Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi n’zotheka Kusiya Zizoloŵezi Zoipa?

Kodi n’zotheka Kusiya Zizoloŵezi Zoipa?

Lingaliro la Baibulo

Kodi n’zotheka Kusiya Zizoloŵezi Zoipa?

WOLEMBA nkhani wina wotchedwa Mark Twain ananena mwanthabwala kuti: “Ngati kunja kuno kuli chinthu chosavuta mapeto, chinthu chake ndicho kusiya kusuta fodya. Ineyo ndikutero chifukwa ndasiyapo kusuta fodya kambirimbiri.” Anthu ambiri angavomereze kuti zosoŵetsa mtendere zimene Twain ananenazi zawachitikirapo. Ngakhale kuti amadziŵa kuti kukhala ndi zizoloŵezi zinazake n’kulakwa mwinanso n’kudziwononga kumene, amadziŵanso kuti m’povuta kwambiri kudziletsa ndiponso kusiyiratu zizoloŵezizo. Pamatha zaka zambiri kuti zizoloŵezi zina ziyale mizu ndipo zimakhala zovuta kwambiri kuzisiya. Kuyesa kusintha zizoloŵezi zotere kumafoola mwinanso kupweteka kumene.

Dr. Anthony Daniels, dokotala amene amagwira ntchito pandende inayake, ananena kuti akaidi nthaŵi zambiri amanena kuti khalidwe ndiponso zilakolako zawo zoipa anafika pozizoloŵera mapeto. Iwowo amati munthu akangofika pozoloŵera kwambiri chinthu chinachake, “ndiye kuti wapita ameneyo basi, sangachitirenso mwina kuti asiye chilakolako chakecho.” Komatu zimenezi zikanakhala zoona, si bwenzi tikuimbidwa mlandu tikapalamula chifukwa cha zilakolako zathu. Koma kodi n’zoonadi kuti sitingachitire mwina kupatulapo kutsatira zilakolako zathu basi? Kapena kodi n’zotheka ndithu kuthetsa zizoloŵezi zoipa? Kuti timve zenizeni tiyeni tione zimene Baibulo limanena.

Mtima Umafuna Koma Zimavuta Kuchita

Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu amaona ntchito zathu, ngati zili zabwino kapena ayi. (Aroma 14:12) Komanso amafuna kuti tizikhala mogwirizana ndi makhalidwe ake olungama. (1 Petro 1:15) Pakuti ndiye Mlengi wathu, amadziŵa zinthu zimene zingatipindulitse, ndipo mfundo zake za makhalidwe abwino zimaletsa zizoloŵezi zambiri zamasiku anozi. (1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 5:19-21) Komabe iye salamulira anthu opanda ungwirofe kuchita zinthu zimene sitingathe ndiponso iye amatimvetsa.—Salmo 78:38; 103:13, 14.

Motero wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?” (Salmo 130:3) Inde, Yehova amadziŵa bwino lomwe kuti “ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Chibadwa chathu, zofooka zathu zoyamwira, ndiponso zoipa zimene takumana nazo m’moyo wathu zimatichititsa kuti tilephere kupeŵeratu maganizo ndi zilakolako zonse zoipa. Motero, Yehova mwachikondi chake, safuna kuti tichite kufika pomakhala ngati anthu angwiro.—Deuteronomo 10:12; 1 Yohane 5:3.

Komabe, poti Mulungu amatimvetsa si ndiye kuti tisiye kuganizira zodziletsa kukhala ndi zilakolako zoipa. Inde, mtumwi Paulo anavomera kuti ngakhale iyeyo amene, anasautsika kwambiri ndi zilakolako zoipa, komatu iyeyu sanadzilekerere ayi. (Aroma 7:21-24) Iye anati “ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo.” Anatero n’cholinga chotani? Anati poopa kuti “ndingakhale wotayika ndekha.” (1 Akorinto 9:27) Inde, kudziletsa n’kofunika polimbana ndi zilakolako ndiponso zizoloŵezi zathu zoipa komanso pofuna kuzigonjetseratu.

Mungathe Kusintha

Asayansi ya za khalidwe la anthu amati mofanana ndi zizoloŵezi zabwino, zizoloŵezi zoipa munthu amachita kuziphunzira m’kupita kwa nthaŵi. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti n’zothekanso kuphunzira kusiya zizoloŵezi zoipa! Zingatheke motani? Anthu ena amene analemba buku lina lonena za mmene mungachepetsere kuvutika maganizo, anati: “Ganizirani za ubwino wosiyira chizoloŵezi chanucho.” Kenaka “lembani zinthu zabwino zonse zimene mungapindule nazo ngati mutasintha khalidwe lanulo.” Inde, kuganizira kwambiri za ubwino wosintha chizoloŵezi chathu choipa kungatithandize kusintha.

Taganizirani zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuchita, zakuti tikhale ‘atsopano mu mzimu wa mtima wathu.’ (Aefeso 4:22, 23) Mzimu umene ananenawo umatanthauza zinthu zimene zimakonda kukhala mumtima mwathu. Munthu amakhala watsopano mu mzimu umenewu poyamba kukonda kwambiri Mulungu ndi kumvetsetsa ubwino wotsanzira makhalidwe ake. Kudziŵa kuti mukusangalatsa Yehova kumakulimbikitsani kusintha zochita zanu.—Salmo 69:30-33; Miyambo 27:11; Akolose 1:9, 10.

Inde, n’zoona kuti kuthetsa zizoloŵezi zoipa zimene takhala nazo kwa zaka zambirimbiri n’kovuta. Tisaganize kuti n’kwapafupi. Imafika nthaŵi ina yomwe mumafooka n’kubwerera m’mbuyo. Koma musataye mtima podziŵa kuti pang’ono ndi pang’ono mudzayamba kuzoloŵera. Mukamalimbikira, khalidwe lanu latsopanolo mumayamba kulizoloŵera.

Munthu amene amakonda Mulungu ayenera kudziŵa kuti Mulungu sangam’taye ndiponso kuleka kumudalitsa. Paulo analonjeza kuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma . . . adzapereka populumukira kuti muthe kupirira chiyesocho.” (1 Akorinto 10:13) Posachedwapa, Yehova Mulungu adzachotsa dongosolo loipali pamodzi ndi zoipa zake zonse zimene zimayika anthu pachiyeso, ndiponso zilakolako zake zonse. (2 Petro 3:9-13; 1 Yohane 2:16, 17) Anthu opanda ungwiro onse amene adzapulumuke pamenepa, m’kupita kwa nthaŵi angathe kudzawachiritsa mavuto awo onse am’thupi, ndi am’maganizo moti adzatheratu mpaka kalekale. “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima,” analonjeza choncho Mulungu. (Yesaya 65:17) N’zosakayikitsa kuti zina mwa “zinthu zakale” zimenezi zidzakhala zilakolako zovutitsa. Kodi ichi si chifukwa chomveka chotilimbikitsa kuti tiziyesetsa kulimbana ndi zizoloŵezi zoipa?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 31]

MMENE MUNGASIYIRE ZIZOLOŴEZI ZOIPA

1. Zindikirani ndi kuvomereza kuti muli ndi zizoloŵezi zoipa. Dzifunseni kuti, ‘Kodi chizoloŵezi chimenechi chimandipindulitsadi? Kodi chimawanyong’onya anthu ena? Kodi chimawononga thanzi langa, chuma changa, moyo wanga, anthu am’banja mwanga, kapena kodi chimandisoŵetsa mtendere? Kodi ndingapindule bwanji pa moyo wanga ngati nditasiya chizoloŵezichi?’

2. Pezani chizoloŵezi chabwino choloŵa m’malo mwa choipacho. Mwachitsanzo kodi mumakhala nthaŵi yaitali mutatsegula intaneti, mwina n’kumayang’ana zinthu zosayenerera? Ndiyetu mungachite bwino ngati nthaŵi imeneyo mutaisandutsa nthaŵi yanu yoŵerenga zinthu zaphindu, kapena yochita maseŵera olimbitsa thupi.

3. Onani ngati mukusinthadi. Tsiku lililonse ganizirani kwa mphindi zochepa chabe za mmene mukusinthira. Ngati munabwerera m’mbuyo pang’ono, onani bwinobwino kuti n’chiyani chachititsa kuti mutero.

4. Pemphani chithandizo kwa ena. Uzani anzanu ndiponso anthu a m’banja mwanu kuti mukufuna kusiya chizoloŵezicho, ndipo apempheni kuti azikukumbutsani mukamaoneka kuti mukufuna kubwerera m’mbuyo. Kambiranani ndi anthu ena amene anakwanitsa kuthetsa chizoloŵezi chotero.—Miyambo 11:14.

5. Musapupulume. Musaganize kuti mungasinthe lero ndi lero. Zizoloŵezi zina zimene mwakhala nazo kwa zaka zambirimbiri zingakuvuteni kuzisiya mwamsanga.

6. Pempherani kwa Mulungu. Mulungu angakuthandizeni kusiya chizoloŵezi china chilichonse choipa.—Salmo 55:22; Luka 18:27.