Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Zinachitikira Kuti?

1. Kodi Saulo amapita kuti pamene izi zinachitika?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 9:1-9.

Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapupo.

ROMA

YERUSALEMU

DAMASIKO

BABULO

▪ Kodi mawu ochokera kumwamba amene Saulo anamva anali a ndani?

․․․․․

▪ N’chiyani chinam’chitikira Saulo atangoona kuwala?

․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani Saulo ankazunza Akhristu? N’chifukwa chiyani anthu ena angakuvutitseni mukamawauza za Yehova? Kodi nkhani ya Saulo ingakuthandizeni bwanji kukhala wolimba mtima?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa ndipo lembani vesi kapena mavesi amene akusowa.

TSAMBA 5 Kodi sitiyenera kukhulupirira ndani? Salmo 146:․․․

TSAMBA 6 Kodi dziko lidzadzaza ndi anthu otani? Yesaya 11:․․․

TSAMBA 11 Kodi olungama adzalandira chiyani? Salmo 37:․․․

TSAMBA 27 Kodi Yobu atasowa mtendere anauza ena za chiyani? Yobu 10:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenako lembani mayina olondola pa mizereyi.

2. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Mayi anga anaseka atamva kuti adzabereka ineyo.

Werengani Genesis 17:19; 18:10-14.

3. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: M’kulu wanga anandigulitsa ukulu wake posinthana ndi mphodza.

Werengani Genesis 25:29-34.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Bambo anga anati ndine “mwana wa mkango.”

Werengani Genesis 49:9

▪ Mayankho ali pa tsamba 20

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Damasiko.

▪ Yesu.

▪ Anachita khungu.

2. Isake.—Luka 3:34.

3. Yakobo.—Luka 3:34.

4. Yuda.—Luka 3:33.