Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

4 Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

4 Kodi Tinalengedwa Kuti Tizivutika?

Chifukwa Chake Kudziwa Yankho la Funsoli Kuli Kofunika

Yankho la funso limeneli limakhudza mmene timaonera cholinga cha moyo.

Taganizirani Izi

Kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu amene analenga zinthu zokongola zonsezi, alenge anthufe kuti tizivutika?

Anthu amene sakhulupirira Mulungu amaona kuvutika ngati chifukwa chokayikirira zolinga za Mulungu komanso ngati Mulunguyo alipodi. Iwo amakhulupirira kuti kuvutika kumasonyeza kuti, (1) Mulungu alibe mphamvu zothetsera mavuto, (2) Mulungu sizimamukhudza choncho saona chifukwa chothetsera mavuto, kapena (3) Kulibe Mulungu.

Kodi timavutika chifukwa cha zifukwa zokhazi basi?

KUTI MUDZIWE ZAMBIRI

Onerani vidiyo yakuti Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? pa jw.org.

Zimene Baibulo Limanena

Mulungu sanatilenge kuti tizivutika.

Iye amafuna kuti tizisangalala ndi moyo.

“Palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo, komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”​MLALIKI 3:12, 13.

Mulungu anapatsa anthu awiri oyambirira zinthu zofunika kuti asamavutike.

Iye sankafuna kuti iwo komanso mbadwa zawo azivutika.

“Mulungu anawadalitsa n’kuwauza kuti: ‘Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.’”​GENESIS 1:28.

Anthu awiri oyambirira anasankha kusamvera Mulungu.

Zimenezi zinachititsa kuti iwowo ndiponso mbadwa zawo zonse ayambe kukumana ndi mavuto aakulu.

‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’​AROMA 5:12. *

Mulungu sanatilenge kuti tizichita zinthu popanda malangizo ake.

Mwachitsanzo, Mulungu sanatilenge kuti tizikhala m’madzi. Mofanana ndi zimenezi, sitinalengedwe kuti tizidzilamulira tokha.

“Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”​YEREMIYA 10:23.

Mulungu safuna kuti tizivutika.

Iye amafuna kuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti tizipewa mavuto.

“Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga! Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje.”​YESAYA 48:18.

^ ndime 17 M’Baibulo, mawu akuti “tchimo” samangotanthauza kuchita zinthu zoipa koma amatanthauzanso mmene anthu tonse tilili chifukwa cha uchimo umene tinatengera.