Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kukhala Ololera

Kukhala Ololera

Anthu akakhala ololera amakhululukirana mosavuta ndipo amakhala mwamtendere. Koma kodi kulolera kuyenera kukhala ndi malire?

Kodi chofunika n’chiyani kuti munthu akhale wololera?

ZIMENE ZIKUCHITIKA MASIKU ANO

Anthu ambiri salolerana. Amalimbana kwambiri chifukwa chosiyana mitundu, mayiko kapena zipembedzo.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Vuto limeneli linaliponso pamene Yesu anali padzikoli. Mwachitsanzo, Ayuda ankadana kwambiri ndi Asamariya. (Yohane 4:9) Amuna ankaona kuti akazi ndi otsika kwambiri. Nawonso atsogoleri achipembedzo achiyuda ankanyoza anthu wamba. (Yohane 7:49) Koma maganizo a Yesu anali osiyana kwambiri ndi a anthu onsewa. Izi zinachititsa kuti ena azimutsutsa n’kumanena kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa ndi kudya nawo limodzi.” (Luka 15:2) Yesu sanabwere kudzaweruza anthu koma kudzawathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Choncho iye anali wachifundo, woleza mtima komanso wololera. Chikondi n’chimene chinkamulimbikitsa kusonyeza makhalidwe amenewa.—Yohane 3:17; 13:34.

AYesu sanabwere kudzaweruza anthu koma kudzawathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Choncho iye anali wololera

Chikondi chimathandiza kuti tizikhala ololera n’kumakhala bwino ndi anzathu ngakhale kuti amalakwitsa zina ndi zina. Paja lemba la Akolose 3:13 limati: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”

“Koposa zonse, khalani okondana kwambiri, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”1 Petulo 4:8.

Kulolera Kuyenera Kukhala ndi Malire

ZIMENE ZIKUCHITIKA MASIKU ANO

M’dziko lililonse mumakhala malamulo oti anthu azitsatira. Izi zimachititsa kuti anthuwo azikhala ndi malire ochitira zinthu.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

‘Chikondi sichichita zosayenera.’ (1 Akorinto 13:5) Yesu anali wololera koma sankalekerera makhalidwe oipa monga chinyengo ndipo ankadzudzula anthu amene anali ndi makhalidwe amenewa. (Mateyu 23:13) Iye anati: “Amene amachita zinthu zoipa amadana ndi kuwala.”—Yohane 3:20.

Nayenso mtumwi Paulo analemba kuti: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.” (Aroma 12:9) Iye ankayesetsa kutsatira mfundo imeneyi. Mwachitsanzo, Akhristu achiyuda atayamba kusala Akhristu amitundu ina, Paulo anadzudzula Ayuda anzakewo mokoma mtima. (Agalatiya 2:11-14) Iye ankadziwa kuti “Mulungu alibe tsankho” ndipo sangasangalale kuona anthu ake akusalana.—Machitidwe 10:34.

A Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo. (Yesaya 33:22) Choncho salekerera zoipa mumpingo. Safuna kuti mpingo usokonezeke chifukwa cha anthu amene satsatira malamulo a Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, iwo amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”—1 Akorinto 5:11-13.

“Inu okonda Yehova danani nacho choipa.”Salimo 97:10.

Kodi Mulungu alolera kuti zoipa zizichitikabe?

ZIMENE ANTHU AMBIRI AMAKHULUPIRIRA

Mwachibadwa anthu amachita zoipa. Choncho zoipa sizidzatha mpaka kalekale.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Popemphera kwa Yehova, Habakuku ananena kuti: “N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga? Ndipo n’chifukwa chiyani pali mikangano ndi kumenyana?” (Habakuku 1:3) Mulungu anakhazika mtima m’malo mneneriyu pomutsimikizira kuti adzaweruza oipa. Anamuuza kuti adzakwaniritsa lonjezo limeneli ndipo sadzachedwa.—Habakuku 2:3.

Panopa, anthu onse ochita zoipa ali ndi mpata woti asinthe. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa anati: “Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu aliyense wochimwa? Kodi sindisangalala kuti munthu wochimwayo abwerere kusiya njira zakezo ndi kukhalabe ndi moyo?” (Ezekieli 18:23) Anthu amene amamvera Yehova n’kusiya njira zawo zoipa ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti lemba la Miyambo 1:33 limati: “Munthu wondimvera adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”

“Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”Salimo 37:10, 11.