Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chifukwa Chiyani Timavutika?

Kodi N’chifukwa Chiyani Timavutika?

Ngati Mulungu si amene amachititsa kuti anthu azivutika ndi njala, umphawi, nkhondo, matenda komanso ngozi zadzidzidzi ndiye n’chiyani chimachititsa mavuto amenewa? Baibulo limatchula zifukwa zitatu zimene zimachititsa kuti anthu azivutika:

  1. Kudzikonda, Dyera Komanso Chidani. “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Nthawi zambiri anthu amavutika chifukwa cha zochita za anthu ena omwe ndi adyera, odzikonda komanso ankhanza.

  2. Nthawi Yatsoka ndi Zinthu Zosayembekezereka. Baibulo limati: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.” (Mlaliki 9:11) Anthu ena amatha kuvulala kapena kumwalira chifukwa choti anali pamalo olakwika komanso pa nthawi yolakwika. Ndipo ena amachita ngozi chifukwa cha anthu ena osasamala kapena chifukwa choti wina analakwitsa zinazake.

  3. Wolamulira Woipa Wadzikoli. Baibulo limafotokoza chifukwa chachikulu chimene chimachititsa kuti anthu azivutika. Limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” ndi Satana Mdyerekezi yemwe poyamba anali mngelo wa Mulungu koma “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Angelo ena sanamvere Mulungu ndipo anagwirizana ndi Satana pofuna kukwaniritsa zolakalaka zawo zadyera. Izi zinachititsa kuti akhale ziwanda. (Genesis 6:1-5) Kungoyambira pamene anapanduka, Satana ndi ziwanda akhala akulimbikitsa anthu kuti azichita zinthu zankhanza padzikoli. Ndipotu zimenezi zikuchitika kwambiri makamaka masiku ano. Panopa Mdyerekezi ndi wokwiya kwambiri ndipo “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” zimenezi zachititsa kuti padzikoli pakhale “tsoka” kapena kuti mavuto. (Chivumbulutso 12:9, 12) Kunena zoona Satana ndi wolamulira wankhanza. Iye amasangalala akamaona anthu akuvutika. Choncho ndi Satana amene amachititsa kuti anthu azivutika osati Mulungu.

TAGANIZIRANI MFUNDO IYI: Munthu wopanda chisoni komanso woipa mtima ndi amene angachititse kuti anthu azivutika. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Popeza iye ali ndi chikondi “sangachite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.”​—Yobu 34:10.

Komabe, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu Wamphamvuyonse apitirizabe kulekerera kuti Satana azilamulira anthu mwankhanza mpaka liti?’ Monga mmene taonera, Mulungu amadana ndi zinthu zoipa ndipo zimamuwawa akamaona tikuvutika. Komanso Mawu ake amatilimbikitsa kuti: ‘Tizimutulira nkhawa zathu zonse, pakuti amatidera nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Popeza Mulungu amatikonda komanso ali ndi mphamvu, posachedwapa adzachotsa mavuto onse komanso zinthu zopanda chilungamo monga mmene nkhani yotsatira ikufotokozera. *

^ ndime 7 Kuti mumve zambiri pa nkhani ya chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti anthu azivutika, werengani mutu 11 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungapangenso dawunilodi bukuli pa www.jw.org/ny.