Kodi Ndi Bwino Kugwiritsa Ntchito Mayina Aulemu?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Ndi Bwino Kugwiritsa Ntchito Mayina Aulemu?
PAMOYO wawo watsiku ndi tsiku komanso polalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, Akhristu oyambirira ankakumana ndi akuluakulu a boma, ena audindo wotsikirapo ndipo enanso audindo waukulu. Otsatira a Yesu sankagwiritsa ntchito mayina aulemu pakati pawo pofuna kusiyanitsa udindo umene munthu anali nawo. Koma nthawi imeneyo anthu olamulira anzawo ankatchedwa ndi mayina aulemu. Mwachitsanzo, mfumu ya Roma inkatchedwa kuti “Wolemekezeka.”—Machitidwe 25:21.
Ndiyeno kodi ophunzira a Yesu akakhala pamaso pa akuluakulu a boma, ankaiona bwanji nkhani yogwiritsa ntchito mayina aulemu? Nanga ifeyo tiyenera kuiona bwanji?
Wangokhala Ulemu, Osati Kugwirizana Nawo
Mtumwi Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Perekani kwa onse zimene amafuna, kwa amene amafuna . . . kulandira ulemu, m’patseni ulemu wake.” (Aroma 13:7) Zimenezi zinaphatikizapo kutchula mayina aulemu a akuluakulu a boma. Masiku ano, mawu monga akuti Wolemekeza ndiponso Bwana, amagwiritsidwa ntchito potchula akuluakulu a boma. Koma ena angadabwe kuti, ‘Ndingatchule bwanji munthu wina kuti wolemekezeka, pamene ndikuona kuti alibe khalidwe lolemekezeka?’
Akuluakulu a boma ambiri amachita ntchito yawo bwino, koma sikuti onse tingawadalire. Ngakhale zili choncho, Baibulo limatiuzabe kuti tizigonjera mafumu ndi nduna “chifukwa cha Ambuye.” (1 Petulo 2:13, 14) Choncho, kuzindikira kuti munthuyo ali pa udindo wake mololedwa ndi Mulungu, kuyenera kutilimbikitsa kum’patsa ulemu wake.—Aroma 13:1.
Palembali, khalidwe la mkulu wa boma sindilo chifukwa chimene tiyenera kumupatsira ulemu. Kum’tchula mkulu wa boma pogwiritsa ntchito dzina lake laulemu sikusonyeza kuti tikugwirizana ndi khalidwe lakelo. Nkhani ya mtumwi Paulo ikusonyeza zimenezi.
Mmene Paulo Anagwiritsira Ntchito Mayina Aulemu
Mtumwi Paulo anamangidwa ku Yerusalemu pa milandu yomunamizira ndipo anatumizidwa kwa Felike, bwanamkubwa wa Yudeya. Felike Machitidwe 24:26.
anali mkulu wa boma wopanda khalidwe. Wolemba mbiri wa ku Roma dzina lake Tacitus, ananena kuti Felike “ankakhulupirira kuti angachite choipa chilichonse popanda kulangidwa.” Chidwi chake chinali pa ziphuphu, osati chilungamo. Ngakhale zinali choncho, pa zaka zonse ziwiri zimene Paulo anakhala m’ndende, anapatsabe bwanamkubwayu ulemu. Awiriwa ankakhala pansi n’kumacheza. Pochezapo, Felike ankayembekezera kuti Paulo amupatsa ndalama koma sizinatero, pamene Paulo anagwiritsa ntchito mpatawo kumulalikira.—Fesito atalowa m’malo mwa Felike kukhala bwanamkubwa, anamvetsera mlandu wa Paulo ku Kaisareya. Pofuna kusangalatsa atsogoleri a Ayuda, Fesito anapereka maganizo akuti mlandu wa Paulo ukazengedwe ku Yerusalemu. Koma Paulo anadziwa kuti kumeneko sakaweruzidwa mwachilungamo. Choncho, anagwiritsa ntchito ufulu wake monga nzika ya Roma ndipo anati: “Ndikupempha kukaonekera kwa Kaisara!”—Machitidwe 25:11.
Fesito sanadziwe kuti afotokoza bwanji mlandu wa Paulo kwa Kaisara. Koma mwamwayi, Mfumu Agiripa Yachiwiri inabwera pa ulendo wodzapereka ulemu kwa Fesito ndipo inanena kuti ingakonde kumva mlanduwo. Tsiku lotsatira, mfumuyo inalowa m’bwalo ndi ulemu waukulu wachifumu limodzi ndi akuluakulu a asilikali ndi nduna zina.—Machitidwe 25:13-23.
Atauzidwa kuti alankhule, Paulo anayamba ndi mawu akuti “Mfumu,” ndipo anatamanda Agiripa pokhala katswiri pa miyambo yonse ndi pa zimene Ayuda ankakangana. (Machitidwe 26:2, 3) Komatu panthawiyi n’kuti Agiripa ali ndi mbiri yoipa chifukwa chakuti anali pachibwenzi ndi mlongo wake ndipo ankagona naye. Paulo ayenera kuti ankadziwa mbiri yoipa imene Agiripa anali nawo chifukwa cha kupanda khalidwe kwake. Komabe anam’patsa ulemu wake monga mfumu.
Pamene Paulo anali kufotokoza mbali yake pa mlanduwo, Fesito anakuwa kuti: “Upenga iwe Paulo!” M’malo mokwiya, Paulo anayankha modekha ndipo anatchula bwanamkubwayo kuti “Wolemekezeka.” (Machitidwe 26:24, 25) Paulo anam’patsa ulemu malinga ndi udindo wake. Komabe chifukwa cha zitsanzo zimenezi, funso ndi lakuti, Kodi tiyenera kukhala ndi malire popereka ulemuwo?
Ulemu Wosapitirira Malire
Ulamuliro wa boma uli ndi malire, malinga ndi mmene lemba la Aroma 13:1 limanenera kuti: “Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.” Choncho, ulemu umene umaperekedwa kwa akuluakulu a boma ulinso ndi malire. Yesu anaika malire a ulemu umene tiyenera kupatsa ena pamene anauza ophunzira ake kuti: “Inu musatchulidwe Rabi, pakuti mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wa kumwamba Yekhayo. Ndipo musatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”—Mateyo 23:8-10.
Motero, pa nkhani yopereka ulemu woyenerera, pali kusiyana pakati pa udindo wa boma ndi udindo wa chipembedzo. Ngati akuluakulu a boma ali ndi mayina aulemu omwe ndi achipembedzo, uphungu wa Paulo wakuti tiziwapatsa ulemu sitingaugwiritse ntchito pa mayina oterewa. Munthu amene amatsatira uphungu wa m’Malemba amalemekeza akuluakulu a bomawo. Komabe, chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo chimamuletsa kugwiritsa ntchito mayina aulemu achipembedzo, chifukwa iye afunika ‘kupereka zinthu . . . za Mulungu, kwa Mulungu.’—Mateyo 22:21.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
▪ Kodi otsatira a Yesu ankaona bwanji akuluakulu a boma?—Aroma 13:7.
▪ Kodi mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mayina aulemu potchula akuluakulu a boma?—Machitidwe 25:11; 26:2, 25.
▪ Kodi Yesu analetsa kugwiritsa ntchito mayina aulemu otani?—Mateyo 23:8-10.
[Chithunzi pamasamba 20, 21]
Kodi polankhula ndi Agiripa, Paulo anamutchula kuti chiyani?