Kodi Pali Chipembedzo Choona Chimodzi Chokha?
Kodi Pali Chipembedzo Choona Chimodzi Chokha?
Funso limeneli anthu ena limawaipira. Iwo amati pali zipembedzo zambirimbiri, moti aliyense amene amati chipembedzo chake chokha n’chimene chili choona, ndi woganiza moperewera ndiponso ndi wamakani. Iwo amati chipembedzo chilichonse chiyenera kukhala ndi mfundo zinazake zoona. Kodi inunso mumaona choncho?
N’ZOONA kuti pali nkhani zina zimene anthu angathe kuziona m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, wina angaone kuti zakudya zinazake zingamuthandize kukhala ndi thanzi. Koma kodi ndi bwino kuti azikakamiza aliyense kudya zakudya zakezo, ngati kuti ndi zokhazo zimene zingapatse munthu thanzi? Ayi sibwino. Chifukwatu munthu wanzeru komanso wodzichepetsa amazindikira kuti anthu ena angasankhe zakudya zina zopatsa thanzi, mogwirizana ndi thupi lawo.
Kodi n’chimodzimodzinso ndi zachipembedzo? Kodi pali zipembedzo zambirimbiri zoona zimene munthu angasankhepo malinga ndi mmene anakulira, kapenanso makonda ake? Kapena kodi pali chipembedzo chimodzi chokha chokhala ndi mfundo za choonadi zomwe aliyense ayenera kutsatira? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pankhaniyi. Tiona kaye ngati zili zotheka n’komwe kudziwa choonadi. Chifukwatu ngati n’zosatheka ndiye kuti kufunafuna chipembedzo choona n’kungotaya nthawi.
Kodi N’zothekadi Kudziwa Choonadi?
Atangotsala pang’ono kuphedwa, Yesu Khristu ananena mawu otsatirawa kwa Bwanamkubwa wachiroma, Pontiyo Pilato, yemwe ankamva mlandu wake. Iye anati: “Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvera mawu anga.” Pilato anafunsa kuti: “Choonadi n’chiyani?” ndipo n’kutheka kuti funsoli linali lamwano. (Yohane 18:37, 38) Komabe, Yesu sankanena za choonadi mokayikira chifukwa ankadziwa kuti choonadi chilipo. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zinayi zotsatirazi zimene Yesu Khristu ananena kwa anthu osiyanasiyana:
“Chimene ndinabadwira, ndi chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.”—Yohane 18:37.
“Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo.”—Yohane 14:6.
“Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira ndi mzimu ndi choonadi.”—Yohane 4:23, 24.
“Ngati mukhala m’mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga, mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:31, 32.
Pamenepatu taona kuti Yesu ananena mosakayika ngakhale pang’ono kuti choonadi chilipo ndiponso kuti tingathe kuchidziwa, motero kodi si kwanzeru kufufuza tokha nkhaniyi, ngati timakayikira?
Kodi Pali Choonadi Chosatsutsika?
N’zosachita kufunsa kuti pali zinthu zina zimene inuyo simuzikayikira ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, simukayika zoti inuyo ndinu munthu weniweni ndiponso kuti zonse zimene mukuona pamene mulipo ndi zenizeni. Mitengo, mapiri, mitambo, dzuwa, ndiponso mwezi ndi zenizeni, osati zongoyerekezera. Inde, pali anthu ena odziona ngati anzeru amene anganene kuti zinthu zimene tatchulazi si zenizeni. Koma n’zokayikitsa kuti mungatengeke ndi mfundo zoterezi.
Komanso pali malamulo a chilengedwe. Nawonso ali m’gulu la zinthu zosatsutsika kuti zilipodi. Mwachitsanzo, mutati mudumphe kuchokera pamwamba, mukhoza kukagwa pansi; mutakana kudya mukhoza kumva njala, ndipo ngati mutapanda kudya kwa nthawi yaitali
mukhoza kumwalira. Malamulo amenewa amagwira ntchito kwa munthu wina aliyense ndipotu simukayikira mfundo imeneyi.Mfundo ya m’Baibulo yotsatirayi, imakhudzanso ena mwa malamulo achilengedwewa. Mfundo yake ndi yakuti: “Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake?” N’zoona kuti panthawi imene lembali linkalembedwa, aliyense ankavomereza mfundo yakuti zovala zingathe kupsa ngati zitaikidwa pa moto. Komabe potchula zimenezi, mwambi wa m’Baibulowu ukutithandiza kumvetsa mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Wolowa kwa mkazi wa mnzake; [n’kugona naye] sadzapulumuka chilango.”—Miyambo 6:27, 29.
Kodi mfundo imeneyi ndi yosatsutsika ngakhale pang’ono? Ena anganene kuti ayi. Iwo anganene kuti anthu amaona nkhani ya makhalidwe abwino m’njira zosiyanasiyana, malingana ndi mmene anakulira, zikhulupiriro zawo, ndiponso mmene zinthu zilili pamoyo wawo. Komabe, taonani malamulo angapo a m’Baibulo a makhalidwe abwino. Kodi simungavomereze kuti malamulo amenewa ndi osatsutsika?
Baibulo limaletsa chigololo. (1 Akorinto 6:9, 10) Anthu ena savomereza kuti mfundo imeneyi ndi yoona, motero amachitabe chigololo. Komabe amatuta zimene afesa, motero nthawi zambiri amavutika ndi zinthu monga chikumbumtima chawo, chisudzulo, kukhumudwa kapenanso kukhumudwitsa kwambiri anzawo.
Mulungu amaletsanso uchidakwa. (Miyambo 23:20; Aefeso 5:18) Kodi chimachitika n’chiyani anthu akakhala zidakwa? Nthawi zambiri anthuwa amachotsedwa ntchito, amawononga thanzi lawo, mabanja awo, ndiponso amavutika maganizo. (Miyambo 23:29-35) Ngakhale anthu amene savomereza mfundo yakuti uchidakwa n’ngolakwika amakumana ndi mavuto amenewa. Motero kodi tingati malamulo amenewa amagwira ntchito kwa anthu okhawo amene amawakhulupirira?
Ndiye palinso malamulo a makhalidwe abwino amene Baibulo limati tizitsatira. Mwachitsanzo, Baibulo limati tizikonda akazi athu, tizilemekeza amuna athu, ndiponso kuti tizichitira ena zabwino. (Mateyo 7:12; Aefeso 5:33) Kutsatira malamulo amenewa kumatipindulitsa. Kodi mungati malangizo amenewa ndi othandiza kwa anthu enaake okha basi?
Pankhani ya kutsatira malamulo a makhalidwe abwino a m’Baibulo, munthu wina aliyense amatuta chimene wafesa. Zimenezi zimatsimikizira kuti malamulo amenewa satengera makonda a munthu. Koma ndi choonadi. N’zoonekeratu kuti munthu amatuta zabwino akatsatira malamulo a m’Babulo a makhalidwe abwino koma amatuta zoipa akapanda kutero.
Motero taganizirani: Ngati malamulo a m’Baibulo a makhalidwe abwino amagwira ntchito kwa aliyense, kuli bwanji mfundo za m’Baibulo zokhudza zinthu monga chipembedzo, zimene zimachitika munthu akamwalira, ndiponso chiyembekezo chathu cha moyo wosatha? Munthu wanzeru angathe kuona kuti mfundo zimenezinso ndi choonadi, chimene chimakhudza munthu wina aliyense. Pamfundo zimenezinso, aliyense amatuta chimene wafesa, kaya amakhulupirira mfundozi kapena ayi.
Inde, n’zotheka kudziwa choonadi. Yesu anati, Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, ndi Yohane 17:17) Komabe, mwina mungaone kuti choonadi n’chovuta kuchipeza. N’chifukwa chiyani mungaone choncho? N’chifukwa choti pali zipembedzo zambiri zimene zimati zimaphunzitsa choonadi. Ndiyeno kodi n’chipembedzo chiti chimene chikuphunzitsadi choonadi cha m’Mawu a Mulungu? Kodi tingati n’chimodzi chokha? Kodi sizotheka kuti choonadi, kapena mfundo zina za choonadi, zimapezekanso m’zipembedzo zosiyanasiyana?
choonadi. ([Mawu Otsindika patsamba 4]
Kodi zomwe zimachitika tikaika moto pa chovala zikufanana bwanji ndi kusamvera malamulo a Mulungu?