Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Posachedwapa Chisinthe N’chiyani?

Kodi Posachedwapa Chisinthe N’chiyani?

Kodi Posachedwapa Chisinthe N’chiyani?

“Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake.”

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

“Imfa sidzakhalaponso.”

ANTHU ena angaganize kuti zimene zafotokozedwa pamwambapa ndi zosatheka. Koma sitiyenera kukayika kuti zimenezi zidzachitika chifukwa amene analonjeza zimenezi si anthu andale. Iwo amangolonjeza zinthu zomwe sangazikwaniritse chifukwa alibe mphamvu zosintha zinthu padzikoli. Koma malonjezowa ndi odalirika chifukwa amapezeka m’Baibulo. *

Anthu ambiri amaganiza kuti Baibulo ndi buku lakale kwambiri ndipo limanena zinthu zimene sizigwirizana ndi zochitika za masiku ano. Kodi inunso mumaliona choncho? Ngati mumaganiza choncho, mungachite bwino kufufuza zimene Baibulo limanena. Mfundo ndi yakuti, Baibulo ndi buku lokhalo lomwe limafotokoza bwino mbiri ya anthu kuyambira pachiyambi. Mwachitsanzo, limafotokoza:

● Chimene chinachitika kuti anthu ayambe kuvutika.—Aroma 5:12.

● Zimene Mulungu wakonza kuti athetse mavutowa.—Yohane 3:16.

● Chifukwa chimene maboma sangakwanitse kusintha zinthu padzikoli.—Yeremiya 10:23.

● Chifukwa chimene tingakhulupirire kuti Mulungu adzakwanitsadi zimene analonjeza.—Yoswa 23:14.

Kodi mumakhulupirira kuti Mulungu adzathetsadi njala, nkhondo, matenda komanso imfa? Simungakayikire ngati mumakhulupiriranso kuti:

1. Mulungu ndi amene anatilenga.

2. Mulungu amasamala za ife.

3. Mulungu ali ndi mphamvu zotha kusintha zinthu padziko lapansi.

4. Mulungu akufunitsitsa kusintha zinthu padziko lapansi.

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira mfundo zinayi zimenezi? A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magazini ino, akukupemphani kuti muyambe kuphunzira nawo Baibulo kuti mupeze yankho la funso limeneli.

N’kutheka kuti muli ndi Baibulo koma mumaliwerenga mwa apo ndi apo kapena simuliwerenga n’komwe. Ndipotu anthu ambiri amene amawerenga Baibulo amanena kuti samvetsa zimene akuwerengazo. Ngatinso zili choncho ndi inu, tikukulimbikitsani kuti mupemphe a Mboni za Yehova kuti ayambe kukuphunzitsani Baibulo kwaulere. Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse anayamba kale kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komano kodi kuphunzira kwake kuziyenda bwanji?

Ngati mutalola, mlungu uliwonse a Mboni za Yehova akhoza kumabwera kunyumba kwanu kapena pamalo ena alionse amene inu mungafune kuti azikuphunzitsani Baibulo kwaulere. Kuphunzira Baibulo kudzakuthandizani kupeza mayankho a mafunso ngati awa: N’chifukwa chiyani timavutika? N’chifukwa chiyani maboma alibe mphamvu yosintha zinthu padzikoli? Kodi ufumu wa Mulungu n’chiyani? Ndipo udzakwanitsa bwanji kuchita zimene maboma akulephera? *

Ngati mukufuna kudziwa ubwino wophunzira Baibulo, funsani a Mboni za Yehova a m’dera lanu kapena fufuzani pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org. Komanso mungalembe kalata ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 m’magazini ino.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Malonjezo amene ali pamwambawa amapezeka pa Yesaya 2:4; Yesaya 33:24 ndi Chivumbulutso 21:4.

^ ndime 18 Werenganinso nkhani yakuti “Zimene Baibulo Limanena: Ndani Angakwanitse Kusintha Zinthu Padzikoli?” patsamba 26 ndi 27 la magazini ino.