NKHANI YOPHUNZIRA 42
NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso
Muziyamikira Amuna Amene Yehova Watipatsa Mumpingo
“Atakwera pamalo apamwamba . . . , anapereka amuna kuti akhale mphatso.”—AEF. 4:8.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona mmene atumiki othandiza, akulu komanso oyang’anira madera amatithandizira. Tikambirananso zimene tingachite kuti tiziyamikira zimene amatichitira.
1. Kodi ndi mphatso ziti zimene Yesu watipatsa?
YESU ndi wowolowa manja kuposa munthu aliyense. Ali padziko lapansi anagwiritsa ntchito mphamvu zimene anali nazo pothandiza ena. (Luka 9:12-17) Iye anatipatsa mphatso yaikulu kwambiri potifera. (Yoh. 15:13) Yesu wakhala akutipatsanso zinthu zambiri kungochokera pamene anaukitsidwa n’kubwerera kumwamba. Iye analonjeza kuti adzapempha Atate wake kuti atipatse mzimu woyera kuti uzidzatiphunzitsa komanso kutilimbikitsa ndipo ndi zimene wachita. (Yoh. 14:16, 17, mawu a m’munsi; 16:13) Amatiphunzitsanso pa ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe ikuchitika padziko lonse pogwiritsa ntchito misonkhano yampingo.—Mat. 28:18-20.
2. Mogwirizana ndi Aefeso 4:7, 8, kodi ndi amuna ati omwe aperekedwa kuti akhale “mphatso”?
2 Palinso mphatso ina imene Yesu watipatsa. Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu atapita kumwamba, “anapereka amuna kuti akhale mphatso.” (Werengani Aefeso 4:7, 8.) Paulo anafotokoza kuti Yesu anapereka amuna amenewa kuti azithandiza mpingo. (Aef. 1:22, 23; 4:11-13) Masiku ano, “amuna” amenewa amatumikira monga atumiki othandiza, akulu komanso oyang’anira madera. a Amuna amenewa si angwiro, choncho amalakwitsa zinthu zina. (Yak. 3:2) Koma Ambuye wathu Yesu Khristu amawagwiritsabe ntchito kuti azitithandiza ndipo ali ngati mphatso zimene watipatsa.
3. Kodi tingathandize bwanji pa ntchito imene “amuna” amenewa amagwira?
3 Yesu anapereka “amuna” amenewa kuti azithandiza anthu mumpingo. (Aef. 4:12) Koma tonsefe tikhoza kuwathandiza pa ntchito yawo yofunikayi. Mwachitsanzo, ena amathandiza nawo pa ntchito zomanga Nyumba za Ufumu. Pomwe ena amathandiza nawo popereka chakudya, mayendedwe komanso zinthu zina. Komanso zimene tonsefe timalankhula kapena kuchita zikhoza kuthandiza akulu mumpingo komanso oyang’anira madera. Munkhaniyi tikambirana mmene timapindulira chifukwa cha ntchito imene “amuna” amenewa amagwira. Tikambirananso mmene tingasonyezere kuti timayamikira iwowo komanso Yesu.
NTCHITO ZIMENE ATUMIKI OTHANDIZA AMAGWIRA
4. Kodi ndi ntchito zina ziti zimene atumiki othandiza ankagwira m’nthawi ya atumwi?
4 M’nthawi ya atumwi, abale ena ankaikidwa kukhala atumiki othandiza. (1 Tim. 3:8) N’kutheka kuti abale amenewa ndi amene ankachita “utumiki wothandiza anthu” womwe Paulo analemba. (1 Akor. 12:28) Atumiki othandiza ayenera kuti ankagwira ntchito zina zofunika n’cholinga choti akulu aziika maganizo awo pa ntchito yofunika yophunzitsa ndi kuweta nkhosa. Mwachitsanzo, atumiki othandiza ayenera kuti ankathandiza pokopera Malemba kapena kugula zipangizo zogwirira ntchitoyi.
5. Kodi ndi ntchito zina ziti zothandiza zomwe atumiki othandiza amagwira masiku ano?
5 Kodi ndi ntchito zina ziti zothandiza zomwe atumiki othandiza amagwira mumpingo wanu? (1 Pet. 4:10) Iwo amasamalira ndalama zampingo kapena kuyang’anira magawo, kuitanitsa mabuku kuti ofalitsa alandire, kusamalira zipangizo zokuzira mawu ndi zoonetsera mavidiyo, kulandira alendo pamisonkhano kapenanso kugwira ntchito yosamalira pa Nyumba ya Ufumu. Ntchito zonsezi zimathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino pampingo. (1 Akor. 14:40) Atumiki othandiza ena amakamba nkhani pamisonkhano ya mkati mwa mlungu kapenanso nkhani za onse. Atumiki othandiza ena amasankhidwa kuti azithandiza woyang’anira kagulu. Nthawi zinanso atumiki othandiza oyenerera amapita ndi akulu ku maulendo a ubusa.
6. N’chifukwa chiyani timayamikira ntchito zimene atumiki othandiza amagwira?
6 Kodi ntchito zimene atumiki othandiza amagwira zimathandiza bwanji mpingo? Mlongo wina wa ku Bolivia dzina lake Beberly b ananena kuti: “Ndimasangalala ndi misonkhano chifukwa cha ntchito imene atumiki othandiza amagwira. Chifukwa cha ntchito yawo ndimatha kuimba, kupereka ndemanga, kumvetsera nkhani komanso kuonera mavidiyo. Amaonetsetsa kuti tikhale otetezeka komanso amathandiza anthu amene alumikizidwa pa vidiyokomfelensi. Misonkhano ikatha amatsogolera pa ntchito yoyeretsa, amasamalira ndalama za mpingo komanso amaonetsetsa kuti tikulandira mabuku. Ndimawayamikira kwambiri.” Leslie yemwe amakhala ku Colombia ndipo mwamuna wake ndi mkulu ananena kuti: “Mwamuna wanga amadalira atumiki othandiza kuti agwire ntchito zosiyanasiyana. Pakanapanda atumikiwa bwenzi akumatanganidwa kwambiri. Choncho ndimayamikira kwambiri khama lawo.” N’kutheka kuti ndi mmene inunso mumamvera.—1 Tim. 3:13.
7. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira atumiki othandiza? (Onaninso chithunzi.)
7 Ngakhale kuti mumtima mwathu tingawayamikire atumiki othandiza, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akol. 3:15) M’bale Krzysztof yemwe ndi mkulu ku Finland anafotokoza zimene amachita posonyeza kuyamikira. Iye anati: “Ndimalembera mtumiki wothandiza kakhadi kapena meseji yokhala ndi lemba lofotokoza mmene wandilimbikitsira kapenanso chifukwa chake ndikumuyamikira.” Pascal ndi mkazi wake Jael omwe amakhala ku New Caledonia amapempherera atumiki othandiza. Pascal anafotokoza kuti: “Chaposachedwapa, mapemphero athu akhala akuphatikizapo kuchonderera komanso kuyamikira atumiki othandiza omwe amagwira ntchito mwakhama mumpingo wathu.” Yehova amamva mapemphero amenewa ndipo izi zimathandiza mpingo wonse.—2 Akor. 1:11.
AKULU “AKUGWIRA NTCHITO MWAKHAMA PAKATI PANU”
8. N’chifukwa chiyani Paulo analemba kuti akulu a munthawi yake ‘ankagwira ntchito mwakhama’? (1 Atesalonika 5:12, 13)
8 M’nthawi ya atumwi, akulu ankagwira ntchito mwakhama kuti athandize mpingo. (Werengani 1 Atesalonika 5:12, 13; 1 Tim. 5:17) Iwo ankatsogolera zinthu mumpingo. Mwachitsanzo, ankachititsa misonkhano komanso kusankha zochita. Ankapatsa abale ndi alongo malangizo achikondi koma osapita m’mbali n’cholinga choti ateteze mpingo. (1 Ates. 2:11, 12; 2 Tim. 4:2) Abalewa ankagwiranso ntchito n’cholinga choti azipezera mabanja awo zinthu zofunika komanso kuwathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.—1 Tim. 3:2, 4; Tito 1:6-9.
9. Kodi ndi ntchito zina ziti zimene akulu amagwira masiku ano?
9 Akulu amakhala otanganidwa kwambiri masiku ano. Iwo amagwira ntchito yolalikira. (2 Tim. 4:5) Iwo amatsogolera mwakhama ntchitoyi, kuonetsetsa kuti ikuchitika mugawo la mpingo wawo komanso kutiphunzitsa kuti tiziigwira bwino. Iwo amagwiranso ntchito ngati oweruza achifundo komanso opanda tsankho. Mkhristu akachita tchimo lalikulu, akulu amamuthandiza kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova koma pa nthawi imodzimodziyo, amaonetsetsa kuti mpingo ukhale woyera. (1 Akor. 5:12, 13; Agal. 6:1) Akulu amadziwika kuti ndi abusa. (1 Pet. 5:1-3) Amakonzekera komanso kukamba nkhani pamisonkhano, kudziwa bwino aliyense mumpingo komanso kuchita maulendo a ubusa. Kuwonjezera pa ntchito zimenezi, akulu ena amathandiza pa ntchito zomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu, kukonzekera misonkhano ikuluikulu ndiponso kukhala m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala komanso Magulu Oyendera Odwala. Akulu amagwira ntchito mwakhama kuti atithandize.
10. N’chifukwa chiyani timayamikira akulu akhama?
10 Yehova ananeneratu kuti abusa adzatisamalira bwino n’cholinga choti ‘tisamaope kanthu kapena kuchita mantha.’ (Yer. 23:4) Mlongo wina wa ku Finland dzina lake Johanna anatsimikizira mawu amenewa pa nthawi imene mayi ake ankadwala kwambiri. Iye anati: “Ngakhale kuti ndinkavutika kufotokozera ena mmene ndinkamvera, mkulu wina yemwe sindimudziwa bwinobwino ankaleza nane mtima, kupemphera nane komanso kunditsimikizira kuti Yehova amandikonda. Sindikumbukira bwinobwino zimene ananena, koma chomwe ndimakumbukira n’chakuti ndinkadzimva kuti ndine wotetezeka. Ndikukhulupirira kuti Yehova ndi amene anamutuma kuti andithandize pa nthawi yoyenera.” Kodi inuyo akulu mumpingo wanu anakuthandizani bwanji?
11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza akulu? (Onaninso chithunzi.)
11 Yehova amafuna kuti tiziyamikira kwambiri akulu “chifukwa cha ntchito yawo.” (1 Ates. 5:12, 13) Henrietta yemwenso amakhala ku Finland ananena kuti: “Akulu amathandiza ena mofunitsitsa, koma sikuti iwo amakhala ndi nthawi kapena mphamvu zapadera. Ndipo nawonso amakumana ndi mavuto pa moyo wawo. Nthawi zina ndimangowauza kuti, ‘Inutu ndi mkulu wabwino, ndimangofuna kuti mudziwe zimenezo.’” Mlongo wina wa ku Türkiye c dzina lake Sera ananena kuti: “Kulimbikitsa akulu kuli ngati kuthira mafuta mugalimoto kuti ipitirize kuyenda. Choncho tikhoza kuwalembera kakhadi, kuwaitanira chakudya kapena kulowa nawo mu utumiki.” Kodi pali mkulu wina amene mumayamikira khama lake? Muzifunafuna mipata yomusonyeza kuti mumamuyamikira.—1 Akor. 16:18.
OYANG’ANIRA MADERA AMALIMBIKITSA MIPINGO
12. Kodi mipingo inkalimbikitsidwa bwanji m’nthawi ya atumwi. (1 Atesalonika 2:7, 8)
12 Yesu Khristu anapereka akulu ena ngati “mphatso” kuti azithandiza mipingo m’njira ina. Motsogoleredwa ndi Yesu, akulu ku Yerusalemu anatumiza Paulo, Baranaba ndi ena monga oyang’anira oyendayenda. (Mac. 11:22) Anachita zimenezi kuti azikalimbikitsa mipingo ngati mmenenso akulu ndi atumiki othandiza amachitira. (Mac. 15:40, 41) Amunawa analolera kusiya zinthu zina, ngakhalenso kuika moyo wawo pangozi, n’cholinga choti aziphunzitsa komanso kulimbikitsa anzawo.—Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.
13. Kodi oyang’anira madera amagwira ntchito ziti?
13 Nthawi zambiri oyang’anira madera amakhala akuyendayenda. Ena amayenda makilomita ambirimbiri kuti akafike kumipingo ina. Mlungu uliwonse, woyang’anira dera amakamba nkhani zingapo komanso kuchita maulendo a ubusa. Amachititsa msonkhano wa apainiya, wa akulu komanso misonkhano yokonzekera utumiki. Amathandizana ndi akulu pokonzekera misonkhano yadera ndi yachigawo ndiponso kukamba nkhani pamisonkhanoyo. Amaphunzitsa sukulu za apainiya komanso kukonza msonkhano wapadera wa apainiya m’dera lawo ndipo nthawi zina amagwira ntchito zimene apemphedwa ndi ofesi ya nthambi.
14. N’chifukwa chiyani timayamikira oyang’anira dera akhama?
14 Kodi mipingo imapindula bwanji ndi ntchito zimene oyang’anira dera amagwira? Poyamikira zimene oyang’anira dera amachita, m’bale wina ku Türkiye ananena kuti: “Woyang’anira dera aliyense akafika zimandilimbikitsa kuti ndizithandiza abale ndi alongo anga. Ndakumanapo ndi oyang’anira dera ambiri koma palibe amene anandisonyezapo kuti ndi wotanganidwa kwambiri kapena wosachezeka.” Johanna yemwe tamutchula kale uja anayenda mu utumiki ndi woyang’anira dera ndipo sanapeze anthu m’nyumba zawo, koma iye anati: “Sindidzaiwala zimene zinachitika tsiku limenelo. Ndinkawasowa kwambiri azichemwali anga omwe anali atangosamuka kumene. Ndiye woyang’anira derayo anandilimbikitsa pondiuza kuti panopa ndi zovuta kuti tizikhala ndi achibale athu nthawi zonse. Koma m’dziko latsopano tidzakhala ndi nthawi yambiri yokhala nawo limodzi.” Mofanana ndi zimenezi anthu ambiri amakonda oyang’anira dera amene anawayendera.—Mac. 20:37–21:1.
15. Mogwirizana ndi 3 Yohane 5-8, kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira oyang’anira dera? (Onaninso chithunzi.) (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira akazi a oyang’anira madera, nanga tingachite bwanji zimenezi? (Onaninso bokosi lakuti “ Muzikumbukira Akazi Awo.”)
15 Mtumwi Yohane analimbikitsa Gayo kuti azilandira bwino abale oyendayenda ndipo anamuuza kuti: “Anthu oterewa akamachoka, uziyesetsa kuwathandiza mʼnjira imene Mulungu angasangalale nayo.” (Werengani 3 Yohane 5-8.) Njira imodzi imene ifenso tingachitire zimenezi ndi kuitanira woyang’anira dera kuti tidzadye naye limodzi. Njira ina ndi kulowa nawo mu utumiki pamene akuyendera mpingo wathu. Leslie yemwe tamutchula kale uja amasonyezanso kuyamikira m’njira ina. Iye anati: “Ndimapempha Yehova kuti aziwathandiza kupeza zofunika. Ine ndi mwamuna wanga timawalemberanso makalata owauza mmene atithandizira pa ulendo wawo.” Tizikumbukira kuti nawonso oyang’anira dera amatopa komanso amakumana ndi mavuto. Nthawi zina amadwala, amakhala ndi nkhawa kapenanso kukhumudwa. Choncho mawu amene mungawalankhule kapenanso mphatso imene mungawapatse zingakhale mayankho a mapemphero awo.—Miy. 12:25.
TIMAFUNIKIRA AMUNA OMWE ALI NGATI “MPHATSO”
16. Mogwirizana ndi Miyambo 3:27, kodi abale ayenera kudzifunsa mafunso ati?
16 Padziko lonse, pakufunikira abale oti atumikire m’maudindo osiyanasiyana. Ngati ndinu m’bale wobatizidwa, kodi ‘mungathe kuthandiza’ abale ndi alongo? (Werengani Miyambo 3:27.) Kodi mukufuna mutakhala mtumiki wothandiza? Kodi mungayesetse kuti muzitumikira abale anu monga mkulu? d Kodi mungasinthe zinthu zina n’cholinga choti mukalowe nawo Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Sukulu imeneyi ikhoza kukuthandizani kuti Yesu akugwiritseni ntchito kwambiri. Ngati mukuganiza kuti ndinu wosayenerera, muyenera kuipempherera nkhaniyi kwa Yehova. Muzimupempha kuti akupatseni mzimu woyera kuti muzitha kugwira ntchito iliyonse imene mwapatsidwa.—Luka 11:13; Mac. 20:28.
17. Kodi zimene takambiranazi zikutiuza chiyani zokhudza Mfumu yathu Khristu Yesu?
17 Zimene Yesu wachita posankha “amuna” ena kuti azitumikira mumpingo ndi umboni wakuti akutitsogolera masiku otsiriza ano. (Mat. 28:20) Timayamikira kuti tili ndi Mfumu yachikondi, yopatsa komanso imene imatiganizira. Mfumuyi yatipatsa anthu oyenerera kuti azitithandiza. Choncho tiyeni tizifunafuna mipata yoti tiziyamikira abale akhamawa. Koposa zonse, tiziyamikira Yehova, yemwe amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.”—Yak. 1:17.
NYIMBO NA. 99 Abale Ambirimbiri
a Akulu amene amatumikira m’Bungwe Lolamulira, makomiti othandiza Bungwe Lolamulira, Makomiti a Nthambi komanso mautumiki ena, nawonso ndi “mphatso.”
b Mayina ena asinthidwa.
c Poyamba linkatchedwa kuti Turkey.
d Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukhale mtumiki wothandiza kapena mkulu, onani nkhani yakuti “Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mtumiki Wothandiza?” komanso “Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mkulu?” mu Nsanja ya Olonda ya November 2024.