“Dalitsidwani ndi Mfumu Yotsogoleredwa ndi Mzimu wa Yehova”
“Dalitsidwani ndi Mfumu Yotsogoleredwa ndi Mzimu wa Yehova”
▪ Mawu a pa Mlaliki 8:9 amafotokoza bwino ulamuliro wa anthu. Mawuwo amati: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” Kodi zimenezi zidzasintha? Kapena kodi mmene zinthu zakhala zikuchitikira m’mbuyomu zikusonyeza kuti m’tsogolomu zidzakhala chimodzimodzi? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani ya onse pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2008/2009 wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera”. Mutu wa nkhaniyo ndi wakuti “Dalitsidwani ndi Mfumu Yotsogoleredwa ndi Mzimu wa Yehova.” Nkhaniyo idzafotokoza za Yesu Khristu amene adzalamulira mwa chilungamo chenicheni komanso mwachikondi. Iye anapereka moyo wake m’malo mwa ife.—Mateyo 20:28.
N’chifukwa chiyani Yesu ali wosiyana ndi olamulira ena? Mneneri Yesaya anayankha kuti: “Ndipo mzimu wa Yehova [Mulungu] udzam’balira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera; koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka.”—Yesaya 11:2-4.
Kodi zimene zafotokozedwa pa lembali zakusangalatsani? Ngati zakusangalatsani, kamvereni nkhaniyi pamsonkhano wachigawo umene udzachitike m’malo osiyanasiyana padziko lonse kuyambira mwezi uno. Ngati mukufuna kudziwa malo amene msonkhanowu udzachitikire m’dera lanu, funsani a Mboni za Yehova kwanuko kapena lemberani kalata ofalitsa magazini ino pa adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 la magazini ino. Nsanja ya Olonda ya March 1, 2008, ili ndi mndandanda wa malo amene kudzachitikire misonkhano ku Malawi ndi ku Mozambique.