Kulankhulana ndi Anthu
Kulankhulana ndi Anthu
● Tayerekezerani zochitika izi: Sam amakhala kudera lina lakumudzi ku United States. Kwa zaka zambiri anthu akhala akumunena kuti ndi wotsalira chifukwa amakana kugwiritsa ntchito zinthu zamakono zolankhulirana ndi achibale komanso anzake. Aliyense, kuphatikizapo ana ake, akunena kuti akufuna azigwiritsa ntchito zipangizozi. Sam akuuza mwana wake wamkazi wazaka 16 kuti: “Kale zinali bwino chifukwa anthu ankalankhulana pamasom’pamaso.”
Koma patapita nthawi, Sam akusintha maganizo ake pa nkhaniyi. Iye akuganizira za anthu amene wakhala asanalankhulane kapena kuonana nawo kwa zaka zambiri. Akuganiziranso za achibale ake amene amakhala otanganidwa kwambiri moti iye amaona kuti sangapeze mpata wolankhulana nawo. Sam akulankhula mumtima mwake kuti: ‘Ngati ndikufuna kuti ndizilankhulana ndi anthu amenewa, ndikufunika kupeza zipangizo zamakono.’ Tsopano Sam, yemwe poyamba amaoneka kuti ndi wotsalira uja akuganiza zoikitsa telefoni m’nyumba mwake.
Tsopano yerekezerani kuti muli m’chaka cha 2012 ndipo muli ndi Nathan, mdzukulu wa Sam. Nathan wangomaliza kumene kulankhula ndi anzake awiri, Roberto ndi Daniela, omwe anasamukira kudziko lina zaka 10 zapitazo. Nathan akudabwa kwambiri ndi mmene nthawi yafulumirira kuchokera pamene anzakewo anasamuka.
Kwa zaka zambiri, Nathan wakhala akugwiritsa ntchito foni kulankhulana ndi abale ake komanso anzake amene anasamukira madera akutali. Koma tsopano zikuoneka kuti aliyense kuphatikizapo ana a Nathan, omwe ndi achinyamata, akugwiritsa ntchito Intaneti pocheza ndi anzawo.
Anthu ambiri amaona kuti Nathan ndi wotsalira chifukwa amakana kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono zolankhulira ndi anthu. Iye akunena mumtima mwake kuti: “Kale zinali bwino chifukwa anthu ankalankhulana pafoni n’kumamva zimene wina akulankhula.” Komabe Nathan akusintha maganizo pa nkhaniyi. Iye akuti: ‘Ngati ndikufuna kumacheza ndi anthu onsewa, ndiyenera kumagwiritsa ntchito zipangizo zamakono.’
Kodi munayamba mwaganizapo zochita zimene Nathan akuganiza? Mwachibadwa anthufe timafuna kucheza ndi anzathu. (Genesis 2:18; Miyambo 17:17) Popeza kuti masiku ano anthu ambiri akumacheza pogwiritsa ntchito malo ochezera a pa Intaneti, kodi muyenera kudziwa chiyani za malo amenewa?