Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kutukwana N’kulakwadi?

Kodi Kutukwana N’kulakwadi?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Kutukwana N’kulakwadi?

“Ndikuganiza kuti ndinayamba khalidwe lotukwana chifukwa ndinkafuna kufanana ndi anzanga akusukulu.”—Anatero Melanie. *

“Ndinkaona ngati kutukwana sikulakwa chifukwa choti nthawi zonse ndinkamva anthu akutukwana ku sukulu ndi kunyumba komwe.”—Anatero David.

N’CHIFUKWA chiyani mwana akatukwana, anthu amadabwa nazo kwambiri koma sizioneka ngati zachilendo munthu wamkulu akatukwana? Kodi kutukwana kumasanduka chinthu chabwino chifukwa choti yemwe akutukwanayo ndi wachikulire? Anthu ambiri amatukwana ndiponso ena amaona kuti ana okha ndi omwe sayenera kutukwana. Chifukwa cha zimenezi mwina mungadzifunse kuti: “Kodi kutukwana n’kulakwadi?

Kutukwana Kumaoneka Ngati Chinthu Chabwino

N’zosachita kufunsa kuti kutukwana n’kofala kwambiri. Ndipotu achinyamata ambiri amanena kuti ngati atati nthawi iliyonse akamva munthu akutukwana azipatsidwa ndalama inayake, bwenzi atapeza ndalama zankhaninkhani moti sakanafunikiranso kudzagwira ntchito pamoyo wawo wonse ndipo ngakhale makolo awo akanangosiya kugwira ntchito. Mtsikana wina wa zaka 15 dzina lake Eve anati: “Anthu akamacheza kusukulu kwathu, mawu alionse omwe angatchule, amakhala otukwana. Munthu ukamamva zimenezi tsiku ndi tsiku, n’zosavuta kutengera”

Kodi nanunso muli ndi anzanu amene amakonda kutukwana? Kapena mwina inunso mwatengera khalidweli? * Ngati zili choncho, taganizirani zimene zimakuchititsani kuti muzitukwana. Zingakhale zosavuta kusiya khalidweli ngati mutazindikira zimene zimakuchititsani.

Mukuganizira mfundo zimenezo, tayesani kuyankha mafunso awa.

Kodi nthawi zambiri, mumatukwana pa zifukwa zotani?

□ Kusonyeza kukwiya kapena kukhumudwa

□ Kufuna kuti anthu andione

□ Kutsanzira anzanga

□ Kufuna kuopedwa

□ Kuchitira mwano akuluakulu

□ Zifukwa zina ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

Kodi kawirikawiri mumatukwana muli kuti?

□ Kusukulu

□ Kuntchito

□ Pamakalata otumiza pakompyuta, kapena pa mauthenga a pa foni

□ Ndikakhala ndekha

Kodi mumati chodzikhululukira chanu n’chiyani pa khalidwe lanulo?

□ Anzanga onse amatukwana

□ Makolo amatukwana

□ Aphunzitsi amatukwana

□ M’mafilimu, pawailesi amatukwana

□ Ndimangoona kuti amenewa ndi mawu basi

□ Ndimangotukwana pamaso pa anthu amene siziwaipira basi

□ Zodzikhululukira zina ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

Nanga n’chifukwa chiyani muyenera kuthetsa khalidwe limeneli? Kodi kutukwana n’koipadi? Taganizirani mfundo zotsatirazi.

Amenewatu si mawu chabe ayi. Yesu anati: “Mawu amene umalankhula amasonyeza zimene zili mu mtima mwako.” (Luka 6:45, Contemporary English Version) Onani kuti zimene timalankhula sikuti zimangosonyeza munthu amene timalakalaka titakhala, koma zimasonyezanso munthu amene tili panopa. Ndipotu ngati mumatukwana chifukwa chongotengera anzanu ndiye kuti mukuonetseratu kuti ‘mukutsata unyinji’ ndiponso kuti simutha kuganiza panokha. (Eksodo 23:2)

Ndipotu kutukwana kumasonyeza zinthu zina zambiri zokhudza khalidwe lanu. Katswiri wachilankhulo, dzina lake James V. O’Connor, anati: “Anthu amene amatukwana nthawi zambiri sakhala ogwirizanika, amakonda kutsutsa kapena kunyoza ena, kukayikira, kukwiya, kukangana, ndiponso kudandauladandaula.” Mwachitsanzo, anthu amene amakonda kutukwana chinachake chikangolakwika amasonyeza kuti amafuna kuti zinthu zonse zizingoyenda bwino nthawi zonse. Amakhala ngati kuti sadziwa chochita akalakwitsa penapake. Komanso, O’Connor anati, anthu amene satukwana, “nthawi zambiri amakhala anthu okhazikika maganizo, . . . ochita zachikulu, omwe [angathe] kuthana bwinobwino ndi zinthu zopweteketsa mtima za tsiku ndi tsiku.” Kodi pamenepa, inuyo mungakonde mutakhala m’gulu liti la anthu?

Kutukwana kumawonongetsa mbiri yanu. N’kutheka kuti monga achinyamata ambiri, inunso mumaganizira za maonekedwe anu. Mumafuna kuti muzioneka bwino. Koma kodi mukudziwa kuti zolankhula zanu zimasintha kwambiri mmene anthu amakuonerani kuposa maonekedwe anu? Zolankhula zanu zingakhudze zinthu monga

▪ Anthu amene angakopeke nanu n’kukhala anzanu

▪ Mwayi wanu wopeza ntchito

▪ Ulemu umene ena angakupatseni

Komanso dziwani kuti nthawi zambiri ulemu wonse umene anthu angakhale nawo akangotiona kumene umatha akatimva tikulankhula zopusa. Taonani mfundo inanso imene ananena O’Connor: “Mosadziwa, nthawi zambiri mumataya mwayi wokhala paubwenzi ndi munthu winawake, kapena mumachititsa kuti winawake akuthaweni, kapenanso mumadzitayira ulemu kwambiri chifukwa cha kutukwana kwanuko.” Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Ngati mumakonda kutukwana, dziwani kuti amene amapwetekedwa nazo ndi inu nomwe.

Kutukwana kumasonyeza kusalemekeza Mlengi wa mlomo. Taganizirani kuti mnzanu mwamugulira shati kapena bulauzi. Kodi mungamve bwanji ngati mutaona kuti chovala chija wachiika pakhomo kuti azipondapo polowa m’nyumba? Ndiyeno taganizirani mmene Mlengi amamvera akaona tikugwiritsira ntchito mphatso yathu ya kulankhula m’njira yolakwika? N’zosadabwitsa kuti Mawu a Mulungu amati: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.”—Aefeso 4:31.

Mungathe kuona kuti ngati mumatukwana m’pofunika kuti musiye. Komano mungatani ngati khalidweli linakulowererani kwambiri?

Choyamba: Zindikirani kuti m’pofunika kusintha. Simungasiye kutukwana ngati simukuzindikira kuti kusiya khalidweli kungakupindulitseni kwambiri. Kodi ndi mfundo zotani m’munsimu zimene inuyo zingakulimbikitseni kuti musiye kutukwana?

□ Kusangalatsa Mlengi wa mlomo

□ Kuyamba kupatsidwa ulemu kwambiri

□ Kudziwa mawu ena atsopano

□ Kusintha kuti ndikhale munthu wolongosoka

Chachiwiri: Dziwani chimene chimakuchititsani kutukwana. Melanie anati: “Ndikamatukwana ndimadziona kuti siine munthu wosewera nane ayi. Sindinkafuna kuti anthu azinditola ayi. Ndinkafuna kuti aliyense azindiopa, kuti ndizitha kum’masula wina aliyense, monga mmene anzanga onse ankachitira.”

Nanga inuyo bwanji? Kuti mudziwe mmene mungathetsere vutoli, m’pofunika kuti mumvetse kaye chimene chimakuchititsani kuti muzitukwana. Mwachitsanzo, ngati mumatukwana chifukwa choti aliyense amatero, muyenera kuphunzira kuchita zinthu panokha. Mukamaona kuti kuyendera mfundo zanu n’konyaditsa, ndiye kuti mukukula, ndipo zimenezi zingakuthandizeni kwambiri kuthetsa khalidwe lotukwana.

Chachitatu: Pezani mawu ena ofotokozera maganizo anu. Musaganize kuti mungathetse vutoli poyesetsa kukumbukira kuti musatukwane panthawi imene mukufuna kutero. Kuti muthane ndi chizolowezi choipachi muyeneranso kuvala “umunthu watsopano.” (Aefeso 4:22-24) Umunthu umenewu umakuthandizani kuphunzira kukhala munthu wodziletsa kwambiri, wodzipatsa ulemu, komanso wopatsa ulemu anthu ena.

Malemba otsatirawa angakuthandizeni kuvala ndi kusunga, umunthu watsopano.

Akolose 3:2: “Zikani maganizo anu pa zinthu za kumwamba.”

Mfundo imene mungatolepo ndi yakuti: Phunzirani kukonda kwambiri zinthu zabwino. Zimene mumaganiza zimakhudza zolankhula zanu.

Miyambo 13:20: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”

Mfundo imene mungatolepo ndi yakuti: Zolankhula za anzanu zingakulowelereni inunso.

Salmo 19:14: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova.”

Mfundo imene mungatolepo ndi yakuti: Yehova amaona mmene timagwiritsira ntchito mphatso ya kulankhula.

Kodi mukufunikira thandizo lina? Gwiritsirani ntchito ndandanda ili pamunsiyi kuti muone ngati mukuchepetsa mawu otukwana mukamalankhula. Mungadabwe kwambiri kuona kuti sizikutengerani nthawi kuti mupeze mawu ena abwino, osati otukwana.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha maina m’nkhani ino.

^ ndime 8 Akhristu sayenera kuona kutukwana ngati nkhani yamasewera, chifukwa Baibulo limati: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu.” “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere.”—Aefeso 4:29; Akolose 4:6.

ZOTI MUGANIZIRE

Kodi kutukwana kungakhudze bwanji

▪ anthu amene angakopeke nanu n’kukhala anzanu?

▪ mwayi wanu wopeza ntchito?

▪ mmene ena amakuonerani?

[Tchati patsamba 21]

ONANI MMENE MWASINTHIRA

Lolemba Lachiwiri Lachitatu Lachinayi Lachisanu Loweruka Lamlungu

Mlungu 1 ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․

Mlungu 2 ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․

Mlungu 3 ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․

Mlungu 4 ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․ ․․․․․․․ ․․․․․․

[Chithunzi patsamba 20]

Mphatso yamtengo wapatali simungaigwiritse ntchito molakwika. Nanga bwanji mphatso ya kulankhula?