Zoti Mudziŵe Pankhani ya Khirisimasi
Lingaliro la Baibulo
Zoti Mudziŵe Pankhani ya Khirisimasi
PADZIKO lonse anthu osaneneka akukonzekera Khirisimasi ya chaka chino cha 2002. N’kuthekatu kuti inunso muli m’gulu lomweli. Komanso n’kutheka kuti mwina simukhulupirira nawo zimene amatchalitchi amakhulupirira pankhani ya chikondwererochi. Kaya muli mbali iti pamenepa, mwina simungapeŵe zimene zimachitika chifukwa cha Khirisimasi. Zochitikazo zimakafika mpaka ku zamalonda ndi zisangalalo, ndipo izi zimachitika ngakhale kumayiko omwe si achikristu.
Kodi mumadziŵa zotani pankhani ya Khirisimasi? Kodi m’Baibulo chikondwerero cha kubadwa kwa Kristu amachitchula n’komwe? Kodi chikondwerero chotchuka chimenechi chomwe chimachitika pa December 25 paliponse chinayamba bwanji?
Kuletsa Mwambo wa Khirisimasi
Mutati mukhale ndi kanthaŵi ndithu koti mufufuze nkhani yokhudza za Khirisimasi, mupeza kuti chiyambi chake si chachikristu n’komwe. Akatswiri a Baibulo ambiri ochokera m’zipembedzo zosiyanasiyana amavomereza zimenezi. Poganizira zimenezo, mukhoza kuona kuti mpake ndithu kuti ku England, Nyumba ya Malamulo pa ulamuliro wa Cromwell inalamula m’chaka cha 1647 kuti tsiku la Khirisimasi likhale tsiku lolapa machimo kenaka m’chaka cha 1652 n’kuletseratu mwambowu. Aphungu a nyumba ya malamuloyi ankachita dala misonkhano yawo pa December 25 chaka chilichonse kuyambira m’chaka cha 1644 mpaka mu 1656. Penne L. Restad yemwe amadziŵa kwambiri mbiri yakale ananena kuti, “abusa omwe ankalalikira za kubadwa kwa Yesu ankatero kwinaku ali chewuchewu kuopa kumangidwa. Osamalira ntchito zina n’zina za tchalitchi ankawakhaulitsa powalipiritsa ndalama akakongoletsa matchalitchi awo pa Khirisimasi. Lamulo linkati patsikuli masitolo azitsegulidwa ngati mmene amachitira tsiku lina lililonse la ntchito.” Kodi n’chifukwa chiyani panali kukhwimitsa malamulo choncho? Akuluakulu a chipembedzo cha Puritan ankakhulupirira kuti sikunali kwabwino kuti tchalitchi chiziyambitsa miyambo imene m’Malemba munalibemo. Iwo ankalalikira ndi kugaŵira anthu mabuku otsutsiratu zikondwerero za pa Khirisimasi.
Nawonso anthu a ku North America ankadana nayo Khirisimasi. Kungoyambira m’chaka cha 1659 mpaka mu 1681, mwambo wa Khirisimasi unali woletsedwa ku Massachusetts Bay Colony. * Lamulo limene linakhazikitsidwa panthaŵi imeneyo linali lakuti anthu asamachite china chilichonse chosonyeza kukondwerera Khirisimasi. Onse ophwanya lamulo limeneli ankawakhaulitsa powalipiritsa ndalama. Sikuti anthu a chipembedzo cha Puritan ku New England okha ndiwo amene ankadana ndi chikondwerero cha Khirisimasi basi, panalinso magulu ena a m’chigawo chapakati kumeneko. Anthu a m’chipembedzo chotchedwa Quaker ku Pennsylvania sankafuna n’komwe kukondwerera nawo mwambowu ngati mmene sankafuniranso a m’chipembedzo cha Puritan aja. Buku lina limati “anthu a ku America atangolandira ufulu wodzilamulira, Elizabeth Drinker wa m’chipembedzo cha Quaker anagaŵa anthu a ku Philadelphia m’magulu atatu. Panali anthu ena a m’chipembedzo chomwechi omwe ‘sankaona tsiku [la Khirisimasi] ngati lapadera kuposa tsiku lina lililonse,’ ena ankakondwerera tsikuli pazifukwa za chipembedzo, ndipo enanso ‘ankangochita zinthu zopokosera ndiponso kumangomwa mowa.’ ”
Munthu wina wotchuka ndi kulalikira ku America yemwe anakulira m’banja lotsatira chipembedzo cha Calvin, dzina lake Henry Ward Beecher, Khirisimasi sankaidziŵa kwenikweni mpaka pamene anakwanitsa zaka 30. Iye analemba m’chaka cha 1874 kuti: “Khirisimasi ndinalibe nayo ntchito n’komwe.”
Nawonso matchalitchi a Baptist ndi Congregationalist sanapeze umboni uliwonse m’Malemba woti azikondwerera kubadwa kwa Kristu. Buku lina limati kwa nthaŵi yoyamba, Tchalitchi cha Baptist cha mumzinda wa Newport [ku Rhode Island] chinayamba kukondwerera nawo Khirisimasi kuyambira pa December 25, 1772. Apa n’kuti patatha zaka pafupifupi 130 chiyambitsidwireni tchalitchi choyamba cha Baptist ku New England.
Chiyambi cha Khirisimasi
Buku la Chikatolika lotchedwa New Catholic Encyclopedia limavomereza kuti: “Tsiku limene Yesu anabadwa silidziŵika. Mabuku a mauthenga abwino sasonyeza n’komwe tsiku kapena mwezi wake . . . Malingana ndi zimene H. Usener ananena . . . zimenenso anthu ophunzira ambiri amagwirizana nazo masiku ano, n’zakuti tsiku la kubadwa kwa Kristu analiika kuti likhale . . . (pa December 25 pakalendala ya Julius ndipo pa January 6 pakalendala ya Aigupto), chifukwa chakuti patsikuli dzuŵa likayamba kutuluka monga mwa nthaŵi zonse, anthu achikunja otsatira mulungu wotchedwa Mithra ankakondwerera tsiku la dies natalis Solis Invicti (kubadwa kwa dzuŵa losagonjetseka). Pa December 25, 274, Aurelian anali atalengeza kuti mulungu dzuŵa ndiye anali mtetezi wamkulu wa ufumuwo ndipo anam’patulira kachisi kumalo otchedwa Campus Martius. Khirisimasi inayambika nthaŵi imene mwambo wolambira dzuŵa unafika pakaindeinde ku Roma.”
Buku la Cyclopœdia la M’Clintock ndi Strong limati: “Mulungu sindiye amene anakhazikitsa mwambo wa Khirisimasi, ndipo mu [Chipangano Chatsopano] mulibe nkhani imeneyi. Tsiku limene Kristu anabadwa silingapezeke mu [Chipangano Chatsopano], kapenanso m’buku lina lililonse.”
“Chinyengo Chopanda Pake”
Poganizira zonsezi zimene tatchula, kodi Akristu enieni angachite nawo chikondwerero cha Khirisimasi? Kodi Mulungu angakondwere nazo zosakaniza kulambira kwake ndi zikhulupiriro ndiponso miyambo ya zipembedzo za anthu omwe sam’lambira iye? Pa Akolose 2:8 mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.”
Mtumwiyu analembanso kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali [Satana]? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?”—2 Akorinto 6:14, 15.
Poona umboni wosatsutsika womwe ulipowu, Mboni za Yehova sizichita nawo chikondwerero cha Khirisimasi. Potsatira Malemba, iwo amayesetsa kukhala ndi “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu” podzisunga okha ‘osachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.’—Yakobo 1:27.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Chigawochi chinakhazikitsidwa mu 1628 ndi a m’chipembedzo cha Puritan a ku England ndipo chinali chachikulu ndiponso chotsogola kwambiri panthaŵi imeneyo ku New England.
[Mawu Otsindika patsamba 24]
Nyumba ya malamulo ya ku England inaletsa mwambo wa Khirisimasi mu 1652
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Khirisimasi ndinalibe nayo ntchito n’komwe”—ANATERO HENRY WARD BEECHER, MBUSA WA KU AMERICA
[Chithunzi patsamba 25]
Anthu achikunja otsatira mulungu wotchedwa Mithras ndi mulungu dzuŵa (amene awasonyeza pa chosemacho ) anakondwerera tsiku la December 25
[Mawu a Chithunzi]
Musée du Louvre, Paris