MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?
Zimene Zimachitika Munthu Akakhala ndi Nkhawa
Munthu akapanikizika kapena akakhala ndi mantha, ubongo umachititsa kuti thupi litulutse mahomoni osiyanasiyana. Zimenezi zimachititsa kuti mtima uyambe kugunda kwambiri, magazi ayambe kuthamanga, kapumidwe kasinthe komanso kuti minofu ikungike. Izi zikamachitika, thupi limakhala litakonzekera kuchita chilichonse. Manthawo akachepa, thupi limayambanso kubwerera m’chimake.
MANTHA ABWINO NDI OIPA
Tonsefe mwachibadwa timachita mantha ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tikonzekere kulimbana ndi zina zake. Mantha amayambira muubongo. Mantha abwino amatithandiza kuti tichite zinthu mwamsanga. Angatithandizenso kukwaniritsa zolinga zathu komanso kuchita bwino zinazake, monga kukhoza mayeso, intavyu kapena kuchita bwino masewera ena ake.
Komabe kukhala ndi mantha komanso wopanikizika kwa nthawi yaitali n’koopsa. Thupi likamangokhala lokonzeka kulimbana ndi mavuto nthawi zonse, munthu akhoza kumakhala wotopa, wokhumudwa komanso akhoza kusokonekera maganizo. Akhozanso kusintha khalidwe komanso mmene amachitira zinthu ndi ena. Kukhala wopanikizika kungachititsenso kuti munthu ayambe kumwa mowa mwauchidakwa, kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita zinthu zina zoipa. Kupanikizika kukhozanso kupangitsa munthu kudwala matenda a maganizo, kutopa kwambiri komanso kufuna kudzipha.
Kukhala wopanikizika komanso wamantha kwa nthawi yaitali, kungayambitse nkhawa ndipo kungakhudze mmene thupi lanu limagwirira ntchito.