Kodi Mulungu Ndi Ndani?
Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Mulungu. Koma mukawafunsa kuti Mulungu ndi ndani, amayankha zosiyanasiyana. Ena amaona kuti Mulungu ndi woweruza wankhanza amene amangoganizira zopereka chilango kwa anthu olakwa. Pomwe ena amaona kuti Mulungu amakonda komanso kukhululukira anthu nthawi zonse, kaya anthuwo achita zotani. Ndiye palinso ena amene amaona kuti Mulungu ali kutali kwambiri ndipo alibe nafe chidwi. Chifukwa choti pali maganizo osiyanasiyana chonchi onena za Mulungu, anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kudziwa kuti zoona ndi ziti.
Kodi kudziwa zolondola kuli ndi phindu lililonse? Inde. Kudziwa zolondola zokhudza Mulungu kungakuthandizeni kwambiri. (Machitidwe 17:26-28) Mukamayesetsa kumuyandikira kwambiri, m’pamenenso iye amakuthandizani komanso kukukondani kwambiri. (Yakobo 4:8) Chofunikanso kwambiri n’chakuti, kudziwa Mulungu molondola kungakuthandizeni kuti mudzakhale ndi moyo wosatha.—Yohane 17:3.
Kodi mungatani kuti mumudziwe Mulungu? Taganizirani za munthu amene mumamudziwa bwino, mnzanu wapamtima. Kodi zinayamba bwanji kuti munthuyo afike pokhala mnzanu? Muyenera kuti poyamba munadziwa dzina lake, makhalidwe ake, zimene amakonda, zimene amadana nazo, zimene wachita, zimene amafuna kudzachita ndi zina zambiri. Choncho tingati munaphunzira zokhudza munthuyo ndipo zimenezi ndi zimene zinachititsa kuti muyambe kumukonda.
N’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Kudziwa mayankho a mafunso otsatirawa kungatithandize kuti timudziwe bwino:
Magaziniyi yakonzedwa n’cholinga choti itithandize kupeza mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa. Nkhani zimene zili m’magaziniyi zikuthandizani kudziwa zolondola zokhudza Mulungu. Zikuthandizaninso kudziwa mmene kukhala naye pa ubwenzi wolimba kungakuthandizireni.