Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

Otsatira ena a Yesu ankafuna atadziwa nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira. Yesu anawauza kuti sangathe kudziwa tsiku komanso nthawi yeniyeni yomwe Ufumuwu udzayambe kulamulira dzikoli. (Machitidwe 1:6, 7) Koma asananene zimenezi, anafotokozera otsatira akewo kuti akadzaona zinthu zinazake zikuchitika pa nthawi yofanana ‘adzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira’ ndiponso kuti nthawi yoti uyambe kulamulira yafika.​—Luka 21:31.

KODI NDI ZINTHU ZITI ZOMWE YESU ANANENA KUTI ZIDZACHITIKA?

Yesu ananena kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana.” (Luka 21:10, 11) Zinthu zimenezi ndi zomwe Yesu ananena kuti zikadzachitika pa nthawi yofanana, zidzakhala chizindikiro choti “ufumu wa Mulungu wayandikira.” Kodi pali umboni wakuti zinthu zimenezi zikuchitika pa nthawi imodzi komanso padziko lonse? Taganizirani izi.

1. NKHONDO

Mu 1914, padzikoli panachitika nkhondo yaikulu kwambiri yomwe inali isanachitikeponso. Olemba mbiri amanena kuti chakachi chinali chapadera chifukwa ndi chomwe kunachitika nkhondo yapadziko lonse kwa nthawi yoyamba. Pa nkhondoyi, anthu anagwiritsa ntchito koyamba zida monga akasinja, mabomba oponya kuchokera m’ndege, mfuti zamphamvu kwambiri, mpweya wapoizoni ndiponso zida zina zoopsa kwambiri. Kenako panadzachitika nkhondo yachiwiri yapadziko lonse ndipo pa nthawiyi anthu anayamba kugwiritsa ntchito mabomba anyukiliya. Kuyambira mu 1914, anthu akhala akumenya nkhondo m’mayiko osiyanasiyana ndipo anthu mamiliyoni ambiri aphedwa.

2. ZIVOMEZI

Buku lina limanena kuti chaka chilichonse kumachitika zivomezi zamphamvu pafupifupi 100 “zowononga kwambiri.” (Britannica Academic) Ndipotu lipoti la bungwe lina lofufuza za nthaka ndi miyala linanena kuti “tikatengera mmene zivomezi zakhala zikuchitikira kuyambira m’ma 1900, tikuyembekezera kuti kutsogoloku kuzichitikanso zivomezi zina zamphamvu kwambiri pafupifupi 16 chaka chilichonse.” (United States Geological Survey) Anthu ena akhoza kuganiza kuti zivomezi zikuoneka kuti zikuwonjezereka chifukwa choti akatswiri apeza njira zapamwamba zochitira kafukufuku. Ngakhale zili choncho, zoona n‘zakuti panopa zivomezi zamphamvu zikubweretsa mavuto komanso kuphetsa anthu ambiri padziko lonse.

3. KUSOWA KWA CHAKUDYA

Padziko lonse lapansi, chakudya chimasowa chifukwa cha nkhondo, chinyengo, mavuto aakulu azachuma, kusachita bwino kwa zaulimi kapenanso kusakonzekera bwino mavuto azanyengo. Lipoti la 2018 la nthambi ya UN yoona za chakudya padziko lonse linanena kuti: “Padziko lonse, anthu 821 miliyoni alibe chakudya chokwanira ndipo pa anthu amenewa 124 miliyoni alibiretu chakudya.” Matenda osowa zakudya m’thupi achititsa kuti ana pafupifupi 3.1 miliyoni azimwalira chaka chilichonse. Mu 2011, ana pafupifupi 45 pa 100 alionse, anamwalira chifukwa cha matendawa.

4. MATENDA KOMANSO MILIRI

Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti: “Zaka za m’ma 2000, kwakhala kukuchitika miliri yoopsa. Matenda akale monga kolera ndi chikasu ayambiranso kuvutitsa anthu ndipo pabweranso ena atsopano monga SARS, chimfine choopsa, matenda obanika a MERS, Ebola ndi Zika.” Posachedwapa kwabwera mliri wa COVID-19. Ngakhale kuti madokotala ndi asayansi aphunzira zambiri zokhudza matenda, akulephera kuthana ndi matenda onse.

5. NTCHITO YOLALIKIRA PADZIKO LONSE

Yesu ananenanso za chinthu china chomwe chidzachitike monga chizindikiro. Anafotokoza kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Ngakhale kuti padzikoli pali mavuto aakulu, anthu oposa 8 miliyoni ochokera m’mitundu yosiyanasiyana akulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’mayiko 240 ndiponso m’zilankhulo zoposa 1,000. Zinthu zoterezi sizinachitikeponso.

KODI ZIKUCHITIKAZI ZIKUTIKHUDZA BWANJI?

Zinthu zimene Yesu ananena kuti zidzakhala chizindikiro, zikuchitika masiku ano. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira zimenezi? Zili choncho chifukwa Yesu ananena kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.”​—Luka 21:31.

Posachedwapa Ufumu udzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu padzikoli

Tikaganizira chizindikiro chimene Yesu anapereka ndiponso zimene Baibulo limanena, zimatithandiza kuzindikira kuti Mulungu anakhazikitsa Ufumu wake kumwamba mu 1914. a Nthawi imeneyo, Mulungu anaika Mwana wake, Yesu Khristu, kukhala Mfumu. (Salimo 2:2, 4, 6-9) Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira padzikoli ndipo udzachotsa maulamuliro ena onse. Udzachititsanso kuti dzikoli likhale labwino kwambiri ndipo anthu adzakhalamo mpaka kalekale.

Posachedwapa mawu a Yesu am’pemphero lija adzakwaniritsidwa. Paja iye anapemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Koma kodi Ufumuwu wakhala ukuchita chiyani kuyambira pamene unakhazikitsidwa mu 1914? Nanga tiyembekezere kuti udzachita zotani ukamadzalamulira anthu onse padzikoli?

a Kuti mudziwe zambiri zokhudza chaka cha 1914, onani phunziro 32 m’buku lakuti, Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova.