Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Mu 2007, dziko la China linali ndi “ampondamatiki 106 amene anali ndi ndalama za United States kuyambira madola 1 biliyoni kupita m’mwamba, pamene [mu 2006] ampondamatiki analipo 15 ndipo mu 2002 panalibe ndi mmodzi yemwe.”—CHINA DAILY, CHINA.
▪ “Ku India, anthu amene amanyalanyaza makolo awo okalamba azimangidwa, malinga ndi lamulo latsopano [limene] likusonyeza nkhawa imene anthu ambiri ali nayo yakuti moyo wamakono . . . ukusokoneza chikhalidwe cha makolo cholemekeza achibale.”—REUTERS, INDIA.
▪ “Masiku ano ku England, chiwerengero cha Asilamu enieni chingakhale chochuluka mofanana ndi chiwerengero cha Aangilikani enieni.”—THE ECONOMIST, BRITAIN.
Mitengo ya ku Siberia ndi Mgodi wa Miyala Yamtengo Wapatali
Magazini ina ya ku Russia inati m’nkhalango za ku Siberia “zimatheka kupeza golide m’zitsa zowola za mitengo.” (Vokrug Sveta) Asayansi a ku Ulan-Ude ku Irkutsk ndi ku Novosibirsk apeza kuti mitengo yosayoyola masamba imamera panthaka yomwe pansi pake pali miyala yamtengo wapatali ku Siberia. Mitengoyi imayamwa miyala yosungunukayo kuchokera mu nthaka. Ndipo mitengoyo ikafa n’kuwola, miyalayo imatsala pamwamba pa nthaka. Ku zowola za mitengoyi zokwana tani imodzi, asayansi ku Siberia apezako magalamu asanu a miyala ya pulatinamu, pafupifupi mamiligalamu 200 a golide ndi makilogalamu atatu a siliva.
Chithandizo cha Mankhwala Kumanda
Nyuzipepala ya ku Sydney ya Sun-Herald inati anthu okumba manda ku Australia apatsidwa makina othandiza anthu odwala mwadzidzidzi kumanda. Makinawo amathandiza anthu amene ali ndi matenda a mtima panthawi yakuti mtima wawo waleka kugunda chifukwa cha chisoni chimene ali nacho. Mayi Sisenanda Santos, yemwe ndi mneneri wa bungwe la St. John Ambulance limene limayang’anira ntchitoyi, anati: “Kumanda ndi malo oopsa kwambiri kwa anthu odwala matenda a mtima. Kumakhala anthu ambiri, anthuwo amakhala ndi chisoni kwambiri, ndipo nthawi zambiri zovala zawo zimakhala zotentha pamene nyengonso ili yotentha.” Amene amagwiritsa ntchito makinawo amatsatira malangizo ake ndipo makinawo amatulutsa mphamvu yamagetsi imene imachititsa mtima wa wodwalayo kuyambanso kugunda. Makina amenewa amatulutsa mphamvu yamagetsi ngati vutolo ndi la mtima basi.
Chisudzulo Chikuwononga Zachilengedwe
Kuchuluka kwa zisudzulo padziko lonse kukuwononga zachilengedwe. Zili choncho chifukwa kuchuluka kwa anthu osudzulana kumawonjezera chiwerengero cha anthu ofuna zinthu monga madzi ndi magetsi, zomwe ndi zochepa kale. Zotsatira za kafukufuku zimene zinafalitsidwa m’magazini ya Proceedings of the National Academy of Sciences zinasonyeza kuti chifukwa cha chisudzulo, anthu okhala m’mabanja amachepa, ambiri amayamba kukhala paokha, ndipo zimenezi zimachititsa kuti munthu mmodzi aliyense azigwiritsa ntchito madzi ndi magetsi ambiri. Magaziniyo inati: “Ku [United States], anthu osudzulana akanatha kuthandiza kuti dzikolo lisamange nyumba zoposa 38 miliyoni, kusawononga magetsi oposa makilowati 73,000 biliyoni, ndi madzi oposa malita 2.4 biliyoni m’chaka cha 2005 chokha, akanakhala kuti anagwiritsa ntchito zinthu zimenezi monga mabanja.” M’chaka cha 2000, ku United States kunali mabanja “owonongetsa chuma” ngati amenewa okwanira 6.1 miliyoni.
Baibulo Lonse Pamutu wa Singano
Ku Israel, asayansi yogwiritsa ntchito tinthu tating’ono tosaoneka ndi maso asindikiza “Chipangano Chakale” chonse m’Chiheberi pakachitsulo “kakang’ono kwambiri kuposa mutu wa singano,” inatero Science Daily ya pa Intaneti. Iwo anachita zimenezi mwa kumamenyetsa tinthu tina tating’ono tosaoneka totchedwa gallium ions, pakachitsulo kagolide kakang’onoko ndipo malembawo n’kumazokotedwa. Pulofesa Uri Sivan wa pa Technion-Israel Institute of Technology, anati: “Ntchito yokonza kabaibulo kakang’ono kosaoneka imeneyi ikusonyeza luso lochepetsa zinthu limene tili nalo.” Ntchito imeneyi ikusonyezanso kuti tingathe “kusunga mawu ochuluka pamalo ochepa kwambiri.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
AP Photo/Ariel Schalit