Kodi Anthu Angabweretse Tsogolo Labwino?
Kodi Anthu Angabweretse Tsogolo Labwino?
Tiyerekeze kuti mwangosamukira kumene m’nyumba ya njerwa yomwe ikuoneka kuti ndi yolimba ndiponso yokongola. Nyumbayi ndi imene mwakhala mukuilakalaka. Tsopano zinthu zikuoneka kuti zili bwino. Koma pasanathe zaka zambiri, nyumba ija ikuchita ming’alu ikuluikulu ndipo ikungofunika kuigwetsa. Izi zakukhumudwitsani zedi. Komabe zimenezi sizikuchitikira inu nokha. Nyumba zambiri m’dera lanulo zilinso ndi vuto lomweli. Ofufuza apeza kuti chikuchititsa zimenezi ndi vuto la njerwa komanso kuti nyumbazo sizinamangidwe bwino.
MOFANANA ndi nyumba imeneyi, dzikoli lili ndi mavuto aakulu. Ngakhale kuti pali mabungwe ndi magulu andale osiyanasiyana komanso kupita patsogolo kwa sayansi, zikuoneka kuti anthu sakugwirizana. M’mayiko ambiri, kuswa malamulo ndiponso zipolowe n’zofala. Koma kodi kufunitsitsa kuthetsa mavuto kungachititse anthu kukonza zinthu kuti akhazikitse boma labwino? Taganizirani zimene olamulira ena anena zokhudza mbiri ya anthu.
“Tayesa Njira Zonse”
Pofuna kuti dziko likhale labwino, anthu ambiri anzeru monga Plato yemwe ndi katswiri wa maphunziro wa ku Greece, komanso Karl Marx yemwe ndi katswiri wa maphunziro a za ndale wa ku Germany, atchulapo mitundu yosiyanasiyana ya maboma. Kodi zotsatira zake zakhala zotani? Nkhani ya m’nyuzipepala ina inati: “Anthufe sitinathetse umphawi kapena kubweretsa mtendere wapadziko lonse. Zimene takwanitsa n’zosiyana kwambiri ndi zimene timafuna. Sikuti sitinayesetse. Tayesa njira zonse, kungoyambira maboma olimbikira kwambiri zamalonda komanso maboma osalimbikira za malonda. Tayesanso kuthetsa nkhondo pogwiritsa ntchito bungwe la League of Nations ndiponso zida za nyukiliya. “Tamenya nkhondo zambiri kuti tikhazikitse mtendere . . . koma talephera. M’malo mwake nkhondo zikungopitirirabe m’madera ambiri.” Nyuzipepalayo inapitiriza kuti: “Mmene zaka za m’ma 2000 zimayamba, tinkakhulupirira kuti asayansi atithandiza, koma pano sitingakhulupirire chilichonse chimene angatiuze.”—New Statesman.
Mu 2001, pulofesa wa mbiri yakale amene anapuma pantchito pa yunivesite ya ku London, dzina lake Eric Hobsbawm, analemba kuti magulu andale “afika nthawi imene zochita zawo zawononga kwambiri chilengedwe ndi dziko.” Kuti mavuto amenewa athe, kapena
achepe “pakufunika zambiri osati kungosintha ndale kapena kungotengera zimene anthu ambiri akunena. Zimenezi sizolimbikitsa chifukwa si zimene anthu okonda demokalase kapena anthu padziko lonse akhala akuyembekezera.”Poganizira mavuto amene ali m’tsogolomu, katswiri wina wa zakuthambo, dzina lake Stephen Hawking anafunsa kuti: “Popeza dzikoli lafika poipa kwambiri pankhani zandale, moyo wa anthu ndiponso zachilengedwe, kodi anthu angakhalenso padzikoli zaka zina 100?”
N’chifukwa Chiyani Anthu Alephera Kukonza Zinthu?
Ndi Baibulo lokha limene limafotokoza bwino chifukwa chimene anthu alepherera kudzilamulira bwinobwino. Choyamba, Baibulo limatifotokozera momveka bwino mmene anthu anapangidwira. Mwachitsanzo, taonani mfundo zinayi zotsatirazi zimene ndi zosatsutsika.
Tonse ndife opanda ungwiro. “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Monga momwe njerwa zosalongosoka zingapangitsire nyumba kugwa, kupanda ungwiro kumene tinatengera kwa makolo athu kungatipangitse kuchita zinthu zimene zingayambitse kusagwirizana ndi anthu ena. Zimenezi ndi zinthu monga katangale, chinyengo, dyera ndiponso kuponderezana. Izi sizachilendo. Zaka 3,000 zapitazo, wolemba Baibulo wanzeru anati: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.”—Mlaliki 8:9.
Pozindikira kuti anthufe ndi opanda ungwiro ndiponso timakonda kulakwitsa zinthu, atsogoleri aboma ndiponso oweruza amapanga malamulo ambirimbiri. Koma amachita zimenezi akudziwa bwino kuti palibe amene angaike lamulo lolimbikitsa anthu kukonda anzawo kapena kumvera malamulo.
Timafa. “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya [mphamvu ya moyo] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:3, 4) Mfumu Solomo ya ku Isiraeli wakale inali yanzeru kwambiri, koma inaona kuti khama lake pantchito linali lopanda phindu. Iye analemba kuti: “Ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzam’siyira izo munthu wina amene adzanditsata. Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse . . . Ichinso ndi chabe.”—Mlaliki 2:18, 19.
Sitingadzilamulire bwinobwino. “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kuwonjezera pa kupanda ungwiro, Baibulo limaphunzitsa kuti malinga ndi cholinga chake, Mulungu sanapatse anthu udindo wodzilamulira ndipo anthuwo sangathe kuchita zimenezi bwinobwino. Mwachitsanzo, n’chifukwa chiyani anthu safuna kuuzidwa zochita ndi anthu anzawo kapena kupatsidwa mfundo zoti azizitsatira? Yankho n’lakuti tinalengedwa kuti tizilamuliridwa ndi wolamulira winawake wamkulu osati anthu. Wolamulira ameneyu ndi Mulungu.—Yesaya 33:22; Machitidwe 4:19; 5:29.
Anthu akulamuliridwa ndi wolamulira wosaoneka. “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” yemwe ndi Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Ngati akuluakulu pakampani ali oipa kwambiri ndipo palibe amene angawauze zochita, kodi antchito wamba angakonze zinthu? Iwo sangasinthe zinthu kwenikweni. Ndi mmenenso zilili pankhani yokonza mavuto amene Satana ndi ziwanda zake, omwe ndi olamulira osaoneka a dzikoli, abweretsa. Baibulo limatchula olamulira amenewa kuti “maboma,” “maulamuliro,” “olamulira dziko a mdimawu,” ndiponso “makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba.”—Aefeso 6:12.
Komabe sikuti Baibulo limangonena za kulephera kwa anthu ndi olamulira osaoneka a dzikoli. Limanenanso uthenga wabwino wa chiyembekezo wosonyeza mmene mavuto athu adzathere.
Mlengi Wathu Adzatipulumutsa
Patokha sitingathetse mavuto athu. Ngakhale munthu atakhala wanzeru, wamphamvu, kapena wachuma chochuluka motani, sangathetse mavuto anayi amene tawatchula m’nkhani ino. * M’nkhani yotsatira tiona kuti Mlengi wathu amatiganizira ndipo sanatiiwale. Popeza iye ndi Wolamulira woyenera, adzachotsa mavuto onse amene amachititsa kuti tisamasangalale. (1 Yohane 4:8) Ndipotu adzachita zimenezi posachedwapa. Kodi tikudziwa bwanji?
Nkhani za mu Galamukani! ya mwezi watha zinasonyeza kuti zochitika m’dzikoli zikuonetseratu kuti tilidi “m’masiku otsiriza” a dziko lino. (2 Timoteyo 3:1; Mateyo 24:3-7) Mapetowo sadzafika chifukwa cha kuphulika kwa zida za nyukiliya kapena kuwombana kwa dziko ndi zinthu zina, kumene kudzaphe anthu abwino ndi oipa omwe. Mulungu ndiye adzamenye nkhondoyi pochotsa oipa, ndi onse amene amalimbikitsa ulamuliro wa anthu. (Salmo 37:10; 2 Petulo 3:7) Iye adzathetsanso mavuto oyambitsidwa ndi anthu otsutsana naye. *—2 Atesalonika 1:6-9.
Kenako Mlengi adzathetsa vuto lathu losowa ulamuliro wabwino mwa kubweretsa “ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Nkhani yotsatirayi isonyeza kuti ufumu umenewu ndi boma limene limatipatsa chiyembekezo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 17 Onani nkhani yakuti “Kodi Mphatso Zachifundo Zingathetse Mavuto Athu Onse” pa tsamba 19.
^ ndime 18 Funso lakuti “N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?” linayankhidwa pa tsamba 106 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
ANTHU ALI NGATI “NJERWA” ZOSALONGOSOKA PAZIFUKWA IZI
▪ Tonsefe ndife opanda ungwiro.
▪ Timafa.
▪ Sitingadzilamulire bwinobwino.
▪ Anthu akulamuliridwa ndi wolamulira wosaoneka.
[Bokosi patsamba 6]
ANTHU SADZAWONONGERATU DZIKOLI
Baibulo limapereka umboni wokwanira wakuti cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi chinali chakuti anthu omuopa azikhalapo bwinobwino mwamtendere. Taonani malemba otsatirawa.
“Anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.”—Salmo 104:5.
“Munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.”—Salmo 119:90.
“Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.”—Mlaliki 1:4.
“Dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.
“[Yehova ndi] amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.”—Yesaya 45:18.