“Ndikupempha Kuti Mundithandize”
“Ndikupempha Kuti Mundithandize”
● Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico inalandira kalata kuchokera kwa mayi wina amene amagwira ntchito pasukulu inayake ya anthu olumala. Iye anati: “Mayi anga anamwalira pa May 9. N’zovuta kufotokoza chisoni chimene ndinali nacho. Miyezi ingapo asanamwalire, ndinafufuza kuntchito kwanga nkhani yokhudza imfa komanso zimene munthu angachite kuti asakhale ndi chisoni kwambiri wachibale wake akamwalira. Ndinkaganiza kuti zimenezi zindithandiza, koma sizinandithandize.”
Kenako, mayiyo anapemphera kwa Mulungu kuti, “Ndikupempha kuti mundithandize.” Iye anati: “Usiku wa tsiku limeneli ndinawerenga kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Kabukuka kanandithandiza kwambiri moti ndinkangoona ngati alembera ineyo. Kabukuka kanafotokoza kuti kulira si kulakwa. Pamutu wakuti ‘Kodi Ndingakhale Motani ndi Chisoni Changa?’ Kabukuka kamanena kuti: ‘Musachepetse phindu la pemphero. . . . Chithandizo chimene Mulungu amapereka chilidi chikondi chothandiza. . . . Zoona, chithandizo chaumulungu sichimachotsa kupweteka, koma chingakuchititse kukhala kosavuta kupirira. Zimenezo sizitanthauza kuti simudzaliranso kapena kuti mudzaiwala wokondedwa wanuyo. Koma mukhoza kupezanso bwino.’ Mawu amenewa anandithandiza kwambiri.”
Ngati pali wachibale wanu amene anamwalira ndipo mukufuna kulimbikitsidwa, kabuku ka masamba 32, kamutu wakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kangakuthandizeni.
Mukhoza kuitanitsa kabukuka polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi, n’kutumiza ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire kabukuka.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.