GALAMUKANI! Na. 2 2016 | Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?
Pali chifukwa chabwino chomwe chachititsa kuti Baibulo lifalitsidwe ndi kusindikizidwa m’zinenero zambiri kuposa buku lina lililonse.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Baibulo Langokhala Buku Labwino Basi?
Nanga n’chifukwa chiyani anthu analolera kuika moyo wawo pangozi chifukwa cha Baibulo?
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Zimene Mungachite Mwana Akatsala Pang’ono Kutha Msinkhu
Mfundo 5 za m’Baibulo zomwe zingathandize makolo panthawi imene mwana wawo akukumana ndi mavuto chifukwa cha kusintha kwa thupi lake.
KUCHEZA NDI ANTHU
Katswiri Woona za Mmene Ana Osabadwa Amakulira Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Pulofesa Yan-Der Hsuuw ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, koma anasintha maganizo atakhala wasayansi wochita kafukufuku.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Nkhawa
Nkhawa zothandiza ndi zabwino; nkhawa zoipa zimatibweretsera mavuto. Kodi mungatani kuti nkhawa zisamakulepheretseni kukhala osangalala?
Mbalame Zokongola Kwambiri
Werengani nkhaniyi kuti muzidziwe bwino mbalame zokongolazi.
ZOCHITIKA PADZIKOLI
Nkhani Zokhudza Anthu
Kafukufuku yemwe wachitika posachedwapa akusonyeza kuti Baibulo lili ndi nzeru zothandiza.
Zina zimene zili pawebusaiti
Khalidwe Langa Loipa Linanditopetsa
Dmitry Korshunov anali chidakwa, koma kenako anayamba kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Kodi n’chiyani chimene chinamuthandiza kuti asinthe khalidwe lake n’kukhala munthu wosangalala
Zinthu Zinayamba Kuyenda Bwino
Donald, yemwe m’mbuyomo anamangidwa, anafotokoza mmene kuphunzira Baibulo kunamuthandizira kuti adziwe Mulungu, asinthe moyo wake komanso kuti azikonda kwambiri mkazi wake.