“Kodi Mulungu Anali Kuti?”
“NTHAWI ZAMBIRI ANTHU AMADZIFUNSA KUTI: KODI MULUNGU ANALI KUTI?”—Awa ndi mawu omwe Papa Benedict wa 16, ananena ali kumalo omwe kale anali ndende yozunzirako anthu ku Auschwitz, m’dziko la Poland.
KODI PA NTHAWI INA PATACHITIKA NGOZI INAYAKE, MUNAYAMBA MWADZIFUNSAPO KUTI, ‘MULUNGU ANALI KUTI’ KAPENA MUNAYAMBA MWAKAYIKIRAPO NGATI AMAKUKONDANI INUYO PANOKHA?
Kapena munayamba mwamvapo ngati mmene Sheila, yemwe amakhala ku United States, anamvera? Iye anakulira m’banja lokonda kupemphera ndipo anati: “Kuyambira ndili mwana ndinkachita chidwi ndi Mulungu chifukwa ndi amene anatilenga. Komabe sindinkaona kuti ndinali naye pa ubwenzi. Ndinkadziwa ndithu kuti amaona zimene ndimachita koma ndinkaganiza kuti sankachita nazo chidwi kwenikweni. Sindinkaona kuti Mulungu amadana nane komanso sindinkakhulupirira kuti amandikonda.” Kodi n’chifukwa chiyani Sheila ankakayikira chonchi? Iye anati: “Banja lathu linkakumana ndi mavuto ambiri, ndipo zinkaoneka ngati Mulungu sakutithandiza ngakhale pang’ono.”
Mofanana ndi Sheila, n’kutheka kuti nanunso mumakhulupirira kuti Mulungu alipo. Koma mwina mumakayikira ngati amakukondani. Nayenso Yobu, yemwe ankakhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu komanso nzeru, anakayikirapo ngati Mulungu ankamukonda. (Yobu 2:3; 9:4) Atakumana ndi mavuto aakulu motsatizana, n’kusowa mtengo wogwira, anafunsa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu, n’kunditenga ine ngati mdani wanu?”—Yobu 13:24.
Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Kodi Mulungu ndi amene amachititsa mavuto amene timakumana nawo? Kodi pali umboni wosonyeza kuti Mulungu amatiganizira anthufe komanso wina aliyense payekhapayekha? Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu amaona zimene zikutichitikira, amatimvetsa, amadziwa mmene tikumvera komanso amatithandiza tikamakumana ndi mavuto?
M’nkhani zotsatirazi tiona mmene zinthu zomwe Mulungu analenga zimatithandizira kudziwa kuti amatiganizira. (Aroma 1:20) Kenako tiziona mmene Baibulo limasonyezera kuti Mulungu amatikonda kwambiri. Ngati ‘titamudziwa’ bwino kudzera m’zimene analenga komanso Mawu ake, sitingakayikire kuti ‘amatidera nkhawa.’—1 Yohane 2:3; 1 Petulo 5:7.