Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Luso Lopanga Khofi

Luso Lopanga Khofi

Luso Lopanga Khofi

Anthu ambiri masiku ano amakonda kumwa khofi, ndipo khofi ndi chakumwa chotchuka kwambiri padziko lonse.

ANTHU ambiri okonda kumwa khofi, amakonda khofi wochita kutchezedwa. Potcheza khofiyu amathira madzi m’ketulo, ndipo madziwo akawira amachita nthunzi. Kenako nthunziwo umanyowetsa khofi amene amakhala pasefa. Ndipo khofiyo akanyowa, amakha madzi n’kupanga khofi amene anthu amamwa. Magazini ina inati: “Khofi amene amaphikidwa mwanjira imeneyi amakhala wokoma kwambiri chifukwa amakhala ndi kafungo konse ka khofi.”—Scientific American.

Katswiri wina wodziwa za khofi anati: “Anthu amakonda kumwa khofi wochita kutcheza m’malo ogulitsira khofi ndipo ena amayesetsa kuphika khofi wotere m’nyumba zawo.” Masiku ano anthu ambiri ali ndi maketulo otchezera khofi. Chifukwa cha zimenezi, chiwerengero cha anthu amene amamwa khofi ameneyu chikuwonjezereka m’mayiko ambiri.

Kodi inuyo mumamwa khofi? Kodi mukufuna kudziwa mmene khofi ameneyu amapangidwira? Kodi mungatani kuti muziphika khofi wokoma kwambiri? Galamukani! inafunsa John ndi bambo ake, a Gerardo, omwe amakhala mumzinda wa Sydney ku Australia, kuti afotokoze mmene amapangira khofi.

Kapangidwe Kabwino ka Khofi

A Gerardo ndi mwana wawo John ali ndi fakitale yopanga khofi. M’fakitale yawoyi mumakhala matumba ambiri a khofi wongochokera kumunda, wolimidwa m’mayiko osiyanasiyana. John anati: “Ndimasakaniza khofi wosiyanasiyana mogwirizana ndi malangizo a kapangidwe kake. Mtundu uliwonse wa khofi ndi wosiyana ndi unzake ndipo umathandizira kuti tipange khofi wabwino. Kuti munthu apange khofi wokoma zimatenga nthawi. Ifeyo tinayesera kwa miyezi 6 kuti tiyambe kupanga khofi wokoma kwambiri.” Mwina ichi n’chifukwa chake anthu opanga khofi safuna kuti anthu ena adziwe mmene iwo amapangira khofi wawo.

A Gerardo ndi amene amadziwa kukazinga nyemba za khofi ndipo zinawatengera nthawi kuti aphunzire luso limeneli. Ntchitoyi imafunikadi luso chifukwa nyemba za khofi zikapanda kukazingidwa bwino, khofi wake sanunkhira. Nyembazi zimakazingidwa m’chiwaya choyendera gasi, chomwe chimakhala ndi madzi. Madziwa akatentha kwambiri, amatulutsa nthunzi umene umatenthetsa nyembazi ndipo nyembazo zimafufuma mpaka kusweka. Nyembazi zikasweka zimatulutsa mafuta onunkhira ndipo mafuta amenewa ndi amene amapangitsa kuti khofi wamtunduwu akhale wabwino. Kuti khofiyu akhale wabwino, pamafunika kudziwa zinthu zoyenera kuchita pokazinga, monga kuchuluka kwa moto ndiponso kuchuluka kwa nthawi imene nyembazo ziyenera kukhala pamoto.

Nyembazi zikapsa, a Gerardo amaziphula n’kuziika m’beseni lalikulu ndipo amaziika pamalo ozizira kwambiri kuti zisapserere. John anati: “Fungo la khofi limamveka kwambiri pakapita tsiku limodzi kapena awiri mutakazinga.” Nthawiyi ikatha, mafuta amene amatulutsa fungo lonunkhira amakhazikika pansi pa besenilo ndipo mukhoza kuwayenga.

Kuphika Khofi

John anati: “Kuphika khofi wotere n’kovuta kwambiri kuposa kuphika khofi wamitundu ina.” Kuti munthu aphike khofi wotereyu amafunika kutsatira njira zitatu izi: kugaya nyemba za khofi (1), kuika nyemba zogayidwazo pasefa (2), kenako n’kuzithira madzi otentha ndipo khofi amayamba kukha (3). John ananenanso kuti: “Ntchito yogaya nyembazi ndi yovuta. Ngati nyembazo sizinagayike, khofi wake sakhala wamphamvu. Komanso nyembazi zikagayika kwambiri khofi wake amawawa. Khofi amene wapangidwa bwino sasowa chifukwa amakhala ndi mafuta pamwamba pake.”

Akagaya nyemba za khofi, John amaziika pasefa pogwiritsa ntchito chisupuni chachikulu kuti atsendere khofiyo. Kenako iye amaika sefa yodzaza nyembayo m’makina n’kuyatsa moto ndipo makinawo amayamba kugwira ntchito. Akatero, khofi amayamba kutuluka. John amatha kudziwa mwamsanga kuti khofi wagayika bwino kapena ayi. Iye anati: “Kuti mupange khofi wabwino pamafunika kuyeserera kangapo. Mukalephera kupanga khofi wabwino paulendo woyamba, mutha kuwonjezera kapena kuchepetsa khofi, kapenanso kumutsendera kwambiri pasefa.”

John akamaliza kuchita zimenezi, amayatsanso makina ophikira khofi aja, ndipo khofi wonunkhira bwino amayamba kudontha pang’onopang’ono ngati uchi. Zikatere, John amasangalala kwambiri kuti wapanga khofi wabwino. Iye ananena kuti: “Khofi akayamba kuoneka woyera, timathimitsa makinawo.” Kuti khofi ayambe kuoneka woyera zimatenga masekondi 30 okha. Khofi amene mungatunge pambuyo pake amakhala ndi mankhwala ambiri a caffeine ndipo amawawa kwambiri.

Akapanga khofi wamphamvu ndiponso wonunkhira kwambiri, John amasangalala kwambiri ndipo amafunsa makasitomala kuti: “Alipo akufuna khofi?”

Anthu ambiri amakonda khofi wochita kutcheza amene samusakaniza ndi zinthu zina kupatulapo shuga. Koma ena amakonda kuika mkaka m’khofi ameneyu. Magazini ina inati: “Masiku ano, pafupifupi 90 peresenti ya khofi amene amagulitsidwa amakhala wamkaka.” *Fresh Cup Magazine.

Kunena zoona, kumwa khofi kapena tiyi wabwino pamene mukucheza ndi anzanu n’kofunika kwambiri kuti musangalale. John anati: “Zakumwa zokoma zimachititsa kuti anthu akhale pamodzi n’kumasangalala.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Ngati mukufuna kudziwa ngati Mkhristu ayenera kupewa kumwa khofi kapena tiyi chifukwa chakuti amakhala ndi mankhwala a caffeine, amene amachititsa kuti munthu azingofuna kumwa khofi kapena tiyi, werengani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2007.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]

KUGULA NDI KUSUNGA KHOFI

Buku lina limati: “Nyemba za khofi zimene zakazingidwa zimawonongeka pakangodutsa mlungu umodzi, khofi wogayidwa amawonongeka pakangodutsa ola limodzi, ndipo khofi amene waphikidwa amawonongeka pakangodutsa mphindi zochepa.” Choncho, mukafuna kugula nyemba za khofi, ndi bwino kuti muzigula zochepa ndi kuzisunga pamalo ozizira ndiponso amdima. Koma musazisunge m’firiji chifukwa zikhoza kusiya kununkhira. Ndipo muziphika khofi wanu mukangogaya nyembazo.

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Photo 3: Images courtesy of Sunbeam Corporation, Australia