Kayendedwe ka Mpweya ndi Zinthu Zina
Kayendedwe ka Mpweya ndi Zinthu Zina
MUMZINDA mutakhala kuti simukufika madzi ndi mpweya wabwino komanso zinyalala sizikuchotsedwa, anthu angayambe kudwala ndi kufa. Padziko lapansili, mpweya ndi madzi abwino sizichita kubwera kuchokera ku malo ena ndipo zoipa sizinyamulidwa kuchoka padziko pano kukatayidwa kwinakwake. Ndiyeno kodi zimatheka bwanji kuti dziko lisadzaze ndi zonyansa zomwe zingachititse kuti zamoyo zife? Izi zimatheka chifukwa cha kayendedwe ka madzi ndi mpweya. Zimenezi tazifotokoza mosavuta ndipo zithunzizi zikuthandizanso kuti mumvetse.
Madzi akamayenda amasintha m’njira zitatu. 1. Amasanduka nthunzi n’kuulukira m’mlengalenga dzuwa likawomba. 2. Nthunzi ija ikafika m’mlengalenga imaundana n’kupanga mitambo. 3. Kenako mitambo imapanga mvula, matalala ndi chipale chofewa ndipo zonsezi zimagweranso padziko. Apa madziwa amakhala atayeretsedwa bwinobwino. Kodi ndi madzi ochuluka bwanji amene amayeretsedwa chonchi pachaka? Ofufuza apeza kuti amakhala ochuluka kwabasi moti atathiridwa padziko lapansili nthawi imodzi, angathe kuzama kufika m’chiuno mwa munthu.
2
← ◯
↓ 3 ↑
↓ 1 ↑
↓ ↑
→ →
→
Kayendedwe ka mpweya umene zinyama ndi zomera zimapuma. * Zinyama komanso anthufe timapuma mpweya umene umachokera m’zomera, nazonso zomera zimagwiritsa ntchito mpweya umene anthufe ndi zinyama zimatulutsa. Zomera zikamapanga chakudya zimagwiritsa ntchito mphamvu ya dzuwa, madzi komanso mpweya woipa umene anthufe ndi nyama zimatulutsa ndipo zikamapanga zakudyazi zimatulutsa mpweya wabwino umene anthufe timagwiritsa ntchito. Mpweya wabwinowu ukalowa m’matupi mwa nyama komanso anthufe umakasakanikirana ndi zakudya zogayidwa m’maselo kuti zitulutse mphamvu. Zimenezi zikamachitika, maselo amatulutsa madzi komanso mpweya woipa umene timatulutsa tikamapuma. Choncho, zomera zimayeretsa bwinobwino mpweya woipa umene timatulutsa zikamapanga chakudya. Zonsezitu zimachitika ife tisakudziwa.
Mpweya umene timapuma
←
← ←
↓ ↑
↓ ↑
↓ ↑
→ →
→
Mpweya umene zomera zimapuma
Kayendedwe ka mpweya wofunika kwambiri m’nthaka kamathandiza kwambiri kuti nthakayo ikhale ya chonde. A. Mpweya umenewu umachokera m’mlengalenga kukachitika mphenzi n’kufika m’nthaka ndipo tizilombo ta m’nthaka timagwiritsa ntchito mpweyawu popanga manyowa. B. Ndiyeno zomera zimagwiritsa ntchito manyowawa. Nyama zomwe zimadya zomerazi zimapezanso mpweyawu. C. Nyama komanso zomera zikafa, tizilombo tina tam’nthaka timaziwoletsa. Motero mpweya wotere umene unali m’zinthu zimenezi umabwerera m’mlengalenga ndipo wina umatsala m’nthaka momwemo.
← ← ← ← ← ← ← ← ← ←
↓ ↑
↓ Mpweya wofunika kwambiri m’nthaka ↑
↓ ndi wochuluka kwambiri m’mlengalenga ↑
↓ ↑
↓ Tizilombo ↓ Mpweya wofunika ↑
↓ A tosaoneka ↓ kwambiri m’nthaka ↑
↓ ndi maso ↓ B ↑ ↓ C ↑
→ Tizidutswa ta Tizilombo ↑
zinthu zakufa tosaonekandi ↑
maso →
→ → →
Dzikoli Limadziyeretsa Modabwitsa
Taganizirani izi: Chifukwa cha kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga, chaka chilichonse anthu akamapanga zinthu zosiyanasiyana pamatulukanso zoipa zambirimbiri zimene anthuwo amalephera kuziwononga. Koma dzikoli limayeretsa lokha zoipa zake zonse. Mkulu wina, dzina lake M. A. Corey, amene amalemba nkhani za chipembezo ndi za sayansi, anati: “N’zosatheka ngakhale pang’ono kuti zinangochitika mwamwayi kuti dziko lizitha kuchita zimenezi.”
Baibulo limapereka ulemu kwa amene anachititsa zimenezi. Limati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru.” (Salmo 104:24) Mulungu wasonyeza nzeru zimenezi mwapadera kwa anthu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Mpweya wabwino umene nyama ndi anthufe timagwiritsa ntchito umapezekanso m’madzi, m’zakudya zina komanso mu mpweya woipa umene timatulutsa. Choncho mpweya umene timapuma umayenda mogwirizana ndi kayendedwe ka madzi ndi mpweya umene zomera zimapuma.