Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Kodi Zithunzizi Zikusiyana Pati?

Kodi mungatchule zinthu zitatu zimene zikusiyana pakati pa chithunzi A ndi chithunzi B? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 25:23, 30, 31, 37; 30:1-7; Levitiko 24:5, 6.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. Kodi chithunzi cholondola n’chiti, A kapena B?

KAMBIRANANI:

Kodi ansembe ankafunika kuchita chiyani asanayambe kutumikira m’chihema chokumanako?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Ekisodo 30:17-21.

Ngati mukufuna kusangalatsa Yehova, kodi muyenera kumaona bwanji nkhani ya ukhondo? Kuwonjezera pa kusamalira thupi lanu, kodi mungasonyezenso bwanji kuti ndinu waukhondo?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani 1 Akorinto 6:9-11; 2 Akorinto 7:1.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Aliyense m’banja mwanu afufuze za “Malo Oyera” a m’chihema chokumanako. (Aheberi 9:2) Kenako aliyense afotokoze mfundo yatsopano imene wapeza.

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 119:105; 141:2; Mateyu 4:4; Yohane 4:34; Chivumbulutso 8:4.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 9 YEREMIYA

MAFUNSO

A. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya kulemba mabuku anayi a m’Baibulo ati?

B. Zoona kapena zabodza? Yeremiya sanakwatire moyo wake wonse.

C. Malizitsani mawu a Yeremiya awa: “Mumtima mwangamu, mawu [a Mulungu] anali ngati . . . ”

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa Anakhala ndi moyo

cha m’ma 650 B.C.E.

kwa Adamu Baibulo linamalizidwa

kulembedwa

[Mapu]

Ankakhala ku Yerusalemu. Anapita ku mtsinje wa Firate ndiponso ku Iguputo—Yeremiya 13:1-9; 43:8-13.

IGUPUTO

Mtsinje wa Firate

Yerusalemu

YEREMIYA

ANALI NDANI?

Anasankhidwa kukhala mneneri asanabadwe. (Yeremiya 1:1-5) Yeremiya anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zoposa 65. Ngakhale kuti Yeremiya ankadziona kuti ndi mwana komanso sangathe kulankhula, Yehova anamuuza kuti: “Usachite mantha . . . , ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’”—Yeremiya 1:6-8.

MAYANKHO

A. 1 Mafumu, 2 Mafumu, Yeremiya, ndi Maliro.

B. Zoona.—Yeremiya 16:1-4.

C. “. . . moto woyaka umene autsekera m’mafupa anga.”—Yeremiya 20:9.

Anthu ndi Mayiko

5. Dzina langa ndi Geoffrey. Ndili ndi zaka 9 ndipo ndimakhala ku Fiji. Kodi ku Fiji kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 500; 2,500 kapena 10,500?

6. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ineyo ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Fiji.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 27

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 ndi 31

1. Chiwerengero cha nyale zoyenera kukhala pa choikapo nyale.

2. Chiwerengero cha mikate yachionetsero.

3. Nyanga ziyenera kutulukira kuchokera paguwa la nsembe.

4. A.

5. 2,500.

6. D.