Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?

Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?

NKHANI yakuti ngati zili zololeka kuti amuna kapena akazi okhaokha azikwatirana ili mkamwamkamwa m’mayiko ambiri. Ndipotu mu 2015, khoti lalikulu kwambiri ku United States linalengeza kuti maukwati a amuna kapena akazi okhaokha ndi ovomerezeka m’dzikolo. Kenako anthu ambiri anayamba kufufuza nkhaniyi pa intaneti. Ndipo funso limene ankalemba kwambiri linali lakuti, “Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani ya maukwati a amuna kapena akazi okhaokha?”

Baibulo silinena chilichonse chokhudza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha. Ndiyeno funso n’kumati, kodi Baibulo limalola kuti akazi kapena amuna azigonana okhaokha?

Anthu ambiri amathamangira kunena kuti akudziwa yankho la funsoli asanafufuze bwinobwino m’Baibulo. Komatu mayankho awo amakhala osiyanasiyana. Ena amanena kuti Baibulo silivomereza kuti amuna kapena akazi azigonana okhaokha. Pomwe ena amanena kuti lamulo la m’Baibulo lakuti “uzikonda mnzako” limapatsa anthu ufulu wogonana ndi aliyense.—Aroma 13:9.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kodi ndi mfundo iti imene mukuona kuti ndi yolondola?

  1. Baibulo sililola kuti amuna kapena akazi okhaokha azigonana.

  2. Baibulo limalola kuti amuna kapena akazi okhaokha azigonana.

  3. Baibulo limalimbikitsa anthu kuti azidana ndi amuna kapena akazi ogonana okhaokha.

MAYANKHO:

  1. ZOONA. Baibulo limati: “Amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo . . . sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Lamuloli limakhudzanso akazi amene amagonana ndi akazi anzawo.—Aroma 1:26.

  2. ZABODZA. Baibulo limanena kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana ndi amene ayenera kumagonana.—Genesis 1:27, 28; Miyambo 5:18, 19.

  3. ZABODZA. Ngakhale kuti Baibulo limaletsa kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, silimalimbikitsa anthu kuti azidana kapenanso kuchitira nkhanza anthu ochita zimenezi.—Aroma 12:18.

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani Pa nkhaniyi?

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo n’zothandiza ndipo amayesetsa kuzitsatira. (Yesaya 48:17) Choncho iwo amapewa kuchita zinthu zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani yakugonana, monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. (1 Akorinto 6:18) A Mboni anasankha zimenezi ndipo ali ndi ufulu wozitsatira.

A Mboni za Yehova amachitira ena zimene iwonso angakonde kuti ena awachitire

A Mboni za Yehova amayesetsa “kukhala pa mtendere ndi anthu onse.” (Aheberi 12:14) Ngakhale kuti savomereza kuti amuna kapena akazi okhaokha azigonana, iwo sakakamiza anthu kuti aziyendera maganizo awo. Komanso sachitira nkhanza anthu amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha kapenanso kusangalala akamamva kuti ena akuwachitira zankhanza. A Mboni za Yehova amayesetsa kuchitira ena zimene nawonso angakonde kuti ena awachitire.—Mateyu 7:12.

Kodi Baibulo Limalimbikitsa Anthu Kuti Azisalana?

Anthu ena anganene kuti Baibulo limalimbikitsa anthu kuti azisala amuna kapena akazi amene amagonana okhaokha, ndipo amaona kuti anthu omwe amatsatira mfundo za m’Baibulo ndi omva zawo zokha. Iwo amanena kuti: ‘Nthawi yomwe Baibulo linkalembedwa n’kuti anthu asanachangamuke. Masiku ano timakhala bwinobwino ndi anthu osiyana nawo mitundu, mayiko ndiponso amuna kapena akazi omwe amasankha kugonana okhaokha.’ Anthu amaganizo oterewa amaona kuti kudana ndi khalidweli kumangofanana ndi kudana ndi anthu a mitundu ina. Komatu zimenezi sizingakhale zomveka. N’chifukwa chiyani tikutero?

Zili choncho chifukwa chakuti kudana ndi khalidwe la kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha n’kosiyana kwambiri ndi kudana ndi anthu akhalidweli. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azilemekeza anthu onse. (1 Petulo 2:17) Koma mfundoyi sikusonyeza kuti Akhristu azingochita nawo makhalidwe osiyanasiyana amene anthu ena akuchita.

Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti inuyo mumaona kuti kusuta kumaononga moyo ndiponso n’koipa. Ndiyeno munthu amene mumagwira naye ntchito amasuta. Kodi zingakhale zomveka ngati anthu atamati ndinu wosazindikira chifukwa chakuti mumadana ndi kusuta? Kodi tinganene kuti mumamusala kapena kumuda chifukwa chakuti inu simusuta? Ngati mnzanuyo atamakukakamizani kuti muyambe kusuta, kodi pamenepa sitinganene kuti iyeyo ndi wosazindikira komanso wankhakamira?

A Mboni za Yehova anasankha kumatsatira mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Baibulo. Iwo salimbikitsa anthu kuchita zinthu zimene Baibulo limaletsa. Komabe sanyoza kapena kuchitira nkhanza anthu amene ali ndi makhalidwe osiyana ndi awo.

Kodi Zimene Baibulo Limanena N’zankhanza?

Kodi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo anabadwa choncho? Ngati zili choncho, kodi sikungakhale kuwalakwira kunena kuti amalakwitsa kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo?

Baibulo silinena kuti anthu ena amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo chifukwa cha mmene anabadwira. Komabe limasonyeza kuti anthu ena amavutika kusiya makhalidwe ena ake. Ngakhale zili choncho, Baibulo limati tizipewa makhalidwe oipa, monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kuti tisangalatse Mulungu.—2 Akorinto 10:4, 5.

Ena anganene kuti zimene Baibulo limanenazi n’zankhanza. Amanena zimenezi chifukwa amaganiza kuti anthufe timayenera kuchita zimene thupi lathu likufuna. Amaonanso kuti n’zosatheka munthu kudziletsa maganizo ofuna kugonana akamubwerera. Komabe Baibulo limasonyeza kuti anthu analengedwa mosiyana ndi nyama chifukwa angathe kudziletsa. Apatu Mulungu anatilemekeza kwambiri anthufe.—Akolose 3:5.

Taganizirani izi: Akatswiri ena amanena kuti anthu ena mwachibadwa amakhala osachedwa kupsa mtima. Pa nkhaniyi, Baibulo silinena kuti anthu ena sachedwa kupsa mtima chifukwa cha mmene anabadwira. Komabe limasonyeza kuti anthu ena amakhala ‘okonda kukwiya’ ndiponso ‘aukali.’ (Miyambo 22:24; 29:22) Baibulo limanenanso kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.”—Salimo 37:8; Aefeso 4:31.

Anthu ambiri angavomereze kuti malangizo amenewa ndi othandiza komanso sakusonyeza nkhanza kwa anthu amene ali ndi vutoli. Ndipotu akatswiri amene amakhulupirira kuti anthu ena mwachibadwa sachedwa kupsa mtima ndi amenenso amayesetsa kuthandiza anthu oterewa kuti azidziletsa.

Nawonso a Mboni za Yehova amayesetsa kuthandiza anthu kuti asinthe khalidwe lililonse losemphana ndi zimene Baibulo limanena monga kugonana kwa amuna ndi akazi omwe sanakwatirane. Baibulo limalangiza anthu a amakhalidwe onsewa kuti: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana.”—1 Atesalonika 4:4, 5.

“Ena Mwa Inu Munali Otero”

Anthu amene ankafuna kukhala Akhristu m’nthawi ya atumwi, anali ndi makhalidwe osiyanasiyana ndipo ena anafunika kusintha kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za anthu ena omwe anali “adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo.” Limanenanso kuti: “Ndipo ena mwa inu munali otero.”1 Akorinto 6:9-11.

Kodi mfundo yakuti “ena mwa inu munali otero,” ikutanthauza kuti anthu amene anasiya kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo sankakhala ndi maganizo ofuna kuchitanso khalidweli? Ayi, tikutero chifukwa Baibulo limalangiza anthu oterewa kuti: “Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.”—Agalatiya 5:16.

Apatu sikuti Baibulo likunena kuti Mkhristu akasintha sangakhalenso ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. M’malomwake limanena kuti munthu angasankhe kuchita kapena kusachita zoipa zimene akuganizazo. Akhristu amayesetsa kudziletsa kuti asachite zinthu zoipa zimene mtima wawo umalakalaka.—Yakobo 1:14, 15.

Baibulo limasonyeza kuti kulakalaka zinthu n’kosiyana ndi kuzichita. (Aroma 7:16-25) Choncho, munthu yemwe amalakalaka kugonana ndi amuna kapena akazi anzake angathetse vutoli ngati atasiya kuganizira kwambiri zimenezi. Izi n’zotheka chifukwa anthufe timatha kudziletsa kuti tisakwiye msanga, tisachite chiwerewere ndiponso tisakhale adyera.—1 Akorinto 9:27; 2 Petulo 2:14, 15.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, iwo sakakamiza anthu ena kuti azitsatira. Ndipotu amalemekeza ufulu wa ena ngakhale kuti zochita za anthuwo sizigwirizana ndi zimene iwo amachita. Uthenga umene a Mboni za Yehova ali nawo ndi wothandiza kwambiri ndipo amafunitsitsa kuuza anthu omwe angafune kumvetsera.—Machitidwe 20:20.

1. Aroma 12:18: “Khalani mwamtendere ndi anthu onse.”

2. Yesaya 48:17: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”

3. 1 Akorinto 6:18: “Thawani dama.”

4. 1 Petulo 2:17: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.”

5. Akolose 3:5: “Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana.”

6. Yakobo 1:14, 15: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.”