Muzikhala ndi Nthawi Yochita Zinthu Zofunika Kwambiri?
Muzikhala ndi Nthawi Yochita Zinthu Zofunika Kwambiri?
“Nthawi yotsalayi yafupika.”—1 Akorinto 7:29.
MUNTHU wina, dzina lake Michael LeBoeuf, analemba m’buku lake kuti: “Munthu akamajowajowa m’madzi sizitanthauza kuti akusambira.”—Working Smart.
M’mawu ena, pali kusiyana pakati pa kutanganidwa ndi kuchita zinthu zaphindu. Ganizirani zimene mwachita mlungu wapitawu. Kodi nthawi yanu munaigwiritsa ntchito bwanji? Kodi munatanganidwa ndi chiyani? Kodi mukuona kuti mufunika kusintha kuti muzithera nthawi yambiri pa zinthu zofunika?
Ganizirani zimene Yesu analosera zokhudza nthawi yathu ino. Iye ananena kuti pamene dongosolo la zinthu lino likufika kumapeto ndiponso pamene dziko latsopano la Mulungu likuyandikira, ophunzira ake adzakhala otanganidwa. Kodi anati adzatanganidwa ndi chiyani? Kulalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu [wa Mulungu].” Yesu ananenanso kuti anthu ambiri adzakhala otanganidwa moti sadzamvetsera uthengawo. Iye anati anthuwo adzatanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku. Yesu anawonjezeranso kuti anthu amene amanyalanyaza uthenga wa Ufumu adzawonongedwa.—Mateyo 24:14, 37-39; Luka 17:28-30.
Masiku ano, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 230. Ndipo mogwirizana ndi zimene Yesu analosera, anthu ambiri samvetsera, ndipo amanena kuti, ‘Tatanganidwa.’ Koma tikukupemphani kuti muzikhala ndi nthawi yophunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu. Tikukhulupirira kuti mukadziwa zinthu zabwino zimene Mulungu watisungira, mudzaona kuti kumvetsera ndiponso kutsatira uthenga wa m’Baibulo n’kofunika kwambiri ndipo sikutaya nthawi. *
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Mukafuna kudziwa zambiri, kaonaneni ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu, kapena lembani kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenerera patsamba 5 la magazini ino. Mungagwiritsenso ntchito Intaneti pa adiresi iyi: www.jw.org.