Zimene Makanda Amafunikira Ndiponso Zimene Amafuna
Zimene Makanda Amafunikira Ndiponso Zimene Amafuna
MWANA wakhanda akangobadwa, amafunikira chisamaliro chapadera, monga kumusisita ndi kumukhudza. Madokotala ena amati maola 12 oyambirira mwana akangobadwa amakhala ofunika kwambiri kwa mayi ndi mwana wakeyo. Iwo amati mayi akachira kumene, zimene iye ndi mwanayo amafuna kwambiri “si kugona kapena chakudya ayi, koma kusisitana ndi kukumbatirana ndi kuyang’anana ndiponso kumvetserana.” *
Mwachibadwa, makolo amayesetsa kugwira mwana wawo wakhanda bwinobwino, kumuyangata mwachikondi, kumusisita, ndi kukhala naye pafupi kwambiri posonyeza kumukonda. Nayenso mwanayo amayamba kukonda kwambiri makolo akewo ndipo amawasangalalira. Mgwirizano umenewu umakhala wamphamvu kwambiri moti makolo satopa ayi ndipo amalolera kuchita chilichonse chimene angathe kuti asamalire khanda lawolo.
Komano popanda makolo omukonda, mwanayo akhoza kunyentchera mpaka kufa. Ndiye n’chifukwa chake madokotala ena amaona kuti ndi bwino kuti mwana akangobadwa aperekedwe kwa amayi ake. Amati ndi bwino kuti mphindi zoyambirira 30 kapena 60 mwana akangobadwa azimusiya kaye ndi amayi ake.
Ngakhale kuti anthu ena amalimbikitsa zoti pazikhala mgwirizano woterewu, n’zovuta, mwinanso sizitheka kumene, m’zipatala zina kuti mwana ndi amayi ake aziyamba akhala kaye limodzi mwanayo akangobadwa. Nthaŵi zambiri, ana akangobadwa amawasiyanitsa ndi amayi awo chifukwa choopa kuti mwana angatenge matenda enaake opatsirana. Komano pali umboni wosonyeza kuti matenda oopsa opatsirana angachepe ndithu ngati ana ongobadwa kumene atamakhala ndi amayi awo. Choncho zipatala zambiri zayamba kugwirizana ndi mfundo yakuti makanda akangobadwa aziyamba akhala kaye ndi amayi awo kwa nthaŵi ndithu.
Kuopa Kuti Sadzamukonda
Azimayi ena sakonda kwambiri mwana wawo akamuona koyamba. Choncho amakayikira n’kumati, ‘Kodi ndidzathadi kumukonda?’ Inde, n’zoona kuti azimayi ena sakonda mwana wawo wakhanda akamuona koyamba. Koma zimenezo si zodandaulitsa kwenikweni.
Ngakhale mayi atalephera kukonda mwana wake nthaŵi yomwe wangobadwa kumene, amatha kudzamukonda kwambiri pakapita kanthaŵi. “Munthu akamabereka sadziŵiratu kuti mwana wakeyo adzamukonda kapena adzaipidwa naye,” anatero mayi wina amene anaberekapo. Komabe, ngati muli woyembekezera ndipo muli ndi nkhaŵa, zingakhale bwino kuuza azamba anu nthaŵi idakalipo. Muwauze momveka bwino kuti mwanayo akabadwa mungakonde kukhala naye pakatha nthaŵi yotani ndiponso kwa nthaŵi yaitali bwanji.
“Tandiyankhuleni!”
Zikuoneka kuti ubongo wa makanda suvutika kugwira zinthu zinazake pa nthaŵi inayake yokha basi. Nthaŵiyo ikadutsa sizithekanso kugwira msanga zinthuzo. Mwachitsanzo, ubongo wa mwana umagwira chinenero mosavutikira kwenikweni, ngakhale zitakhala zinenero zingapo. Koma zimaoneka kuti nthaŵi yabwino kwambiri yoti mwana aphunzire chinenero mosavuta imayamba kutha mwanayo akafika zaka pafupifupi zisanu.
Mwana akakwanitsa zaka 12 kapena 14, zimakhala zovuta kwambiri kuti aphunzire chinenero china. Malingana ndi kunena kwa dokotala woona za ubongo pachipatala china cha ana dzina lake Peter Huttenlocher, akuti nthaŵi imeneyo ndi imene “mbali ya ubongo imene imathandiza munthu kudziŵa chinenero imakhala itayamba kuchepa mphamvu.” Ndiye n’zoonekeratu kuti zaka zingapo zoyambirira m’moyo zimakhala nthaŵi yofunika kwambiri yoti munthu adziŵe chinenero!
Kodi ana akhanda amakwanitsa bwanji chintchito chophunzira kuyankhula, komwe n’kofunika kwambiri panthaŵi yawo yonse yophunzira kumvetsa zinthu bwinobwino? Amatero makamaka chifukwa makolo awo amayankhulitsana nawo. Ana amatsanzira makamaka zochita za anthu. “Mwana wa khanda . . . amatsanzira mawu a amayi ake,” anatero Barry Arons wa pasukulu yotchedwa Massachusetts Institute of Technology. Komano n’zochititsa chidwi kuti ana akhanda satsanzira mawu a chinthu chilichonse. Arons anati mwana wakhanda “akamva mawu a amayi ake ndi phokoso losokosera la chinthu chinachake pa nthaŵi imodzimodziyo, satsanzira chinthucho koma amayi akewo basi.”
Makolo a chikhalidwe chosiyanasiyana akamayankhula ndi ana awo akhanda amayankhula mwa njira yofanana powauza zinazake. Kholo likamayankhula mwachikondi kwa mwana wakhanda, mtima wa mwanayo umawonjezera kugunda kwake. Akuti kuyankhula ndi mwana mwa njira imeneyi kumathandiza kuti mwanayo afulumire kugwirizanitsa mawu ndi zinthu zimene mawuwo akuimira. Popanda kutulutsa mawu, mwana wakhandayo amakhala akunena kuti: “Tandiyankhuleni!”
“Tandiyang’aneni!”
Tsopano zinadziŵika kuti mwana amayamba kuika mtima wake wonse kwa munthu amene akumusamalira m’chaka chake choyamba kapena kuposa pang’ono, ndipo nthaŵi zambiri munthuyo amakhala amayi ake. Mwanayo akaona kuti ali wotetezeka bwino, amamasukiranso anthu ena kuposa mmene amachitira ana amene amasoŵa chisamaliro choterocho kwa makolo awo. Akuti mgwirizano woterewu pakati pa mwana ndi amayi ake umafunika kuti ukhale utakhazikitsidwa pamene mwanayo azikwanitsa zaka zitatu.
Kodi chingachitike n’chiyani mwana wakhanda atanyalanyazidwa panthaŵi yofunika kwambiri imeneyi imene maganizo ake amakhala oti angathe kutengeka mosavuta ndi zochita za anthu ena? Martha Farrell Erickson, yemwe anakhala akutsata bwino zochita za azimayi 267 ndi ana awo kwa zaka zoposa 20, anatchula mfundo iyi: “Kunyalanyaza mwana wakhanda kumangopha pang’onopang’ono chilakolako chake chochita zinthu mpaka [mwanayo] safunanso kwenikweni kugwirizana
ndi anthu ena kapena kudziŵa zinthu zina ndi zina.”Poyesetsa kufotokoza mmene iye amaonera kuopsa kwake kwa kunyalanyaza zimene mtima wa mwana umafuna, Dr Bruce Perry wa pachipatala cha ana cha Texas Children’s Hospital, anati: “Mutandiuza kuti ndisankhe, kutenga mwana wa miyezi isanu ndi umodzi n’kumuthyolathyola mafupa onse m’thupi mwake, kapena kunyalanyaza zofuna mtima wake kwa miyezi iŵiri, ndinganene kuti zingakhale bwino kwa mwanayo kumuthyolathyola mafupa onse m’thupi mwake.” N’chifukwa chiyani anatero? A Perry anati, “mafupa n’ngotheka kulumikizananso, koma ngati miyezi iŵiri yofunika kwambiri poumba ubongo wa mwana itadutsa osamuchitira zofuna mtima wake, ndiye kuti mpaka kalekale mwanayo amadzakhala ndi ubongo wosokonekera.” Anthu ena savomereza kuti vutoli limakhaladi mpaka kalekale. Komabe, kafukufuku wa asayansi amasonyeza kuti ndi bwinodi kwambiri kulabadira zimene mtima wa mwana wakhanda umafuna.
“Mwachidule, [makanda] amafunitsitsa kukonda ena ndiponso kukondedwa,” limatero buku lonena za makanda lakuti Infants. Nthaŵi zambiri mwana akamalira amakhala akupempha makolo ake kuti: “Tandiyang’aneni!” Ndi bwino kuti makolo azimuyankha mosonyeza kuti amamuganizira kwambiri. Mwanjira imeneyi, mwanayo amazindikira kuti akhoza kudziŵitsa ena zimene akufunikira. Amakhala akuphunzira kucheza ndi anthu.
‘Kodi Sindimuzoloŵeza Zoipa Mwanayo?’
‘Kodi ndikamachitapo kanthu mwanayo akangolira, sindimuzoloŵeza zoipa?’ mungafunse choncho. Mwinadi n’kutheka kutero. Anthu amayankha funso limeneli m’njira zosiyanasiyana kwambiri. Popeza kuti mwana aliyense amakhala wosiyana ndi mnzake, makolo makamaka ayenera kuona kuti ndi njira yotani imene imawayendera bwino. Komabe, zimene ofufuza apeza posachedwapa zikusonyeza kuti mwana wakhanda akakhala ndi njala, akakhala kuti sakumva bwino, kapena akakhala kuti wakhumudwa, mbali yathupi lake yomudziŵitsa zimenezi imatulutsa timadzi timene timam’pangitsa kuti avutike maganizo. Iye amasonyeza kuvutikako polira. Akuti kholo likachitapo kanthu posamalira khandalo moyenerera, khololo limayamba kuthandizira mbali ya ubongo wa mwanayo imene imamuthandiza kuphunzira kuti azitha kukhazikitsa mtima pansi yekha. Komanso Dr Megan Gunnar ananena kuti mwana yemwe walabadiridwa mwamsanga amatulutsa timadzi totere tochepa. Ndipo ngakhale atati wakhumudwa, timadzito timasiya msanga.
“Ndipotu ana amene nthaŵi zonse amawasamala msanga, makamaka amene amakhala atha miyezi 6 mpaka 8 atabadwa, ndithudi amalira pang’ono powayerekeza ndi ana amene amangosiyidwa kuti azidzilirira,” anatero a Erickson. Ndi bwinonso kwambiri kusinthasintha zimene mumachita mwana wanu akalira. Ngati mumachita zimodzimodzi nthaŵi iliyonse mwanayo akalira, kaya
kungom’patsa bere kapena kungom’gwira basi, akhoza kuzoloŵeradi zoipa. Nthaŵi zina, kungosonyeza kuti mwamva kulira kwake poyankhula timawu tinatake kungakhale kokwanira. Kapena kungom’yandikira n’kumunong’oneza timawu tinatake kungathandize. Mwinanso kungom’sisita pamsana kapena pamimba kungathandizenso.“Kulira ndiyo ntchito ya mwana.” Umatero mwambi wina wa kumayiko ena a ku Asia. Kwa mwana wakhanda, kulira ndiyo njira yake yaikulu yofotokozera zimene akufuna. Kodi mungamve bwanji ngati nthaŵi zonse mukapempha chinachake amangokunyalanyazani? Ndiye mwana wanu, yemwe sangachite chilichonse popanda wom’samalira, angamve bwanji ngati nthaŵi zonse akafuna thandizo amangonyalanyazidwa? Koma kodi ndani ayenera kuchitapo kanthu mwana akalira?
Kodi Ndani Ayenera Kusamalira Mwana?
Kalembera wa posachedwapa ku United States anasonyeza kuti ana 54 pa 100 alionse akangobadwa mpaka pamene adzafike mu giredi 3, nthaŵi ndi nthaŵi amasamalidwa ndi anthu ena osati makolo awo. Makolo ambiri amatha kuloŵa ntchito ziŵiri kuti apeze zinthu zofunikira m’moyo. Ndipo, azimayi ambiri akatsala pang’ono kuchira amatenga tchuthi, zikakhala zotheka, kuti akasamalire mwana wawo wakhanda kwa masabata kapena miyezi ingapo. Komano kodi ndani amene amasamalira mwanayo tchuthicho chikatha?
Kunena zoona, palibe malamulo okakamiza munthu zoti achite pankhani imeneyi. Komabe, ndi bwino kukumbukira kuti panthaŵi yofunika kwambiri imeneyi mwana wakhanda amakhalabe adakali wanthete kwambiri. Makolo onse aŵiri afunika kuganizira mozama kwambiri nkhaniyi. Polingalira zoti achite, ndi bwino kuti makolowo aganizire mosamala kwambiri zimene angasankhe kuchita.
“Tsopano zayamba kuonekeratu kwabasi kuti ngakhale ana athu titawasiya kuti aleredwe ndi masukulu abwino zedi olera ana, zimenezi sizingaloŵe m’malo nthaŵi imene ana amafunikira yokhala ndi amayi ndi abambo awo,” anatero Dr. Joseph Zanga, wa pasukulu yoona za matenda a ana, yotchedwa American Academy of Pediatrics. Akatswiri ena adandaulapo kuti ana akhanda amene amasungidwa panyumba zosamalira ana sakhala omasukirana ndi munthu amene akuwasamalira mongadi mmene anawo amafunira.
Azimayi ena a pantchito, pozindikira zinthu zimene ana awo amafunikira kwambiri, aganizapo zongokhala pakhomo kusiyana n’kuti azisiya anthu ena akuwagwirira ntchito youmba mitima ya ana awo. Mayi wina anati: “Ndine wokhutira kwambiri ndi moyo wanga ndipo ndimakhulupirira kuti palibenso ntchito ina imene ingandikhutiritse kuposa yolera ana anga.” Inde, n’zoona kuti chifukwa cha mavuto a zachuma azimayi onse sakwanitsa kuchita zoterozo. Makolo ambiri sangachitire mwina koma kupititsa ana awo ku masukulu olera ana, choncho amangoyesetsa kusamalira ana awo ndi kuwakonda mpata wokhala nawo ukapezeka. Ndiponso n’zochepa zimene makolo ambiri amene sali pabanja angachitepo pankhaniyi, koma amayesetsa kwambiri kulera ana awo, ndipo zinthu zimawayendera bwino.
Kulera ana ndi ntchito yosangalatsa kwambiri. Komanso ndi ntchito yovuta, yolira zambiri. Nanga mungaikwanitse bwanji?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Mu nkhanizi, Galamukani! ikufotokoza maganizo akatswiri otchuka pa zakaleredwe ka ana, popeza kuti zimene amapeza pa nkhani zoterezi akachita kafukufuku zimatha kuthandiza makolo ndi kuwadziŵitsa zina ndi zina. Komabe, n’zoona kuti zimene ofufuzaŵa amapeza kaŵirikaŵiri amadzaziunikanso n’kusintha kunena zina. Koma si choncho ndi mfundo za m’Baibulo zimene Galamukani! imagwirizana nazo kwathunthu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 22]
Makanda Osamveka Mawu
Madokotala ena a ku Japan akuti ana akhanda amene salira kapena kumwetulira ayamba kuchuluka. Dokotala wa pachipatala cha ana dzina lake Satoshi Yanagisawa amawatchula ana otereŵa kuti ndi makanda osamveka mawu. Kodi n’chifukwa chiyani anaŵa safuna kusonyeza mmene akumvera? Madokotala ena akukhulupirira kuti vutoli limayamba chifukwa makandawo amakhala akusoŵa kholo lawo. Vutoli amalinena kuti ndi vuto lochita kum’pangitsa dala mwana kusoŵa pogwira. Ena amati n’kutheka kuti mwana akamachita zinthu zosonyeza kuti mumuyankhule, ndiye inu n’kumangomunyalanyaza kapena kusamvetsa bwino zimene akutanthauza, mapeto ake amangosiya.
Dr. Bruce Perry, yemwe ndi dokotala wamkulu woona za matenda a maganizo pa chipatala cha Texas Children’s Hospital anati, mwana wakhanda akapanda kuthandizidwa panthaŵi imene ubongo wake suvuta kugwira zinthu, mbali ya ubongowo imene imam’thandiza kumvetsa zofuna za anthu anzake singakule. Ngati zofuna za mtima wake zitanyalanyazidwa kwambiri, akhoza kudzakhala munthu wosamvera ena chisoni. Dr. Perry amakhulupirira kuti anthu ena amene amagwiritsira ntchito kwambiri mankhwala ozunguza bongo ndiponso ana osinkhukirapo amene amakhala ankhanza amakhala otero chifukwa chakuti ananyalanyazidwa adakali makanda.
[Chithunzi patsamba 23]
Mgwirizano wa kholo ndi mwana wakhanda umakula kwambiri akamayankhulana