MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE
Kodi Mungatani Ngati Zimakuvutani Kupepesa?
VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
Tiyerekeze kuti inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu mwasemphana maganizo pa nkhani inayake. Ndiyeno inuyo mukunena kuti: ‘Sindingapepese. Nanga vuto ndi ineyo?’
Kenako mukuganiza zongonyalanyaza nkhaniyo, komabe inuyo komanso mnzanuyo mudakali chikwiyire. Mukuona kuti mutati mupepese, nkhaniyo ikhoza kutha koma kungoti zikukuvutani kupepesa.
ZIMENE ZIMACHITITSA
Kunyada. Mwamuna wina dzina lake Charles * ananena kuti: “Nthawi zina zimakhala zovuta kuti upepese chifukwa umaona kuti ukapepesa uoneka ngati wopusa.” Choncho, kunyada kungachititse kuti munthu asavomereze kuti walakwa.
Mmene mumaganizira. Anthu ena amaganiza kuti m’pomveka kupepesa akazindikira kuti alakwitsadi zinthu. Mkazi wina dzina lake Jill anati: “Sizindivuta kupepesa ndikazindikira kuti ineyo ndi amene ndili wolakwa. Koma ndikazindikira kuti amene ndalakwitsa si ine ndekha, zimandivuta kupepesa. Ndimaona kuti sindingathe kupepesa ndikaona kuti tonse ndi amene tachititsa kuti zinthu zisokonekere.”
Anthu ambiri safuna kupepesa zikakhala kuti mnzawoyo ndi amene wawalakwira. Mwamuna wina dzina lake Joseph, ananena kuti: “Ukaona kuti iweyo sunalakwe, supepesa pofuna kumusonyeza mnzakoyo kuti ndiwe wosalakwa.”
Mmene munaleredwera. Ngati munakulira m’banja limene anthu ake sankapepesana, zimakhalanso zovuta kuti muvomereze zimene mwalakwitsa. Choncho ngati simunkachita zimenezi muli mwana, zingakhaledi zovuta kuti muzipepesa.
ZIMENE MUNGACHITE
Muziganizira mnzanuyo. Mungachite bwino kumakumbukira nthawi imene munthu wina anakupepesani komanso mmene Luka 6:31.
munamvera. Muyenera kuti munamva bwino mumtima. Choncho mkazi kapena mwamuna wanu angamve bwino ngati mutam’pepesa. Ngakhale zitakhala kuti inuyo mukuona kuti simunalakwitse, mungachitebe bwino kupepesa chifukwa mnzanuyo wakhumudwa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti mtima wake ukhale m’malo.—Lemba lothandiza:Muziganizira banja lanu. Musamaone kuti kupepesa n’kupusa, koma muziona kuti kungathandize banja lanu kuti liziyenda bwino. Lemba la Miyambo 18:19 limanena kuti munthu amene wakwiya chifukwa choti munthu wina wamukhumudwitsa, safuna kumvanso maganizo a mnzake moti “amaposa mzinda wolimba.” Ngati aliyense akuona kuti sanalakwitse, zimakhala zovuta kuti mukambirane n’kuthetsa nkhaniyo. Mukapepesa zimathandiza kuti nkhaniyo isakule. Mukamachita zimenezi, mumasonyeza kuti mumaona kuti banja lanu ndi lofunika kwambiri.—Lemba lothandiza: Afilipi 2:3.
Muzipepesa mwamsanga. Anthu ambiri zimawavuta kuti apepese akazindikira kuti onse analakwitsa. Ngati mkazi kapena mwamuna wanu walakwitsa, si bwino kusiya kumuchitira zinthu zabwino. Choncho ndi bwino kuti muyambe ndinu kupepesa m’malo moganiza kuti pakapita nthawi, nkhaniyo izizira. Ngati mutayamba ndinu kuchita zimenezi, mnzanuyo sangavutike kuti akupepeseni. Ngati nthawi zonse mutamapepesa mukhoza kuzolowera ndipo simungamaonenso kuti kupepesa n’kovuta.—Lemba lothandiza: Mateyu 5:25.
Muzipepesa kuchokera pansi pa mtima. Kuyesetsa kufotokoza zimene zakuchititsani kuti muchite zinazake si kupepesa. Komanso sikungakhale kupepesa ngati mutalankhula monyoza kuti, “Pepanitu sindimadziwa kuti zimene ndachitazi zikukhudwitsani.” Ndi bwino kuvomereza kuti mwalakwitsa komanso kuti mwakhumudwitsa mnzanuyo m’malo modziikira kumbuyo. Muyenerabe kuchita zimenezi kaya mnzanuyo wakhumudwa kapena ayi.
Muzivomereza mukalakwitsa. Ndi bwino kukhala wodzichepetsa n’kumadziwa kuti nthawi zina mukhoza kulakwitsa. Ndipo palibe munthu yemwe amachita zabwino zokhazokha osalakwitsa. Ngakhale mutaona kuti simunalakwitse chilichonse, muzikumbukira kuti nthawi zina timaona zinthu molakwika. Baibulo limanena kuti: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.” (Miyambo 18:17) Sizingakuvuteni kupepesa ngati mumadziwa kuti simungachite zinthu zonse molondola.
^ ndime 7 Tasintha mayina m’nkhaniyi.