Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana amisinkhu yosiyanasiyana akuseweretsa zipangizo zamakono m’malo momasewera ndi zidole kapena kuchita masewera olimbitsa thupi.

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ana Anu?

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ana Anu?

Nthawi zambiri anthu akuluakulu zimawavuta kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono poyerekezera ndi ana.

Koma anthu ena anazindikira kuti ana amene amathera nthawi yambiri pa intaneti . . .

  • amakhala odalira kwambiri zipangizo zawo.

  • amavutitsa anzawo kapena kuvutitsidwa pa intaneti.

  • amaona zolaula, kaya mwadala kapena mwangozi.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Mnyamata ali ndi foni m’manja ndipo mwamantha akutseka chitseko cha kuchipinda kwake pamene mayi ake akudutsa.

KUDALIRA ZIPANGIZO

Zinthu zina za pa intaneti, mwachitsanzo magemu, zinapangidwa m’njira yakuti munthu akaziyamba kuzikhala kovuta kuti asiye. Moti buku lina limanena kuti “mapulogalamu omwe ali m’mafoni athu anapangidwa kuti tizingokhalira pafoni.” (Reclaiming Conversation) Izi zili choncho chifukwa anthu amalonda amapanga ndalama zambiri tikamathera nthawi yochuluka tikuona malonda amene amaika pa intaneti.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi ana anu amaoneka kuti amakonda kwambiri zipangizo zamakono? Nanga mungawathandize bwanji kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yawo?​—AEFESO 5:15, 16.

KUVUTITSA ENA PA INTANETI

Anthu ena akakhala pa intaneti amalemba mawu achipongwe, otukwana komanso saganizira mmene zimenezi zingakhudzire anthu ena ndipo izi zingachititse kuti ayambe kuvutitsa anzawo kapena kuvutitsidwa.

Anthu ena amachita zinthu mosayenera pa intaneti chifukwa amaganiza kuti zimawapatsa mwayi woti akhale otchuka. Kapena wina angachite zimenezi chifukwa chakuti anzake sanamuitane ku zochitika zina, mwachitsanzo kupate, ndipo angaganize kuti anzakewo akumukhaulitsa.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi ana anu amachita zolemekeza anzawo pa intaneti? (Aefeso 4:31) Kodi amamva bwanji akaona kuti anzawo sanawaitanire ku zochitika zina?

ZOLAULA

Masiku ano n’zosavuta kupeza zinthu zoipa pa intaneti. Mapulogalamu ena amapereka mwayi kwa makolo woti atha kutchera zipangizo za ana awo kuti pasamabwere zinthu zoipa akakhala pa intaneti, koma ngakhale zili choncho nthawi zina ana amaonabe zinthu zoipa.

Kutumizirana zithunzi kapena zinthu zina zolaula kukhoza kukhala kuphwanya malamulo. M’madera ena, potengera ndi malamulo a m’deralo komanso zaka za anthu okhudzidwawo, amene amachita zimenezi akhoza kuimbidwa mlandu ogona ana.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti asakodwe mumsampha oona kapena kutumiza zinthu zolaula pa intaneti?—AEFESO 5:3, 4.

ZIMENE MUNGACHITE

MUZIPHUNZITSA ANA ANU

Ngakhale kuti ana savutika kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, amafunikabe kuthandizidwa. Buku lina linanena kuti kumpatsa mwana foni kapena chipangizo china chamakono koma asakudziwa mmene angachigwiritsire ntchito ndi “kusaganiza bwino, ndipo kuli ngati kumulola kuti adumphire m’madzi koma asakudziwa kusambira.”​—Buku lakuti Indistractable.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—MIYAMBO 22:6.

Pa mfundo zotsatirazi, onani zimene mungakonde kugwiritsa ntchito, kapena lembani zanu zimene mungaganize.

  • Kukambirana ndi mwana wanga mmene angasonyezere ulemu kwa anthu ena pa intaneti

  • Kuthandiza mwana wanga kuti asamadzione kuti ndi wosafunikira

  • Kutchera chipangizo cha mwana wanga kuti pasamabwere zinthu zoipa

  • Nthawi ndi nthawi kuona zinthu zimene zili mufoni ya mwana wanga

  • Kuika malire a nthawi imene mwana angamathere pafoni kapena chipangizo chake tsiku lililonse

  • Mwana wanga asamagone ndi chipangizo chamakono kuchipinda kwake

  • Kuletsa aliyense kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono pa nthawi imene tikudyera limodzi