Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kodi Dzikoli Lidzathadi?

Kodi Dzikoli Lidzathadi?

Lemba la 1 Yohane 2:17 limati: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” Kodi mawu akuti “dziko” palembali akutanthauza chiyani? Popeza Baibulo limanena kuti dzikoli lidzawonongedwa, kodi zimenezi zidzachitika bwanji ndipo zidzachitika liti?

Kodi mawu akuti “dziko” omwe ali pa 1 Yohane 2:17 akutanthauza chiyani?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

Lembali silikunena za dziko lapansi lenilenili chifukwa anthu ndi amene amakhala ndi ‘zilakolako’ zoipa. Mawu akuti “dziko” akutanthauza anthu amene safuna kumvera Mulungu ndipo Baibulo limati ndi adani ake. (Yakobo 4:4) Limanenanso kuti Mulungu adzaweruza anthu amenewa “kuti alandire chilango cha chiwonongeko chamuyaya.” (2 Atesalonika 1:7-9) Koma anthu amene amatsatira zimene Yesu Khristu ananena n’kumayesetsa kusakhala “mbali ya dzikoli,” adzalandira moyo wosatha.—Yohane 15:19.

N’chifukwa chake lemba la 1 Yohane 2:17 limamaliza n’kunena kuti: “Wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.” Koma kodi adzakhala kuti? Lemba la Salimo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

“Musamakonde dziko kapena zinthu za m’dziko. Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate.”1 Yohane 2:15.

Kodi Mulungu adzawononga bwanji anthu oipa?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

Baibulo limanena kuti Mulungu adzayamba ndi kuwononga zipembedzo zabodza. Limanena kuti zipembedzo zimenezi zili ngati hule ndipo zimatchedwa “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:1-5; 18:8) Mulungu adzawononga zipembedzozi chifukwa ndi zosakhulupirika. M’malo molambira Mulungu yekha, zimagwirizana kwambiri ndi andale. Ndiye Mulungu adzagwiritsa ntchito andale omwewo kuti aziwononge. N’chifukwa chake Baibulo limati: ‘Adzadana nalo hulelo ndipo adzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Adzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.’—Chivumbulutso 17:16.

Kenako, Mulungu adzathana ndi andalewo, omwe Baibulo limawatchula kuti “mafumu a dziko lonse lapansi.” Adzawononganso anthu onse oipa ndipo zonsezi zidzachitika pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Nkhondo imeneyi imatchedwanso kuti “Haramagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16.

“Bwerani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi, amene mwakhala mukutsatira zigamulo zake. Yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa. Mwina mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.”Zefaniya 2:3.

Kodi Mulungu adzawononga liti anthu oipa?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

Mulungu adzawononga anthu oipa akadzaona kuti uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu walalikidwa mokwanira. Ufumu umenewu udzalowa m’malo mwa maboma a anthu. (Danieli 7:13, 14) Yesu Khristu anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Choncho, ntchito yolalikira ndi “chizindikiro” chakuti mapeto ayandikira ndipo imasonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo. Palinso zizindikiro zina monga nkhondo, zivomerezi, njala komanso matenda.—Mateyu 24:3; Luka 21:10, 11.

Baibulo limanenanso kuti makhalidwe a anthu adzafika poipa kwambiri “m’masiku otsiriza.” Mwachitsanzo, limati: “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvera makolo, . . . osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” *2 Timoteyo 3:1-5.

Dziko lapansili liwonongedwa posachedwapa.—1 Yohane 2:17

Kungochokera m’chaka cha 1914 pamene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inayamba, zinthu padzikoli zakhala zikuipiraipira. Komanso kuyambira chaka chimenecho, uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu wakhala ukulalikidwa padziko lonse. A Mboni za Yehova amayesetsa kugwira ntchito yolalikira za Ufumu umenewu. N’chifukwa chake magazini yawo imene ndi yodziwika kwambiri imakhala ndi mutu wakuti, Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova.

“Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”Mateyu 25:13.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 9 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pa webusaiti ya www.jw.org/ny.