Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Kugwiritsira Ntchito Njira za Kulera?

Kodi N’kulakwa Kugwiritsira Ntchito Njira za Kulera?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi N’kulakwa Kugwiritsira Ntchito Njira za Kulera?

INU mukuganiza bwanji? Kodi kungakhale kulakwa kuti munthu ndi mkazi wake azigwiritsira ntchito njira za kulera? Mwina mungayankhe funsoli mogwirizana ndi chipembedzo chanu. Tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa kuti njira iliyonse imene imalepheretsa munthu kubereka ndi “yoipa kwambiri.” Zimene tchalitchichi chimaphunzitsa zimalimbikitsa maganizo oti mwamuna ndi mkazi wake akamagonana pasamakhale chilichonse chimene chingalepheretse mkazi kutenga pathupi. Choncho, Tchalitchi cha Katolika chimati kugwiritsira ntchito njira za kulera “n’kulakwa.”

Anthu ambiri amavutika kuvomereza mfundo imeneyi. Pankhani imeneyi, nyuzipepala ya Pittsburgh Post-Gazette inati, “Akatolika ambiri ku United States amati tchalitchi chiyenera kuvomereza njira za kulera. . . . Ndipo tsiku lililonse, anthu ambirimbiri amaswa lamulo limeneli.” Mmodzi mwa anthuwa ndi Linda yemwe ali ndi ana atatu. Iyeyu anavomereza mosabisa kuti amagwiritsira ntchito njira za kulera koma anati: “Mogwirizana ndi chikumbumtima changa, sindiona kuti ndikuchimwa.”

Kodi Mawu a Mulungu amati chiyani pankhani imeneyi?

Moyo Ndi Wamtengo Wapatali

Mulungu amaona kuti moyo wa mwana ndi wamtengo wapatali, ngakhale pamene ukungoyamba kumene. Mfumu Davide ya ku Isiraeli inalemba mouziridwa kuti: “Munandiumba ndisanabadwe ine. . . . Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.” (Salmo 139:13, 16) Moyo umayamba mayi akatenga pathupi, ndipo Chilamulo cha Mose chimasonyeza kuti munthu ankaimbidwa mlandu chifukwa chovulaza mwana wosabadwa. Ndipotu, lemba la Eksodo 21:22, 23 limati, ngati mkazi wapakati kapena mwana wosabadwa wamwalira chifukwa choti amuna awiri anali kumenyana, nkhaniyo azipita nayo kwa oweruza. Oweruzawo ankaona mmene nkhaniyo inachitikira ndipo ngati anthu omenyanawo anachita dala, chilango chake chinali “moyo kulipa moyo.”

Malamulo amenewo amakhudza njira za kulera chifukwa zikuoneka kuti njira zina zolerera zimachotsa pathupi. Njira zimenezi sizigwirizana ndi mfundo ya Mulungu yoti moyo ndi wofunika kuulemekeza. Komabe, njira zambiri za kulera sizichotsa pathupi. Nanga bwanji ponena za kugwiritsira ntchito njira zolerera zimenezi?

M’Baibulo mulibe lamulo lililonse loti Akhristu aziberekana. Mulungu anauza banja loyambirira ndiponso banja la Nowa kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” Koma sanaperekenso lamulo limeneli kwa Akhristu. (Genesis 1:28; 9:1) Choncho, mabanja angasankhe okha ngati akufuna kukhala ndi ana, ndiponso kuti akufuna kukhala nawo angati, kapena nthawi yomwe akufuna kukhala nawo. Komanso Malemba saletsa kulera. Choncho, malingana ndi zimene Baibulo limanena, mwamuna ndi mkazi akamagwiritsira ntchito njira za kulera zimene sizichotsa pathupi, chimenecho n’chosankha chawo. Nanga n’chifukwa chiyani Tchalitchi cha Katolika chimaletsa kugwiritsira ntchito njira zolerera?

Nzeru za Anthu Zitsutsana ndi Nzeru za Mulungu

Mabuku a Tchalitchi cha Katolika amafotokoza kuti munali m’zaka za m’ma 100 C.E. pamene anthu odzitcha Akhristu anatengera mfundo ya Asitoiki yomwe imati cholinga chimodzi chokha chovomerezeka cha kugonana m’banja ndi kubereka ana. Choncho mfundo imeneyi ndi maganizo a anthu basi osati a m’Baibulo. Anthu apitiriza kukhala ndi maganizo amenewa mpaka pano ndipo akatswiri osiyanasiyana a maphunziro a Chikatolika amavomereza maganizowa. * Komabe, zimene amaphunzitsazi zachititsa anthu kukhala ndi maganizo akuti kugonana m’banja n’cholinga chongosangalala ndi tchimo ndipo kugonana pali njira zolepheretsa mkazi kutenga pathupi ndi tchimonso. Komatu zimenezi si zimene Malemba amaphunzitsa.

Buku la m’Baibulo la Miyambo limafotokoza mwandakatulo chisangalalo chimene mwamuna ndi mkazi wake amakhala nacho pogonana. Limati: “Imwa madzi a m’chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m’kasupe mwako. . . . Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula naye. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, mawere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.”—Miyambo 5:15, 18, 19.

Kugonana kwa mwamuna ndi mkazi wake ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Koma cholinga chake si kungobereka ana basi. Komanso kugonana kumathandiza mwamuna ndi mkazi kusonyezana chikondi. Choncho ngati banja lasankha kugwiritsira ntchito njira za kulera n’cholinga choti mkazi asatenge pathupi, chimenecho n’chosankha chawo, ndipo wina aliyense asawaweruze.—Aroma 14:4, 10-13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 M’zaka za m’ma 1200, Papa Gregory IX anakhazikitsa lamulo limene buku lina lakuti New Catholic Encyclopedia limati ndi “lamulo loyamba lokhazikitsidwa ndi papa loti anthu asamagwiritsire ntchito njira za kulera.”

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi pali tchimo lililonse ngati mwamuna ndi mkazi wake agonana?—Miyambo 5:15, 18, 19.

▪ Kodi Akhristu ayenera kuganizira chiyani akamagwiritsira ntchito njira za kulera?—Eksodo 21:22, 23.

▪ Kodi ena ayenera kuona motani mabanja amene amagwiritsira ntchito njira za kulera?—Aroma 14:4, 10-13.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Mulungu anauza banja loyambirira ndiponso banja la Nowa kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” Koma sanaperekenso lamulo limeneli kwa Akhristu