cha Mulungu chili ndi malire. Iye sananene kuti, ‘Ndikuona kuti Yehova akhoza kumakonda abale anga, koma ineyo sangandikonde.’ Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Roma kuti: “Moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Choncho chikondi cha Mulungu chilibe malire.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa Aroma 8:38, 39?

10 Werengani Aroma 8:38, 39. Paulo ankakhulupirira kwambiri kuti Mulungu amamukonda. Iye analemba kuti palibe ‘chidzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu.’ Ankadziwa kuti Yehova anachita zinthu moleza mtima ndi mtundu wa Aisiraeli, komanso kuti anamuchitira iyeyo chifundo. Ndiye m’mawu ena tingati Paulo ankati, ‘Popeza Yehova anatumiza Mwana wake kuti adzandifere, kodi ndili ndi zifukwa zilizonse zokayikirira kuti iye amandikonda?’​—Aroma 8:32.

Dziwani kuti kwa Mulungu chofunika kwambiri ndi zimene mungachite panopa komanso m’tsogolo, osati zimene munalakwitsa m’mbuyo (Onani ndime 11) *

11. Ngakhale kuti Paulo anachita machimo kuphatikizapo amene atchulidwa pa 1 Timoteyo 1:12-15, n’chifukwa chiyani anali wotsimikiza kuti Mulungu amamukonda?

11 Werengani 1 Timoteyo 1:12-15. N’kutheka kuti nthawi zina Paulo ankavutika maganizo ndi zinthu zimene anachita m’mbuyo. Iye anafika podzitchula kuti anali wochimwa “kwambiri,” ndipo izi n’zosadabwitsa. Chifukwa poyamba asanaphunzire choonadi, ankazunza mwankhanza Akhristu m’mizinda yosiyanasiyana, kuwatsekera m’ndende komanso kuvomereza nawo kuti ena aphedwe. (Mac. 26:10, 11) Ndipo taganizirani mmene akanamvera kukumana ndi Mkhristu wachinyamata amene iye anavomereza nawo kuti makolo ake aphedwe. Paulo ankadziimba mlandu kwambiri chifukwa cha zimene analakwitsa, koma ankadziwa kuti sangasinthe zinthu zimene zinachitika kale. Iye anavomereza kuti Khristu anamufera, ndipo motsimikiza analemba kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:3, 10) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Muzivomereza kuti Khristu anafera inuyo ndipo zimenezi zinapereka mwayi woti mukhalenso pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. (Mac. 3:19) Dziwani kuti kwa Mulungu chofunika kwambiri ndi zimene mungachite panopa komanso m’tsogolo, osati zimene munalakwitsa m’mbuyo, kaya pa nthawiyo munali wa Mboni za Yehova kapena ayi.​—Yes. 1:18.

12. Kodi mawu a pa 1 Yohane 3:19, 20, angatithandize bwanji tikamaona kuti ndife opanda pake komanso sitimakondedwa?

12 Mwina mukaganizira kuti Yesu anafa chifukwa cha machimo anu munganene kuti, ‘Koma ine sindikuyenera kulandira mphatso yamtengo wapatali imeneyi.’ N’chifukwa chiyani nthawi zina mukhoza kumva choncho? Popeza kuti si ife angwiro mtima wathu ukhoza kutinamiza n’kumaona ngati ndife opanda pake komanso sitimakondedwa. (Werengani 1 Yohane 3:19, 20.) Tikayamba kukhala ndi maganizo amenewa tizikumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” Ngakhale titamaganiza kuti Yehova samatikonda ndiponso sangatikhululukire tiyenera kukhala otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda kwambiri ndipo amatikhululukira. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tiziwerenga Mawu ake pafupipafupi, tizipemphera mobwerezabwereza komanso nthawi zonse tizicheza ndi anthu amene amamulambira. Koma kodi n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika kwambiri?

MMENE KUPHUNZIRA BAIBULO, KUPEMPHERA KOMANSO KUCHEZA NDI ANZATHU OLAMBIRA YEHOVA KUNGATITHANDIZIRE

13. Kodi kuphunzira Mawu a Mulungu kumatithandiza bwanji? (Onaninso bokosi lakuti, “ Mmene Mawu a Mulungu Amawathandizira.”)

13 Muziwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Mukatero mudzayamba kumvetsa bwino kwambiri makhalidwe amene Yehova ali nawo ndipo mudzamvetsa mmene amakukonderani. Kuganizira mozama zimene mwawerenga m’Mawu a Mulungu tsiku lililonse kungakuthandizeni kuti muziganiza bwino, kapena kuti “kuwongola zinthu” m’maganizo ndi mumtima mwanu. (2 Tim. 3:16) Mkulu wina dzina lake Kevin, yemwe ankavutika ndi maganizo odziona kuti ndi wosafunika ananena kuti: “Kuwerenga komanso kuganizira mozama zimene zili mu Salimo 103, kwandithandiza kuti ndiyambenso kuganiza bwino komanso kudziwa mmene Yehova amandionera.” Eva, yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Tsiku likamatha, ndimayesetsa kupeza nthawi yoganizira zimene Yehova amaziona kuti ndi zofunika kwambiri. Zimenezi zimandithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima komanso kulimbitsa chikhulupiriro changa.”

14. Kodi pemphero lingatithandize bwanji?

14 Muzipemphera nthawi zonse. (1 Ates. 5:17) Kuti anthu azigwirizana kwambiri amafunika azilankhulana nthawi zonse komanso momasuka. Zimenezi ndi zofanananso kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Tikamamufotokozera m’pemphero mmene tikumvera, maganizo athu komanso zimene zikutidetsa nkhawa, timasonyeza kuti timamudalira ndipo timadziwa kuti amatikonda. (Sal. 94:17-19; 1 Yoh. 5:14, 15) Yua, amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Ndikamapemphera si kuti ndimangomufotokozera Yehova zimene ndachita kapena zimene zachitika pa tsikulo. M’malomwake ndimamasuka n’kumufotokozera maganizo anga komanso mmene ndikumvera. Pang’ono ndi pang’ono ndayamba kumuona Yehova osati ngati bwana wa pakampani koma monga Bambo amene amakonda kwambiri ana ake.​—Onani bokosi lakuti, “ Kodi Mwaliwerengapo?

15. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatiganizira?

15 Muzicheza ndi atumiki okhulupirika a Yehova chifukwa iwo ndi mphatso yochokera kwa iye. (Yak. 1:17) Atate wathu wakumwamba amasonyeza kuti amatiganizira potipatsa abale ndi alongo mumpingo omwe ‘amatikonda nthawi zonse.’ (Miy. 17:17) M’kalata imene analembera Akolose, Paulo anatchula za Akhristu ena omwe ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Ngakhalenso Khristu Yesu ankafunikira kuti ena amuthandize, ndipo anayamikira kwambiri anzake omwe anamuthandiza kuphatikizapo angelo.​—Luka 22:28, 43.

16. Kodi anzathu a mumpingo angatithandize bwanji kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

16 Kodi mumalola kuti abale ndi alongo anu omwe Yehova anakupatsani ngati mphatso azikuthandizani? Kufotokoza nkhawa zathu kwa anzathu amene amakonda Yehova sikutanthauza kuti ndife ofooka, m’malomwake kumatiteteza. Taonani zimene James, yemwe tamutchula kale uja ananena. Iye anati: “Kukhala ndi anzanga amene amakonda Yehova kwandithandiza kwambiri. Ndikayamba kukhala ndi maganizo akuti Yehova sandikonda, anzangawo amandimvetsera moleza mtima komanso kundikumbutsa kuti iwo amandikonda. Kudzera mwa iwowa ndimatha kuona kuti Yehova amandikonda komanso amandisamalira.” Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizilimbitsa ubwenzi wathu ndi abale ndi alongo athu.

ZIMENE MUYENERA KUCHITA KUTI YEHOVA APITIRIZE KUKUKONDANI

17-18. Kodi tiyenera kumvera ndani, nanga n’chifukwa chiyani?

17 Satana amafuna kuti tigonje pa nkhondo yathu yoyesetsa kuchita zabwino. Iye amafuna tizikhulupirira kuti Yehova satikonda komanso kuti si ife oyenera kumutumikira. Koma monga mmene taonera, zimenezi si zoona.

18 Yehova amakukondani kwambiri. Ndipo ndinu amtengo wapatali kwa iye. Mukamamumvera ‘mudzapitiriza kukhalabe m’chikondi chake’ mpaka kalekale ngati Yesu. (Yoh. 15:10) Choncho musamamvere Satana kapena mtima wanu womwe umakuchititsani kuona ngati Mulungu sakukondani. M’malomwake, muzimvera Yehova yemwe amaona zabwino mwa munthu aliyense. Musamakayikire kuti iye “amasangalala ndi anthu ake” kuphatikizapo inuyo.

NYIMBO NA. 141 Moyo Ndi Wodabwitsa

^ ndime 5 Abale ndi alongo ena zimawavuta kukhulupirira kuti Yehova amawakonda. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amatikonda aliyense payekha. Tikambirananso zimene tingachite ngati tayamba kukayikira kuti Mulungu amatikonda.

^ ndime 2 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Poyamba Paulo ankazunza Akhristu n’kumawatsekera m’ndende. Koma atavomereza mumtima mwake zimene Yesu anamuchitira, iye anasintha n’kuyamba kulimbikitsa abale ake a Chikhristu omwe ena mwa iwo anali achibale a anthu omwe anawazunza.