Baibulo Ndi Buku la Maulosi Olondola Gawo 8
“Ufumu Wanu Ubwere”
Ino ndi nkhani ya nambala 8 komanso yomalizira pa nkhani zofotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo zimene zakhala zikutuluka mu Galamukani! Nkhanizi zatithandiza kwambiri kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Tikukulimbikitsani kuganizira mofatsa mfundo zimene mwaphunzira m’nkhani zimenezi.
KWA zaka pafupifupi 2,000, anthu omwe amati ndi Akhristu akhala akupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, potengera zimene Yesu ananena. Iye anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:10.
Kodi ufumu umenewu ndi chiyani? Ndi boma la Mulungu la kumwamba ndipo lidzalowa m’malo maboma ena onse. Yesu Khristu ndi mfumu yosankhidwa ya Ufumu umenewu ndipo panopo akuchita chifuniro cha Mulungu kumwamba ndi padziko lapansi. (Danieli 2:44; 7:13, 14) Posachedwapa, Mulungu ayankha pemphero limeneli pothetsa zoipa ndi mavuto onse, n’kupulumutsa anthu osawerengeka omwe amamulambira mokhulupirika omwe Baibulo limawatchula kuti “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 10, 13-17) Kenako, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.
Kodi pali njira iliyonse yodziwira madalitso amene tidzapeze mu ulamuliro wa Khristu? Inde ilipo. Njira yake ndikuona zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Iye anachita zinthu zosonyeza kuti akufunitsitsa kuthetsa mavuto a anthu komanso kuti ali ndi mphamvu zochitira zimenezi. Tiyeni tione maulosi anayi a m’Baibulo ndiponso tione mmene Yesu anasonyezera
zimene adzachite padziko lonse monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.Ulosi woyamba:
“Yehova . . . akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:8, 9.
Kukwaniritsidwa kwake: Monga “Kalonga Wamtendere,” Yesu Khristu adzachititsa kuti padziko lapansi pakhale mtendere mpaka kalekale. Mu Ufumu wa Mulungu anthu a mitundu yonse adzakhala ogwirizana. Zimenezi zidzatheka chifukwa chakuti padzakhala ntchito yophunzitsa anthu padziko lonse komanso kuthetsa nkhondo.—Yesaya 2:2-4; 9:6, 7, 11:9.
Zimene mbiri imasonyeza:
Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti asamamenye nawo nkhondo, koma azikhala mwamtendere ndi anthu onse. Pa nthawi ina, wophunzira wake wina anafuna kugwiritsa ntchito chida kuti amuteteze, koma Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:51, 52) Yesu anafotokoza kuti Akhristu oona azidzadziwika chifukwa chokondana.—Yohane 13:34, 35.
Ulosi wachiwiri:
“Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.
Kukwaniritsidwa kwake: Ufumu wa Mulungu udzathetsa njala komanso mavuto onse amene amabwera chifukwa cha njala. Aliyense adzakhala ndi chakudya chabwino komanso chokwanira.
Zimene mbiri imasonyeza:
Yesu anasonyeza kuti ankachitira chifundo anthu anjala ndipo zimene anachita podyetsa khamu la anthu zinali zodabwitsa kwambiri. Ponena za zimene zinachitika nthawi ina, Baibulo limati: “[Yesu] analamula khamu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Pamenepo anatenga mitanda ya mkate isanu ija ndi nsomba ziwiri zija, n’kuyang’ana kumwamba ndi kupempha dalitso. Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija n’kupatsa ophunzirawo, ndipo iwonso anagawira khamulo. Chotero onse anadya n’kukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12. Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aang’ono.”—Mateyu 14:14, 19-21.
Ulosi wachitatu:
“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) “Maso a anthu akhungu adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva. Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.
Kukwaniritsidwa kwake: Ufumu wa Mulungu udzathetseratu matenda onse. Anthu osaona adzaona, ndipo ogontha adzamva ndi kulankhula. Palibe amene adzafunikire mankhwala ndipo sikudzakhala zipatala kapena madokotala.
Zimene mbiri imasonyeza:
Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu, ankachiritsa olumala komanso odwala matenda osiyanasiyana. Zimenezi zinasonyeza pang’ono pokha zimene adzachite padziko lonse akadzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.—Luka 7:22; 9:11.
Ulosi wachinayi:
Mulungu “adzameza imfa kwamuyaya.”—Yesaya 25:8.
Kukwaniritsidwa kwake: Khristu akamadzalamulira mu Ufumu wa Mulungu, “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi. (Yohane 5:28, 29) Yesu adzagonjetsa imfa, yomwe ndi mdani wathu wamkulu, ndipo zimenezi zidzachititsa kuti tikhale ndi moyo mpaka kalekale.—Salimo 37:29.
Zimene mbiri imasonyeza:
Katatu konse, Yesu anasonyeza kuti ali ndi mphamvu zoukitsa akufa. (Luka 7:11-15; 8:41-55; Yohane 11:38-44) Ndipo Yesu atafa, anthu pafupifupi 500 anachitira umboni kuti anaona Yesu ataukitsidwa.—1 Akorinto 15:3-8.
Nkhani 8 zimenezi, zafotokoza maulosi a m’Baibulo omwe akwaniritsidwa. Maulosi onsewa kuphatikizapo ena ambiri asonyeza kuti mfundo zimene zili m’Baibulo si nzeru za anthu. M’malomwake, maulosiwa atithandiza kuona kuti Baibulo linalembedwa ndi Mulungu. Kunena zoona pali umboni wokwanira wosonyeza kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.”—2 Timoteyo 3:16.
Chifukwa choti maulosi onse a m’Baibulo amakwaniritsidwa, sitikayikira zimene limanena kuti: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.