Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu wa Gogomole

Mutu wa Gogomole

Kodi Zinangochitika Zokha?

Mutu wa Gogomole

● Munthu akangomenyetseka mutu pang’ono, amamva kuwawa ndipo ubongo umatha kusokonezeka. Koma mbalame ya gogomole imatha kumenyetsa mutu wake kwambiri pojompha makungwa a mtengo koma osasokoneza mutu wake. Kodi mbalame imeneyi imatha bwanji zimenezi?

Taganizirani izi: Akatswiri ofufuza apeza zinthu zinayi zimene zimathandiza mbalameyi kuti ubongo wake usasokonezeke:

1. Ili ndi mlomo wamphamvu koma wotha kupindika

2. Ili ndi kamnofu kolimba ngati fupa komanso kotamuka kamene kanakuta ubongo wake

3. Ili ndi fupa kumbali ina ya mutu wake lokhala ndi timabowotimabowo

4. Ili ndi timadzi tinatake pakati pa chigaza ndi ubongo wake

Zinthu zonsezi zimathandiza kuti mbalameyi isavulale ikamajompha mtengo, moti imatha kujompha mtengo mofulumira kwambiri mwina maulendo 22 pa sekondi imodzi yokha.

Potengera mutu wa mbalameyi, asayansi apanga chinthu chosungiramo katundu chomwe ngakhale chitamenyetseka mwamphamvu chotani, katundu wamkatimo sangawonongeke. Ngati akatswiriwo atapitiriza kugwiritsa ntchito luso limeneli akhoza kupanga zinthu zina zolimba kwambiri. Mwachitsanzo, akhoza kupanga kabokosi kosungiramo kachipangizo kena ka mundege kamene kamajambula zochitika ndege ikamauluka. Kachipangizoka kamathandiza kuti ngati ndegeyo itachita ngozi adzadziwe kuti chinachitika n’chiyani. Kim Blackburn, yemwe ndi injiniya wa pa yunivesite ya Cranfield ku United Kingdom, ananena kuti zimene akatswiri akafukufuku apeza zokhudza mutu wa mbalame ya gogomole “ndi chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti chilengedwe n’chogometsa kwambiri chifukwa chimatha kukhala ndi zinthu zoyenerera zothandiza kuchita zinthu zimene zingaoneke zosatheka.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mbalame ya gogomole ikhale ndi mutu wogometsa chonchi, kapena ndi umboni wakuti pali winawake wanzeru amene anailenga?

[Chithunzi patsamba 19]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

1

2

3

4

[Mawu a Chithunzi patsamba 19]

Redheaded woodpecker: © 2011 photolibrary.com