GALAMUKANI! July 2013 | Kodi Zionetsero Zimathetsadi Mavuto M’dziko?
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu akumachita zionetsero komanso njira yeniyeni yothetsera mavuto padzikoli.
Zochitika Padzikoli
Muli nkhani monga izi: kusalana polemba ntchito komanso lamulo latsopano lokhudza makampani opanga fodya ku Australia.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Zimene Mungachite Mwana Akayamba Kuvuta
Kodi mungachite chiyani mwana wanu atayamba kuvuta? Baibulo lili ndi malangizo omwe angakuthandizeni kuthana ndi vuto limeneli.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Zionetsero Zimathetsadi Mavuto M’dziko?
Zionetsero zikhozadi kuchititsa kuti zinthu zisinthe. Koma kodi zingathandizedi kuthetsa zinthu zopanda chilungamo, ziphuphu, ndi kuponderezana?
NKHANI YAPACHIKUTO
Ndinaona Kuti Padzikoli Palibe Chilungamo
N’chifukwa chiyani m’nyamata wina wa ku Northern Ireland anasintha maganizo a m’mene mtendere weniweni ungabwerere padzikoli?
Mphaka Wam’tchire Wakuchipululu
Kodi munamvapo za mphaka wam’tchire wakuchipululu? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri za mphakayu komanso zimene zimachititsa kuti zizikhala zovuta kudziwa kumene wadutsa.
ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la Azerbaijan
Anthu a ku Azerbaijan amadziwika kuti ndi okonda kulandira alendo. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri zokhudza dziko lawo komanso chikhalidwe chawo.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Ufumu wa Mulungu
Anthu ena amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu uli m’mitima ya okhulupirira komanso kuti anthu ndi amene adzabweretse Ufumu wa Mulungu. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?
KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Gologolo wa Ubongo Wodabwitsa Kwambiri
Kodi zimatheka bwanji kuti kanyama kameneka kakhalebe ndi moyo m’madera ozizira kwambiri?
Zina zimene zili pawebusaiti
Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2
Werengani zimene achinyamata ena anachita kuti athe kupirira matenda aakulu komanso kuti azikhalabe osangalala.
Nkhani ya Ana a Yakobo
Kodi muyenera kutani ngati m’bale wanu kapena mnzanu wapeza chinthu chimene inuyo mumachifuna kwambiri?