Kukhala Mayi N’chintchito Chovuta
Kukhala Mayi N’chintchito Chovuta
Kukhala mayi ndi ntchito yosautsa komanso yosangalatsa. Azimayi amakhala ndi nthaŵi zina zosangalatsa zimene sangalole kusinthanitsa ndi chilichonse. Komabe nthaŵi zina azimayi ena amaona kuti zingathe kuwapengetsa misala. Helen anayerekeza moyo wake monga mayi ndi mpikisano wothamanga n’kumadumpha zinthu zotsekereza njira. Ndipo zimaoneka kuti ukathamanga kwa kanthaŵi ndithu zinthu zotchinga njira zija zimachuluka ndiponso zimanka zitalikiratalikira.
Azimayi amatha kusoŵa nthaŵi yopuma kapena yochezako ndi anzawo pofuna kuonetsetsa kuti akusamalira bwinobwino ana awo. Esther yemwe ali ndi ana asanu, anati: “Nthaŵi zonse ndimangokhala ndili chire. Ndilibenso nthaŵi yosamba mwachifatse, ngakhalenso yophika chakudya mwachifatse. Ndimakhala ndi maulendo oti ndipite koma sindipita, ndimalephera kukaona malo ena kapena kuchita zinthu zina zambiri. Koma sinditi ndachapa liti, ndipotu zonsezo ndimazipinda bwinobwino!”
Inde, n’zoona kuti azimayi ambiri akhoza kunenanso kuti pali zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa zimene amakumana nazo akamalera ana awo. Esther anati: “Nthaŵi zina mwana wako akamakumwetulira, kapena akamanena n’timawu tokoma kuti, ‘Zikomo kwambiri amayi,’ kapenanso akamakukupatira mosangalala zimakulimbikitsa kwambiri.” *
Amayi Akugwira Nawo Ntchito Yolembedwa
Vuto lalikulu limene lasokoneza ntchito yokhala mayi n’lakuti azimayi ambiri amachita ntchito zamayi pabanja komanso amapita kuntchito kuti athandize kusamala banjalo. Azimayi ambiri otere amakagwira ntchito ina, osati chifukwa chakuti amafuna kutero ayi koma chifukwa chakuti sangachitire mwina. Amadziŵa kuti akangokhala panyumba, ndiye kuti mabanja awo, makamaka ana awo asoŵa zinthu zambiri. Nthaŵi zambiri ndalama zimene amawalipira zimakhala zochepa poyerekeza ndi za amuna amene amagwira ntchito yofanana ndi yawo, komabe amazifuna kwambiri.
Mwachitsanzo mumzinda wa São Paulo, ku Brazil, pa anthu 100 alionse amene amagwira ntchito yolembedwa, 42 ndi azimayi. Nyuzipepala ina kumeneko inanena kuti azimayi amene ntchito yawo n’kulera ana basi “atsala pang’ono kutheratu.” M’midzi ya ku Africa, si zachilendo kuona mayi atasenza mtolo wa nkhuni komanso atabereka mwana kumbuyo.
Kuntchito Kumachuluka Zochita
Kuwonjezera pamavuto ena, kuntchitoko kungamafunike kuti azimayi azigwira ntchito yawo kwa maola ochuluka. Ndipo si zokhazo ayi. Mayi wina amene amakhala ku Greece dzina lake Maria atalembedwa ntchito, bwana wake anamuuza kuti asaine chikalata chovomereza kuti sadzakhala ndi pathupi mpaka patatha zaka zitatu. Ngati atadzakhala ndi pathupi, adzam’pepesa bwana wakeyo pom’lipira ndalama. Maria anasainadi chikalatacho. Koma patangopita mwina chaka chimodzi ndi theka basi, iye anatenga pathupi. Zitatero bwana wakeyo anam’tulutsira Maria chikalata chija, ndipo Mariayo anapita kukhoti kukasumira kampani yakeyo chifukwa chokhala ndi malamulo otere ndipo panopa akudikirira kumva zotsatira zake.
Nthaŵi zina mabwana ena amaumiriza azimayi amene ali ndi pathupi kuti akangochira basi abwerere kuntchito. Kaŵirikaŵiri, azimayiwo akabwerera kuntchitoko si kuti amawachepetserako nthaŵi yogwira ntchito ayi. Motero sawaganizirako ngakhale pang’ono kuti tsopano ali ndi ntchito inanso yosamalira mwana wawo wakhandayo. Sawalola kuwonjezera tchuti popanda kuwadula malipiro. Azimayi amatha kuvutikanso ngati kumene amakhalako n’kovuta kupeza zinthu zosiyanasiyana zofunika pamoyo wamwana ndiponso ngati kulibe chithandizo chaboma.
Komabe, azimayi ena amagwira ntchito osati chifukwa chakuti akusoŵa ndalama, koma chifukwa chofuna kukhala anthu aphindu. Sandra anachembeza kaŵiri ndipo ankabwereranso kuntchito akangochira. Iye amakumbukira zimene ankachita atazindikira kuti ali yekhayekha ndi mwana wake wakhanda ponena kuti, “nthaŵi zina ndinkangonyamuka n’kusuzumira kunja pawindo n’kumangodabwa kuti kodi kunja kulinji?” Ndipo azimayi ena amapita kuntchito pothaŵa mavuto ena a m’banja. Nyuzipepala ya ku Britain yotchedwa Daily Telegraph inati: “Makolo ena amafuna kukhala maola ambiri ali kuntchito kumene wina sawapingapinga. Zimenezi zimabweretsa mavuto ambiri, n’kuchepetsa nthaŵi imene amakhala ndi ana awo amene amasanduka amphwayi, aukali komanso oloŵerera.”
Ntchito Yotangwanitsa
Kuti zinthu ziyende bwino kuntchito ndiponso kunyumba si nkhani ya maseŵera ayi. Potchula mmene azimayi ambiri amamvera, mayi wina wa ku Netherlands anati: “Ndimangokhala wotopa nthaŵi zonse, ngakhale podzuka. Ndikafika panyumba kuchokera kuntchito, ndimakhala wotoperatu. Ana anga ayamba kale kunena kuti, ‘Nthaŵi zonse amayi amangokhala wotopa,’ ndipo mawu ameneŵa amandikhudza kwambiri. Sindikufuna kuleka kugwira ntchito, koma ndimafunanso kukhala mayi wotakasuka wotha kuchita china chilichonse. Koma sindichita zabwino zimene ndimafunazo.”
Mayiyu ali m’gulu la azimayi ambiri amene amapita kuntchito amene amaganiza kuti ‘kukhala ndi
nthaŵi yokambirana ndi ana awo’ kumathandiza akamachokachoka pakhomo, koma azimayiŵa aona kuti zimenezi n’zosathandiza. Azimayi ambiri masiku ano akuti kulimbana ndi mavuto a kuntchito kwawo kenaka n’kumalimbananso ndi maudindo a kunyumba kumawapangitsa kupanikizika kwambiri ndiponso malipiro awo amakhala ochepa kwambiri poyerekeza ndi chintchito chimene amachita.Azimayi akatalikirana ndi ana awo kwa maola ambiri, anawo amasoŵa zinthu zimene amafuna kwambiri zomwe ndi nthaŵi komanso chisamaliro cha amayi awo. Katswiri wa zamaganizo a ana wochokera ku Brazil, dzina lake Fernanda A. Lima ananena kuti palibe munthu wina aliyense amene angakwanitse kuchitira ana zimene mayi awo angawachitire. Iye anatinso: “Zaka zovuta kwambiri polera mwana wakhanda n’kungoyambira pamene mwanayo wabadwa mpaka atafika zaka ziŵiri. Nthaŵi imeneyi mwanayo amakhala adakali wamng’ono kwambiri mwakuti sangadziŵe chifukwa chimene mayi ake achokerapo.” Munthu amene amam’lera angam’chitire mwanayo zinthu zina ndi zina, koma sangachite zonse zimene mayiyo akanachita. Lima anati: “Mwanayo amadziŵa kuti sakukondedwa mofanana ndi mmene mayi ake angam’kondere.”
Mayi wina dzina lake Kathy amene ankapita kuntchito nthaŵi zonse ndipo ali ndi kamwana kakakazi anati: ‘Zinkandipatsa maganizo kwambiri chifukwa chakuti ndinkangokhala ngati ndikum’thaŵa [ndikamakam’siya kusukulu yamkaka]. Zimadandaulitsa kwambiri ukamaganiza kuti mwana wako akukula usakumuona, ndipo sizikhala bwino ukamaganizira kuti mwanayo amakonda kwambiri anthu a kusukulu yake yamkaka kuposa iweyo.’ Mkazi wina wa ku Mexico amene amagwira ntchito yolandira anthu okwera ndege anavomereza kuti: “Zimafika pena pakuti mwana wanu sakuzindikiraninso ndipo sakulemekezani makamaka chifukwa chakuti mukum’lera si inuyo. Anawo amadziŵa kuti inuyo ndiwo amayi awo, koma amakonda munthu amene amawasamalirayo.”
Komanso, azimayi amene amangokhala pakhomo poyang’anira ana awo amati amangofunika kupirira chifukwa chonyozedwa ndi anthu anzawo amene amaona kuti kugwira ntchito yolipidwa ndiko kuganiza bwino. M’madera ena, anthu saonanso kuti n’chinthu chaulemu kukhala mkazi wongokhala pakhomo, choncho azimayi amayesetsa ndithu kupeza ntchito, ngakhale atakhala kuti sakusoŵeratu pogwira.
Amangowasiya Kuti Athane Nazo Okha
Powonjezera mavuto okhala mayi palinso mfundo iyi: Mayi akagwiragwira ntchito yake n’kuŵeruka atatopa, amapita kunyumba osati kukapumula, koma kukapitiriza kugwira ntchito zimene amagwira nthaŵi zonse zapakhomo. Nthaŵi zambiri azimayi, kaya akhale olembedwa ntchito kapena ayi, amaoneka kuti ndiwo amene ali ndi udindo wosamala nyumba ndi ana.
Ngakhale kuti azimayi ochuluka amagwira ntchito kwa maola ambiri, kaŵirikaŵiri azibambo sawathandiza. Nyuzipepala ina ya ku London yotchedwa The Sunday Times inalemba kuti: “Malinga n’kufufuza kwa posachedwapa, akuti azibambo ambiri saonekaoneka pakhomo m’dziko la Britain, moti tsiku lililonse amangokhala ndi ana awo kwa kanthaŵi kochepa
kwambiri kokwana mphindi 15 basi. . . . Azibambo ambiri siziwasangalatsa zomakhala nthaŵi yaitali ali pamodzi ndi mabanja awo. . . . Koma azimayi amakhala ndi ana awo kwa mphindi 90 tsiku lililonse.”Amuna ena amadandaula kuti mkazi wawo safuna kuwapatsako ntchito zina zapakhomo chifukwa chakuti mkaziyo amafuna kuti chilichonse chichitike mmene iyeyo amachichitira. Amunawo amati: “Ukapanda kutero amati walakwitsa.” Kuti mwamuna wake amuthandize, n’zachionekere kuti mkazi wapakhomo amene watopa amayenera kusaumirira kuti
ntchito zapakhomo zizichitika mwakutimwakuti. Komanso, pankhaniyi mwamuna sayenera kupezerapo mpata wokana kugwira nawo ntchito.Kuwonjezera Mavuto Ena
Miyambo imene anthu anaizoloŵera kwambiri ingawonjezerenso mavuto ena. Ku Japan azimayi amafunika kulera ana awo mwakuti azifanana ndi anzawo a msinkhu wawo. Ngati ana ena akuphunzira kuyimba piyano kapena zolembalemba, mayinso amakakamizika kuti ana ake achite chimodzimodzi. Masukulu amachititsa makolo kuonetsetsa kuti ana awo akuphunzira nawo zinthu zimene ana ena akuphunzira. Akamachita zosiyana, ndiye kuti akhoza kuvutitsidwa ndi ana anzawo, aphunzitsi awo, makolo ena ndiponso achibale awo. Zimenezi zimachitikanso m’mayiko ena.
Kunenera malonda ndiponso kulimbikitsa anthu kugula zinthu kumapangitsa ana kuvutitsa makolo awo. M’mayiko otukuka azimayi amaona kuti ayenera kugulira ana awo zimene akufuna chifukwa chakuti amaona azimayi ena akugulira ana awo zinthuzo. Akalephera kutero, amaona ngati atsalira.
Zimene tikukambirana zokhudza azimayi amakonozi zisatiiwalitse zochita za azimayi ambirimbiri odzipereka ogwira ntchito molimbika, amene amachita khama kwambiri polera ana amene ali tsogolo la maŵa. Umenewu ndi mwayi. Baibulo limati: “Ana ndi madalitso ndiponso mphatso yochokera kwa AMBUYE.” (Salmo 127:3, Baibulo la Contemporary English Version) Mayi wina wa ana aŵiri dzina lake Miriam ananena bwino mmalo mwa azimayi onse otere pamene anati: “Ngakhale kuti mavuto alipo, koma chimwemwe chimene chimakhalapo chifukwa chokhala mayi sitingachiyerekezere ndi chilichonse. Azimayife timanyadira tikaona ana athu akutsatira bwino zimene tinawaphunzitsa n’kukhala anthu aphindu.”
Kodi n’chiyani chimene chingathandize azimayi kusangalala kwambiri ndi mphatso yawo? Nkhani yotsatira itchulapo zinthu zina zothandiza.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Nkhanizi zikukhudza azimayi okwatiwa. Mtsogolomu, Galamukani! idzakamba za mavuto a azimayi amene ali okha ndiponso osakwatiwa.
[Bokosi patsamba 6]
“Tsiku la Anakubala”
Umphaŵi wosaneneka, kusaphunzira, amuna osadziŵa kusamala akazi awo, kukonda kuzunza akazi, ndiponso mliri wa Edzi zikuvutitsa azimayi ambiri m’chigawo cha kumwera kwa Africa. Posachedwapa pa Tsiku lina la Anakubala, nyuzipepala ina ya ku South Africa yotchedwa The Citizen, inanena kuti: “Azimayi ambirimbiri amachitidwa nkhanza kapena kuzunzidwa ndi azimuna awo ndipo ena amaphedwa pa Tsiku la Anakubala.” Mavuto amtunduwu amachititsa azimayi a ku South Africa ambirimbiri kutaya ana awo akhanda chaka chilichonse. M’zaka ziŵiri zangopitazi, makanda otayidwa ndi makolo awo anawonjezeka ndi makanda 25 pa 100 alionse. Komanso chomvetsa chisoni kwambiri n’kuchuluka kwa azimayi amene amadzipha. Chaposachedwa pompa, mayi wina wochokera kudera linalake losauka kwambiri anayangata ana ake atatu n’kuima kutsogolo kwa sitima yapamtunda yomwe inkayenda, ndipo onsewo anaphedwa ndi sitimayo. Pofuna kuti apeze zinthu zofunika m’moyo, azimayi ena amangoyamba uhule ndiponso kugulitsa mankhwala ozunguza bongo kapenanso amalimbikitsa ana awo aakazi kuchita zimenezo.
Akuti ku Hong Kong, “azimayi ena achitsikana akangobereka amapha ana awo akhanda kapena kuwataya motayiramo zinyalala chifukwa chakuti sangakwanitse kuwasamala.” Nyuzipepala ina yotchedwa South China Morning Post inatchulapo kuti azimayi achitsikana ena apabanja ku Hong Kong “tsopano akusoŵa mtendere kwambiri [mwakuti] mwina akhoza kudwala maganizo kufika mpaka podzipha okha.”
[Bokosi patsamba 7]
Kukhala Mayi M’mayiko Osiyanasiyana
Vuto la Kuchepa kwa Nthaŵi
❖ Atafufuza ku Hong Kong panapezeka kuti azimayi ogwira ntchito okwana 60 pa 100 alionse samakhala ndi ana awo kwa nthaŵi yochuluka mmene amafunira. Ndipo pamasiku opita kuntchito ana 20 pa 100 alionse a zaka zosapitirira zitatu amene makolo awo amagwira ntchito amakhala kutali ndi kwawo, nthaŵi zambiri amakakhala kwa agogo awo.
❖ Azimayi a ku Mexico amatha pafupifupi zaka 13 m’moyo wawo akusamalira mwina mwana mmodzi wosakwanitsa zaka zisanu.
Amayi ndi nkhani ya kuntchito
❖ Ku Ireland azimayi okwana 60 pa 100 alionse amangokhala panyumba akusamalira ana. Ku Greece, Italy ndiponso ku Spain pafupifupi azimayi 40 pa 100 alionse nawonso amangokhala panyumba kusamalira ana.
Kuthandiza kugwira ntchito zapakhomo
❖ Ku Japan, azimayi okwana 80 pa 100 alionse ananena kuti amalakalaka munthu wina wa m’banja akanamawathandiza kugwira ntchito zapakhomo, makamaka akamadwala.
❖ Ku Netherlands azibambo amatha pafupifupi maola aŵiri tsiku lililonse ali ndi ana ndipo mphindi 42 n’zimene amagwira ntchito zapakhomo. Azimayi amakhala ndi ana pafupifupi kwa maola atatu ndipo kwa ola limodzi ndi mphindi 42, amagwira ntchito zapakhomo.
Azimayi otopa kwambiri
❖ Ku Germany pa azimayi 100 alionse pamakhala azimayi opitirira 70 otopa kwambiri. Mwina azimayi okwana 51 pa 100 alionse amadandaula kuti msana ukuwapweteka. Mwina azimayi oposa 30 pa 100 alionse amangokhala otopa ndiponso maganizo amangoti pwirikiti m’mutu mwawo. Azimayi osachepera 30 pa 100 alionse amadwala litsipa kapena mutu waching’alang’ala.
Azimayi ochitidwa nkhanza
❖ Ku Hongkong, azimayi anayi pa 100 alionse amene anafunsidwapo ananena kuti anali kuchitidwa nkhanza pamene anali oyembekezera.
❖ Magazini ya ku Germany yotchedwa Focus inasonyeza kuti pafupifupi mayi mmodzi pa azimayi asanu ndi mmodzi alionse anavomereza kuti anamenyedwapo ndi mwana wawo.
[Zithunzi patsamba 7]
Kukhala mayi nthaŵi zina n’kosautsa zedi, chifukwa amayi ambiri amayesetsa kuti ayendetse bwino ntchito komanso banja panthaŵi yomweyomweyo