N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?
N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?
Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?
AMENEWA ndi mafunso amene anthu amafunsa nthawi zambiri. Ndiponso funso lina limene anthu amafunsa lofanana ndi amenewa ndi lakuti: Kodi m’tsogolomu muli zabwino kapena tizingokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 basi, kenako n’kumwalira?—Salmo 90:9, 10.
N’kutheka kuti timafunsa kwambiri mafunso amenewa tikazindikira kuti moyo ndi waufupi kwambiri. Komabe, sipofunika kuti tiyambe tavutika kuti tifunse chifukwa chake tili ndi moyo. Kukhumudwa kungatichititsenso kudzifunsa funso limeneli. Ndipo anthu ena amadzifunsa funsoli akamaganizira za moyo wawo.
Dave anali pantchito yabwino kwambiri, anali ndi nyumba yabwino ndiponso ankakonda kucheza ndi anzake. Komabe iye anati: “Tsiku lina usiku ndikuchokera ku phwando ndinadzifunsa kuti, ‘kodi moyo uyenera kukhala chonchi basi?—Kodi ndidzangokhala ndi moyo zaka zochepa kenako n’kumwalira? Kapena kodi m’tsogolomu muli zinthu zina?’ Ndinkavutika maganizo poona kuti ndinalibe cholinga pamoyo wanga.”
M’buku limene Viktor Frankl analemba, anasonyeza kuti anthu ena amene anapulumuka naye limodzi paulamuliro wankhanza wa Nazi anadzifunsa funso limeneli atatulutsidwa ku ndende zozunzirako anthu. Atafika kwawo, ena mwa iwo anapeza abale awo atamwalira. Frankl analemba kuti: “Anthu ena atatulutsidwa anakhumudwa kwambiri chifukwa chakuti moyo sunali umene amauyembekezera.”—Man’s Search for Meaning.
Anthu Amene Amafunsa Funso Limeneli
Kuyambira kalekale anthu amafuna kudziwa chifukwa chake tili ndi moyo. Ndipo Baibulo limatiuza za anthu amene ankafuna kudziwa cholinga cha moyo wawo. Chuma chake chitatha, ana ake atafa komanso akudwala matenda oopsa Yobu 3:11.
kwambiri, Yobu anafunsa kuti: “Ndinalekeranji kufera m’mimba? Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine?”—Mmenemunso ndi mmene mneneri Eliya anamvera. Iye ankaganiza kuti wolambira Mulungu anali iye yekha basi. Ndiyeno anati: “Chotsani tsopano moyo wanga, Yehova.” (1 Mafumu 19:4) Anthu ambiri amakhalanso ndi maganizo amenewa. Ndipotu Baibulo limati Eliya anali “munthu monga ife tomwe.”—Yakobe 5:17.
Kuti Mukhale ndi Moyo Wabwino
Nthawi zambiri moyo umayerekezeredwa ndi ulendo. Mofanana ndi mmene munthu angayambire ulendo popanda malo enieni amene akupita, zingathekenso kukhala wopanda cholinga chenicheni pamoyo. Ngati muchita zimenezi, mungapeze mavuto amene wolemba mabuku wina wotchuka dzina lake Stephen R. Covey anawatchula kuti “kutanganidwa ndi moyo.” Iye ankafotokoza za anthu amene “amayesetsa kuti apeze zinthu zosafunika kwenikweni mwa kunyalanyaza zinthu zimene pambuyo pake amadzazindikira kuti ndi zimene zili zofunika kwambiri.”
Kodi simungavomereze kuti tikakhala paulendo changu chingakhale chopanda phindu ngati tikulowera kolakwika? Mofananamo, kufunafuna cholinga cha moyo wathu mwa kungodzitanganitsa ndi zochita zambiri, sikungatithandize komanso sikungatibweretsere chimwemwe.
Mtima wofuna kudziwa chifukwa chake tili ndi moyo ndi wofala kwa anthu a misinkhu yonse komanso azikhalidwe zosiyanasiyana. Zimenezi zimachitika chifukwa cha chinthu chimene tonsefe timafunikira kwambiri, zinthu zauzimu. Zosowa zauzimu sizingakwaniritsidwe ndi zinthu zakuthupi. Tiyeni tione zimene ena achita pokwaniritsa zosowa zauzimu zimenezi kuti adziwe cholinga cha moyo.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Kufunafuna cholinga cha moyo wathu mwa kungodzitanganitsa ndi zochita zambiri sikungatithandize komanso sikungatibweretsere chimwemwe
[Chithunzi patsamba 3]
Yobu ankafuna kudziwa cholinga cha moyo wake
[Chithunzi patsamba 4]
Eliya anali “munthu monga ife tomwe”