Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Caucasus Dera Lamapiri Komanso Zilankhulo Zosiyanasiyana

Caucasus Dera Lamapiri Komanso Zilankhulo Zosiyanasiyana

TAYEREKEZANI kuti mwapita kudera linalake lalikulu kwambiri komanso lamapiri okhaokha. Mutafika, mukudabwa kuti kudera limenelo kuli anthu amitundu komanso zinenero zosiyanasiyana moti ngakhale anthu oyandikana midzi amalankhula zinenero zosiyana. Izi n’zimene akatswiri akale ofufuza za malo anapeza atafika kudera la Caucasus.

Derali lili pakati pa Nyanja Yakuda ndi ya Caspian ndipo zinthu monga zamalonda zimene zinkachitika m’derali zinachititsa kuti mukhale anthu a zikhalidwe zosiyanasiyana. Anthu a m’derali amadziwika kuti amalemekeza okalamba, amakonda kuvina komanso kuchereza alendo. Koma alendo okaona derali amachita chidwi kwambiri ndi kuchuluka kwa zinenero ndi zikhalidwe za anthu a kumeneko. Derali lili ndi zinenero zambiri kuposa madera ena a ku Europe.

Anthu a Zinenero Zosiyanasiyana

Cha m’ma 400  B.C.E., katswiri wina wa mbiri yakale wa ku Greece, dzina lake Herodotus ananena kuti: “Ku Caucasus kumapezeka anthu a mitundu yonse.” Komanso chaka cha 1 C.E. chitatsala pang’ono kufika, katswiri wina wa mbiri yakale wa ku Greece komweko, dzina lake Strabo, analemba nkhani zokhudza mafuko 70 a anthu a ku Caucasus. Fuko lililonse linali ndi chinenero chake komanso linkachita malonda m’tauni ya Dioscurias, dera lomwe masiku ano lili mu mzinda wa Sukhumi, mphepete mwa Nyanja Yakuda. Patadutsa zaka zambiri katswiri wina wa ku Roma, dzina lake Pliny Wamkulu, analemba kuti pochita malonda ku Dioscurias, Aroma ankafunika anthu 130 oti aziwamasulirira m’zinenero zosiyanasiyana.

Masiku ano ku Caucasus kuli mitundu ya anthu yoposa 50. Mtundu uliwonse uli ndi chikhalidwe chakechake. Ulinso ndi luso lakelake lopanga zinthu, lakamangidwe komanso lakavalidwe. M’derali muli zinenero pafupifupi 37 ndipo zinenero zina zimalankhulidwa ndi anthu ambiri pomwe zina ndi anthu a m’mudzi umodzi basi. Dera limene lili ndi zinenero zambiri ku Caucasus ndi dziko la Dagestan komwe kuli mitundu 30 ya anthu. Mpaka pano sizidziwika ngati pali kugwirizana pakati pa zinenero za anthu a ku Dagestan ndi za m’madera ena ku Caucasus.

Kodi mungakonde kudziwa zina mwa zinenero za m’dera la Caucasus? Pa Webusaiti ya Mboni za Yehova ya www.jw.org, pali mabuku m’zinenero zoposa 400, ndipo zina mwa zinenerozi ndi zomwe zimalankhulidwa ku Caucasus.