Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”​—SALIMO 67:6

Mukhoza Kusangalala ndi Madalitso Ochokera kwa Mlengi Wathu Mpaka Kalekale

Mukhoza Kusangalala ndi Madalitso Ochokera kwa Mlengi Wathu Mpaka Kalekale

Mulungu analonjeza mneneri Abulahamu kuti “mitundu yonse yapadziko lapansi” idzapeza madalitso kudzera mwa mmodzi mwa mbadwa zake. (Genesis 22:18) Kodi ndi ndani anadzakhala mbadwa imeneyi?

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Mulungu anapatsa Yesu, yemwe anali mbadwa ya Abulahamu, mphamvu zochita zozizwitsa zikuluzikulu. Zozizwitsa zimene anachitazi zinasonyeza kuti kudzera mwa Yesu, anthu amitundu yonse adzalandira madalitso amene Mulungu analonjeza Abulahamu.​—Agalatiya 3:14.

Zozizwitsa zimene Yesu anachita zinathandiza anthu kuzindikira kuti iye ndi amene Mulungu anamusankha kuti adzadalitse anthu. Zinasonyezanso mmene Mulungu adzamugwiritsire ntchito podalitsa anthu mpaka kalekale. Taonani mmene zozizwitsa zimene Yesu anachita zikusonyezera makhalidwe ake ena ochititsa chidwi.

Ankachita zinthu mwachikondi—Yesu anachiritsa odwala.

Nthawi ina munthu wina wakhate anachonderera Yesu kuti amuchiritse. Yesu anamukhudza ndi kumuyankha kuti: “Ndikufuna.” Nthawi yomweyo khatelo linatha.​—Maliko 1:40-42.

Anali wopatsa​—Yesu anadyetsa anthu anjala.

Yesu sanafune kuti anthu abwerere kwawo ali ndi njala. Kawiri konse iye anadyetsa anthu masauzande ambirimbiri pochulukitsa mitanda ya mkate yochepa ndi tinsomba tochepa. (Mateyu 14:17-21; 15:32-38) Anthuwo atadya, onse anakhuta ndipo chakudya chinatsala chambirimbiri.

Anali wachifundo​—Yesu anaukitsa akufa.

Mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mkazi wamasiye atamwalira, Yesu “anawamvera chifundo” mayiwo ndipo anaukitsa mwanayo chifukwa anali yekhayo amene akanawasamalira.​—Luka 7:12-15.