Kodi Zipembedzo Zikuthandiza Kuti Anthu Azikhala Mwamtendere?
Kodi Zipembedzo Zikuthandiza Kuti Anthu Azikhala Mwamtendere?
ANTHU ena amanena kuti tchalitchi cha Holy Sepulchre chomwe chili ku Yerusalemu, ndi malo opatulika kwambiri kuposa malo ena alionse. Tchalitchichi chinamangidwa pamalo amene anthu amakhulupirira kuti “m’pamene Khristu anaikidwa m’manda komanso kuukitsidwa.” Koma masiku ano, patchalitchichi pamachitika zinthu zambiri zachiwawa ndi zankhanza. Ansembe ochokera m’matchalitchi 6 achikhristu akhala akumenyanirana tchalitchicho. M’zaka zaposachedwapa udaniwu unakula kwambiri moti pa nthawi ina apolisi okhala ndi mfuti analowererapo pofuna kukhazikitsa bata, ndipo tchalitchicho chinakhala m’manja mwawo kwakanthawi.
Chipembedzo Chakhala Chikulimbikitsa Nkhondo Kuyambira Kalekale
Zimene zakhala zikuchitika pa tchalitchichi ndi chitsanzo chimodzi chabe cha zinthu zachiwawa komanso nkhondo zimene zipembedzo zakhala zikuchita kuyambira kalekale. Pofotokoza nkhondo zimene zakhala zikuchitika posachedwapa m’mayiko osiyanasiyana, buku lina linati: “Kuchokera ku Indonesia mpaka ku Northern Ireland, ku Middle East mpaka ku Kashmir, ku India mpaka ku Nigeria, kumayiko a ku Balkan mpaka ku Sri Lanka, Akhristu, Abuda, Ayuda, Ahindu, Asilamu ndi Asikhi amanena kuti sikulakwa kumenyana ndi anthu amene amadana ndi chipembedzo ndiponso chikhulupiriro chawo.”—Violence in God’s Name.
Ngakhale zili choncho, zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti kukhala mwamtendere komanso mogwirizana n’kofunika kwambiri. Ndipo kwa zaka zambiri, zakhala zikuphunzitsa anthu kuti azikondana komanso aziona kuti moyo wa munthu ndi wopatulika. Ndiyeno kodi n’chifukwa chiyani panopa zipembedzo zikuchita zinthu zosokoneza mtendere? Anthu amene ali ndi mtima wofunadi kulambira Mulungu ayenera kuganizira funso limeneli mwakuya.