Zochitika Padzikoli
Nyanja ya Gulf of Mexico
M’mwezi wa April chaka cha 2010, chitsime cha mafuta chinaphulika, zomwe zinachititsa kuti mafuta ambirimbiri ataikire m’nyanja ya Gulf Of Mexico kwa pafupifupi miyezi itatu. Akatswiri ena ofufuza anapeza kuti patadutsa miyezi iwiri ndi hafu ngoziyo itachitika, mafuta anali atachepa. Iwo akuganiza kuti mabakiteriya ndi omwe ankadya mafutawo. Koma akatswiri ena amanena kuti zimenezi sizoona. Iwo akuganiza kuti mafuta ambiri anamira pansi pa madzi.
Russia
Kafukufuku wina wasonyeza kuti anthu 59 pa 100 alionse a ku Russia, azaka kuyambira 18 mpaka 35, amakhulupirira kuti “nthawi zina munthu amafunika kuchita zinthu zimene anthu amaona kuti n’zosayenera ngati akufuna kuti zizimuyendera.” Zotsatira za kafukufukuyu zinatuluka m’nyuzipepala ya Rossiiskaya Gazeta.
Peru
Akatswiri ofufuza zinthu zakale ku Peru apeza chitsononkho cha chimanga chakale kwambiri. Malinga ndi zimene apezazi, iwo akuganiza kuti anthu amene ankakhala kumpoto kwa dziko la Peru zaka 3,000, zapitazo ankakazinga chimanga komanso kugaya ufa.
Italy
Wansembe wina wachikatolika m’chigawo cha Adria-Rovigo, dzina lake Lucio Soravito De Franceschi, ananena kuti akukhulupirira zoti njira yabwino youzira anthu uthenga ndi “kulankhula nawo pamasom’pamaso,” zomwe zikutanthauza kuti omwe ali ndi uthenga ayenera kupita kumene anthuwo amakhala. Iye ananena kuti: “Panopa m’malo modikira kuti nkhosa zibwere m’matchalitchi mwathu, tiyenera kumapita m’nyumba zawo.”
South Africa
Mtengo wa minyanga ya chipembere wakwera kwambiri moti anthu amene amagulitsa minyangayi mozembera boma, akumaigulitsa pa mtengo wa madola 65,000 pa kilogalamu. Akuti anthu ena amagwiritsa ntchito minyangayi ngati mankhwala. M’chaka cha 2011, ku South Africa kokha, zipembere zokwana 448 zinaphedwa ndi anthu opha nyama mozembera boma. Ku Ulaya, akuba akumathyola malo osungira zinthu zakale komanso malo ogulitsira malonda n’cholinga chokaba minyanga ya chipembere. Anthu enanso akuganiza kuti zipembere zimene zili m’malo osungira zinyama m’mayiko a ku Ulaya zikhozanso kuphedwa ndi anthu ofuna minyangayi.