Kodi Amuna Amamenyeranji Akazi?
Kodi Amuna Amamenyeranji Akazi?
AKATSWIRI ena amati akazi amene amaphedwa ndi amuna awo n’ngochuluka kuposa amene amaphedwa ndi anthu ena onse. Poyesa kuthetsa vuto la kumenya akazi, akatswiri ambiri akhala akufufuza nkhaniyi. Kodi ndi mwamuna wotani amene amamenya mkazi wake? Kodi ubwana wake unali wotani? Kodi ali pachibwenzi analinso munthu wovuta? Kodi mwamuna womenyayo amatani anthu ena akamam’thandiza maganizo?
Chinthu chimodzi chimene akatswiriŵa atulukira n’chakuti si kuti amuna omenya akazi awo n’ngofanana zochitika. Pali ena amene amamenya akazi awo mwakamodzikamodzi. Sagwiritsa ntchito zida ndipo alibe chizoloŵezi chomenya akazi awo. Amuna otereŵa sanyanyuka mtima nthaŵi zonse ndipo amaoneka kuti chilipo chinthu china chimene chimawachititsa kutero. Ndiye pali amuna ena amene anazoloŵera kumenya akazi awo. Amawamenya nthaŵi zonse ndipo siziwakhudza n’komwe akatero.
Koma ngakhale kuti pali amuna omenya akazi awo mosiyanasiyana si ndiye kuti pali kumenya kwabwinoko. Inde, khalidwe lililonse lomenya mkazi lingathe kum’vulaza mwinanso kumupha ndithu. Motero ngakhale kuti wina amamenya mkazi wake mwa apo ndi apo kapena amangom’menya pang’ono poyerekezera ndi ena si ndiye kuti alibe mlandu. Kunena zoona palibe kumenya mkazi “kovomerezeka.” Koma kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse mwamuna kumenya mkazi amene iye yemwe analumbira kuti adzam’konda kwa moyo wake wonse?
Kutsanzira Makolo
N’zosadabwitsa kuti amuna ambiri omenya akazi awo nawonso anakulira m’mabanja otero. “Amuna ambiri omenya akazi awo anakulira m’mabanja okhalira ‘nkhondo,’” analemba choncho Michael Groetsch, amene kwa zaka makumi aŵiri wakhala akufufuza nkhani ya kumenya akazi. “Pamene anali makanda ndiponso ana, amuna ameneŵa ankakhala m’makomo mmene kupweteketsana mitima ndiponso kumenyana zinkachitika ‘monga khalidwe la nthaŵi zonse.’” Katswiri wina anati, mwamuna amene anakula akuona khalidwe lotere “angatengere adakali mwana khalidwe la abambo ake loona akazi ngati achabechabe. Mnyamatayo amaphunzira kuti nthaŵi zonse mwamuna ayenera kulamulira akazi ndipo kuti njira yake ndiyo kuwaopseza, kuwapweteketsa mtima, ndi kuwanyoza. Komanso
amaphunzira kuti njira yabwino yosangalatsira abambo ake ndiyo kutsanzira zimene iwo amachita.”Baibulo limalongosola momveka bwino kuti khalidwe la kholo lingathe kukhudzanso mwana kwambiri, m’njira yabwino kapena yoipa. (Miyambo 22:6; Akolose 3:21) N’zoona kuti ngakhale mwamuna anakulira m’banja lomenyana si ndiye kuti m’pomveka akamamenya mkazi wake, koma zimangopereka umboni wakuti nkhanza zakezo anazitengera m’banja la kwawo.
Kuvuta Chifukwa cha Chikhalidwe
M’madera ena amati kumenya mkazi si nkhani ayi, amangoti ndiko kukhala. “M’madera ambiri anthu amakhulupirira kuti mwamuna ali ndi ufulu womenya kapena kuopseza mkazi wake,” linatero lipoti la bungwe la United Nations.
Ngakhale m’madera amene khalidweli n’losaloleka, anthu ambiri amamenya akazi awo. Amuna ena amawaganizira zoopsa kwambiri akazi awo. Malingana ndi nyuzipepala ya ku South Africa ya Weekly Mail and Guardian, atafufuza ku Cape Peninsula anapeza kuti amuna ambiri amene ankati savuta akazi awo ankaganiza kuti kumenya mkazi si nkhani ndipo ankati ukamenya mkazi si ndiye kuti ukumuvuta.
Zikuoneka kuti nthaŵi zambiri anthu amayamba kuganiza molakwa chonchi adakali ana. Mwachitsanzo ku Britain, atafufuza anapeza kuti anyamata 75 pa 100 alionse a zaka 11 ndi 12 amaona kuti mwamuna ali ndi ufulu womenya mkazi wake ngati atamuyamba.
Palibe Chifukwa Chokwanira Chomenyera Mkazi
Mfundo zili pamwambazi zingathandize kudziŵa chifukwa chimene amuna amamenyera Aefeso 5:28, 29.
akazi, koma si zikutanthauza kuti ayenera kutero. Kunena mosapita m’mbali, kumenya mkazi ndi tchimo lalikulu kwambiri pamaso pa Mulungu. M’Mawu ake, Baibulo, timaŵerenga kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia.”—Baibulo linalonjeza kale kuti mu “masiku otsiriza” a nthaŵi ino, anthu ambiri adzakhala “ovutitsa,” “opanda chikondi chachibadwa,” ndiponso “aukali.” (2 Timoteo 3:1-3; The New English Bible) Kuchuluka kwa amuna ovutitsa akazi awo n’chizindikiro china chongosonyeza kuti tikukhala m’nthaŵi yeniyeni yotchulidwa mu ulosiwu. Koma kodi akazi amene amamenyedwa ndi amuna awo n’kuwathandiza bwanji? Kodi zingatheke n’komwe kuti amuna omenya akazi awo asinthe khalidweli?
[Mawu Otsindika patsamba 5]
“Mwamuna womenya mkazi wake ndi wolakwa mofanana ndi munthu womenya munthu amene sakum’dziŵa.”—Linatero buku lakuti, When Men Batter Women
[Bokosi patsamba 6]
Kudzitukumula Chifukwa Chokhala Mwamuna Ndi Vuto la Padziko Lonse
Padziko lonse, pali anthu ena amene ali ndi kamtima kodzitukumula poti ndi amuna ndipo motero amavutitsa akazi awo. Lipoti lotsatirali likusonyeza zimenezi.
Egypt: Atafufuza kwa miyezi itatu ku Alexandria anapeza kuti akazi ambiri amavulala makamaka chifukwa chomenyedwa ndi amuna awo. Motero kumeneko akazi 100 alionse amene amapita kuchipatala cha anthu ovulala, opitirira 27 amakhala atamenyedwa. Inatero ndemanga ina yachidule yachisanu pa msonkhano wa Fourth World Conference on Women.
Thailand: M’dera lalikulu kwambiri la kunja kwa mzinda wa Bangkok, theka la akazi okwatiwa amamenyedwa kaŵirikaŵiri. Linatero bungwe la Pacific Institute for Women’s Health.
Hong Kong: “Akazi amene akuti akhala akumenyedwa ndi amuna awo awonjezereka modabwitsa n’kufika 40 pa 100 alionse m’chaka chathachi,” inatero nyuzipepala ya South China Morning Post, ya pa July 21, 2000.
Japan: Akazi ofunafuna kokhala pothaŵa kuzunzidwa analipo 4,843 mu 1995 koma anachuluka n’kufika pa 6,340 mu 1998. “Pafupifupi mkazi mmodzi pa akazi atatu alionse pa gululi anali kufunafuna kokhala chifukwa chomenyedwa ndi mwamuna wake,” inatero nyuzipepala ya Japan Times, ya pa September 10, 2000.
Britain: “M’dziko lonse la Britain pa masekondi sikisi alionse kunyumba kwinakwake munthu wina amakhala akugwiriridwa, kumenyedwa kapena kubayidwa.” Malingana ndi lipoti la apolisi ofufuza milandu mwachinsinsi a ku Britain otchedwa Scotland Yard, akuti “apolisi amalandira matelefoni 1,300 kuchokera kwa anthu ovutitsidwa panyumba tsiku lililonse, kutanthauza kuti pachaka apolisiŵa amalandira matelefoni oposa 570,000. Anthu 81 pa 100 alionse ochitidwa zimenezi amakhala akazi ovutitsidwa ndi amuna,” inatero nyuzipepala yotchedwa The Times, ya pa October 25, 2000.
Peru: Milandu 70 mwa milandu 100 iliyonse imene imapita ku polisi n’njokhudza akazi omenyedwa ndi amuna awo. Linatero bungwe la Pacific Institute for Women’s Health.
Russia: “M’chaka chimodzi chokha, akazi 14,500 a ku Russia anaphedwa ndi amuna awo, ndipo enanso 56,400 analemazidwa kapena kuvulazidwa kwambiri pomenyedwa ku nyumba zawo,” inatero nyuzipepala ya The Guardian.
China: “Ndi vuto la posachedwa. Likumka lichuluka, makamaka m’madera a m’tauni,” anatero pulofesa Chen Yiyun, mkulu wa bungwe la Jinglun Family Center. “Masiku ano anthu saopa kuti oyandikana nawo angadziŵe akamamenyana m’nyumba mwawo, inatero nyuzipepala ya Guardian.
Nicaragua: “Ku Nicaragua khalidwe lomenya akazi likuchuluka. Ofufuza ena anati chaka chatha chokha akazi oposa theka la akazi onse a ku Nicaragua anavutitsidwapo ndi amuna awo.” Izi zinali nkhani zoulutsidwa pa wailesi ya BBC.
[Bokosi patsamba 7]
Zimene Zingasonyeze Kuti Mwina Mwamuna Ndi Womenya
Ofufuza amene anatsogoleredwa ndi Richard J. Gelles wa pa yunivesite yotchedwa Rhode Island, ku United States, anapeza kuti izi ndizo zinthu zimene zingasonyeze kuti mwina mwamuna ali ndi khalidwe lomenya ndiponso lozunguza mkazi m’banja:
1. Ngati kale mwamunayo anavutitsapo mkazi wake.
2. Ngati sali pantchito.
3. Ngati amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ngakhale kamodzi kokha pa chaka.
4. Ngati kunyumba kwawo ankaona bambo ake akumenya amayi ake.
5. Ngati anthuwo si okwatirana; anangoloŵana.
6. Akamalandira ndalama zochepa ngati ali pa ntchito.
7. Ngati sanaphunzire mokwanira.
8. Ngati ali ndi zaka zoyambira 18 mpaka 30.
9. Ngati kholo lake limodzi kapena onse ankakonda kumenya ana kunyumba kwawo.
10. Ngati ali osauka kwambiri.
11. Ngati mwamuna ndi mkaziyo ali osiyana chikhalidwe.
[Chithunzi patsamba 7]
Kumenyana pa khomo kungawononge kwambiri khalidwe la ana